< תהילים 71 >

בך יהוה חסיתי אל אבושה לעולם׃ 1
Mwa Inu Yehova ine ndathawiramo; musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
בצדקתך תצילני ותפלטני הטה אלי אזנך והושיעני׃ 2
Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu, mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa.
היה לי לצור מעון לבוא תמיד צוית להושיעני כי סלעי ומצודתי אתה׃ 3
Mukhale thanthwe langa lothawirapo, kumene ine nditha kupita nthawi zonse; lamulani kuti ndipulumuke, pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
אלהי פלטני מיד רשע מכף מעול וחומץ׃ 4
Landitseni Inu Mulungu wanga, kuchoka mʼdzanja la oyipa, kuchoka mʼdzanja la oyipa ndi anthu ankhanza.
כי אתה תקותי אדני יהוה מבטחי מנעורי׃ 5
Pakuti Inu mwakhala chiyembekezo changa, Inu Ambuye Wamphamvuzonse, chilimbikitso changa kuyambira ndili mwana.
עליך נסמכתי מבטן ממעי אמי אתה גוזי בך תהלתי תמיד׃ 6
Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu; Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga, ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.
כמופת הייתי לרבים ואתה מחסי עז׃ 7
Ine ndakhala chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri koma Inu ndinu wonditchinjiriza wamphamvu.
ימלא פי תהלתך כל היום תפארתך׃ 8
Pakamwa panga padzaza ndi matamando anu, kulengeza ulemerero wanu tsiku lonse.
אל תשליכני לעת זקנה ככלות כחי אל תעזבני׃ 9
Musanditaye pamene ndakalamba; musandisiye pamene mphamvu zanga zatha.
כי אמרו אויבי לי ושמרי נפשי נועצו יחדו׃ 10
Pakuti adani anga ayankhula motsutsana nane; iwo amene amadikira kuti andiphe amapangana pamodzi.
לאמר אלהים עזבו רדפו ותפשוהו כי אין מציל׃ 11
Iwo amati, “Mulungu wamusiya; mutsatireni ndi kumugwira, pakuti palibe amene adzamupulumutse.”
אלהים אל תרחק ממני אלהי לעזרתי חישה׃ 12
Musakhale kutali ndi ine Inu Mulungu, bwerani msanga, Inu Mulungu wanga; thandizeni.
יבשו יכלו שטני נפשי יעטו חרפה וכלמה מבקשי רעתי׃ 13
Ondineneza anga awonongeke mwa manyazi, iwo amene akufuna kundipweteka avale chitonzo ndi manyazi.
ואני תמיד איחל והוספתי על כל תהלתך׃ 14
Koma ine ndidzakhala ndi chiyembekezo mwa Inu nthawi zonse, ndidzakutamandani mowirikizawirikiza.
פי יספר צדקתך כל היום תשועתך כי לא ידעתי ספרות׃ 15
Pakamwa panga padzafotokoza za chilungamo chanu, za chipulumutso chanu tsiku lonse, ngakhale sindikudziwa muyeso wake.
אבוא בגברות אדני יהוה אזכיר צדקתך לבדך׃ 16
Ndidzabwera ndi kulengeza za machitidwe amphamvu zanu Inu Ambuye Wamphamvuzonse. Ndidzalengeza chilungamo chanu, chanu chokha.
אלהים למדתני מנעורי ועד הנה אגיד נפלאותיך׃ 17
Kuyambira ubwana wanga, Inu Mulungu mwakhala mukundiphunzitsa, ndipo mpaka lero ine ndikulengeza za ntchito zanu zodabwitsa
וגם עד זקנה ושיבה אלהים אל תעזבני עד אגיד זרועך לדור לכל יבוא גבורתך׃ 18
Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu musanditaye Inu Mulungu, mpaka nditalengeza mphamvu zanu kwa mibado yonse yakutsogolo.
וצדקתך אלהים עד מרום אשר עשית גדלות אלהים מי כמוך׃ 19
Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu zimafika mpaka kumwambamwamba. Ndani wofanana nanu Inu Mulungu, amene mwachita zazikulu?
אשר הראיתנו צרות רבות ורעות תשוב תחיינו ומתהמות הארץ תשוב תעלני׃ 20
Ngakhale mwandionetsa mavuto ambiri owawa, mudzabwezeretsanso moyo wanga; kuchokera kunsi kwa dziko lapansi, mudzandiukitsanso.
תרב גדלתי ותסב תנחמני׃ 21
Inu mudzachulukitsa ulemu wanga ndi kunditonthozanso.
גם אני אודך בכלי נבל אמתך אלהי אזמרה לך בכנור קדוש ישראל׃ 22
Ndidzakutamandani ndi zeze chifukwa cha kukhulupirika kwanu Mulungu, ndidzayimba matamando kwa Inu ndi pangwe, Inu Woyera wa Israeli.
תרננה שפתי כי אזמרה לך ונפשי אשר פדית׃ 23
Milomo yanga idzafuwula ndi chimwemwe pamene ndidzayimba matamando kwa Inu amene mwandiwombola.
גם לשוני כל היום תהגה צדקתך כי בשו כי חפרו מבקשי רעתי׃ 24
Lilime langa lidzafotokoza za ntchito zanu zachilungamo tsiku lonse, pakuti iwo amene amafuna kundipweteka achititsidwa manyazi ndi kusokonezedwa.

< תהילים 71 >