< תהילים 74 >
משכיל לאסף למה אלהים זנחת לנצח יעשן אפך בצאן מרעיתך׃ | 1 |
Ndakatulo ya Asafu. Nʼchifukwa chiyani mwatitaya ife kwamuyaya, Inu Mulungu? Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutira pa nkhosa za busa lanu?
זכר עדתך קנית קדם גאלת שבט נחלתך הר ציון זה שכנת בו׃ | 2 |
Kumbukirani anthu amene munawagula kalekale, fuko la cholowa chanu, limene Inu munaliwombola, phiri la Ziyoni, kumene inuyo mumakhala.
הרימה פעמיך למשאות נצח כל הרע אויב בקדש׃ | 3 |
Tembenuzani mapazi kuloza ku mabwinja awa amuyaya chiwonongeko ichi chonse mdani wabweretsa pa malo opatulika.
שאגו צרריך בקרב מועדך שמו אותתם אתות׃ | 4 |
Adani anu anabangula pa malo pamene Inu munkakumana nafe; anayimika mbendera zawo monga zizindikiro zachigonjetso.
יודע כמביא למעלה בסבך עץ קרדמות׃ | 5 |
Iwo anachita ngati anthu oti anyamula mbendera zawo kuti adule mitengo mʼnkhalango.
ועת פתוחיה יחד בכשיל וכילפת יהלמון׃ | 6 |
Kenaka anaphwanya ndi nkhwangwa ndi akasemasema awo zonse zimene tinapachika.
שלחו באש מקדשך לארץ חללו משכן שמך׃ | 7 |
Iwo anatentha malo anu opatulika mpaka kuwagwetsa pansi; anadetsa malo okhalamo dzina lanu.
אמרו בלבם נינם יחד שרפו כל מועדי אל בארץ׃ | 8 |
Ndipo anati mʼmitima yawo, “Tawatha kwathunthu.” Anatentha malo aliwonse amene Mulungu amapembedzedwerako mʼdzikomo.
אותתינו לא ראינו אין עוד נביא ולא אתנו ידע עד מה׃ | 9 |
Ife sitinapatsidwe chizindikiro chodabwitsa; palibe aneneri amene atsala ndipo palibe aliyense wa ife akudziwa kuti izi zidzatenga nthawi yayitali bwanji.
עד מתי אלהים יחרף צר ינאץ אויב שמך לנצח׃ | 10 |
Kodi mpaka liti, mdani adzanyoze Inu Mulungu? Kodi amaliwongowa adzapeputsa dzina lanu kwamuyaya?
למה תשיב ידך וימינך מקרב חוקך כלה׃ | 11 |
Chifukwa chiyani mukubweza dzanja lanu lamanja? Litulutseni kuchoka pachifuwa chanu ndipo muwawononge!
ואלהים מלכי מקדם פעל ישועות בקרב הארץ׃ | 12 |
Koma Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga kuyambira kalekale; Mumabweretsa chipulumutso pa dziko lapansi.
אתה פוררת בעזך ים שברת ראשי תנינים על המים׃ | 13 |
Ndinu amene munagawa nyanja ndi mphamvu yanu; munathyola mitu ya zirombo za mʼmadzi.
אתה רצצת ראשי לויתן תתננו מאכל לעם לציים׃ | 14 |
Ndinu amene munaphwanya mitu ya Leviyatani ndi kuyipereka ngati chakudya cha zirombo za mʼchipululu.
אתה בקעת מעין ונחל אתה הובשת נהרות איתן׃ | 15 |
Ndinu amene munatsekula akasupe ndi mitsinje, munawumitsa mitsinje imene siphwa nthawi zonse.
לך יום אף לך לילה אתה הכינות מאור ושמש׃ | 16 |
Masana ndi anu ndipo usiku ndi wanunso; Inuyo munakhazikitsa dzuwa ndi mwezi.
אתה הצבת כל גבולות ארץ קיץ וחרף אתה יצרתם׃ | 17 |
Ndinu amene munakhazikitsa malire onse a dziko lapansi; munakhazikitsa chilimwe ndi dzinja.
זכר זאת אויב חרף יהוה ועם נבל נאצו שמך׃ | 18 |
Kumbukirani momwe mdani wakunyozerani Inu Yehova, momwe anthu opusa apeputsira dzina lanu.
אל תתן לחית נפש תורך חית ענייך אל תשכח לנצח׃ | 19 |
Musapereke moyo wa nkhunda yanu ku zirombo zakuthengo; nthawi zonse musayiwale miyoyo ya anthu anu osautsidwa.
הבט לברית כי מלאו מחשכי ארץ נאות חמס׃ | 20 |
Mukumbukire pangano lanu, pakuti malo obisika a mʼdziko asanduka mochitira zachiwawa zochuluka.
אל ישב דך נכלם עני ואביון יהללו שמך׃ | 21 |
Musalole kuti osautsidwa abwerere mwamanyazi; osauka ndi osowa atamande dzina lanu.
קומה אלהים ריבה ריבך זכר חרפתך מני נבל כל היום׃ | 22 |
Dzukani Inu Mulungu ndipo dzitetezeni pa mlandu; kumbukirani momwe opusa akukunyozerani tsiku lonse.
אל תשכח קול צרריך שאון קמיך עלה תמיד׃ | 23 |
Musalekerere phokoso la otsutsana nanu, chiwawa cha adani anu, chimene chikumveka kosalekeza.