< תהילים 76 >

למנצח בנגינת מזמור לאסף שיר נודע ביהודה אלהים בישראל גדול שמו׃ 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo la Asafu. Mulungu amadziwika mu Yuda; dzina lake ndi lotchuka mu Israeli.
ויהי בשלם סכו ומעונתו בציון׃ 2
Tenti yake ili mu Salemu, malo ake okhalamo mu Ziyoni.
שמה שבר רשפי קשת מגן וחרב ומלחמה סלה׃ 3
Kumeneko Iye anathyola mivi yowuluka, zishango ndi malupanga, zida zankhondo. (Sela)
נאור אתה אדיר מהררי טרף׃ 4
Wolemekezeka ndinu, wamphamvu kuposa mapiri amene ali ndi nyama zambiri.
אשתוללו אבירי לב נמו שנתם ולא מצאו כל אנשי חיל ידיהם׃ 5
Anthu owuma mtima amagona atalandidwa chuma, Iwowo amagona tulo tawo totsiriza; palibe mmodzi wamphamvu amene angatukule manja ake.
מגערתך אלהי יעקב נרדם ורכב וסוס׃ 6
Pa kudzudzula kwanu, Inu Mulungu wa Yakobo, kavalo pamodzi ndi galeta zimakhala chete zitagona pansi.
אתה נורא אתה ומי יעמד לפניך מאז אפך׃ 7
Inu nokha ndiye muyenera kuopedwa. Angathe kuyima pamaso panu ndani mukakwiya?
משמים השמעת דין ארץ יראה ושקטה׃ 8
Kuchokera kumwamba Inu munalengeza chiweruzo, ndipo dziko linaopa ndi kukhala chete,
בקום למשפט אלהים להושיע כל ענוי ארץ סלה׃ 9
pamene Inu Mulungu munadzuka kuti muweruze, kupulumutsa onse osautsidwa mʼdziko. (Sela)
כי חמת אדם תודך שארית חמת תחגר׃ 10
Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu.
נדרו ושלמו ליהוה אלהיכם כל סביביו יובילו שי למורא׃ 11
Chitani malumbiro kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse; anthu onse omuzungulira abweretse mphatso kwa Iye amene ayenera kuopedwa.
יבצר רוח נגידים נורא למלכי ארץ׃ 12
Iye amaswa mzimu wa olamulira; amaopedwa ndi mafumu a dziko lapansi.

< תהילים 76 >