< תהילים 7 >
שגיון לדוד אשר שר ליהוה על דברי כוש בן ימיני יהוה אלהי בך חסיתי הושיעני מכל רדפי והצילני׃ | 1 |
Sigioni wa Davide, amene anayimbira Yehova zokhudza Kusi, wa fuko la Benjamini. Inu Yehova Mulungu wanga, Ine ndikuthawira kwa Inu; pulumutseni ndi kundilanditsa kwa onse amene akundithamangitsa,
פן יטרף כאריה נפשי פרק ואין מציל׃ | 2 |
mwina angandikadzule ngati mkango, ndi kundingʼamba popanda wondipulumutsa.
יהוה אלהי אם עשיתי זאת אם יש עול בכפי׃ | 3 |
Inu Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita izi ndipo ndapezeka wolakwa,
אם גמלתי שולמי רע ואחלצה צוררי ריקם׃ | 4 |
ngati ndachita zoyipa kwa iye amene ndili naye pa mtendere, kapena popanda chifukwa ndalanda mdani wanga,
ירדף אויב נפשי וישג וירמס לארץ חיי וכבודי לעפר ישכן סלה׃ | 5 |
pamenepo lolani adani anga andithamangitse ndi kundipitirira, lolani kuti moyo wanga aupondereze pansi ndipo mundigoneke pa fumbi. (Sela)
קומה יהוה באפך הנשא בעברות צוררי ועורה אלי משפט צוית׃ | 6 |
Nyamukani Yehova, mu mkwiyo wanu; nyamukani kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga. Dzukani Mulungu wanga, lamulirani chilungamo chanu.
ועדת לאמים תסובבך ועליה למרום שובה׃ | 7 |
Lolani gulu la anthu a mitundu ina lisonkhane mokuzungulirani. Alamulireni muli kumwambako;
יהוה ידין עמים שפטני יהוה כצדקי וכתמי עלי׃ | 8 |
Yehova aweruzeni anthu a mitundu inayo. Ndiweruzeni Yehova, monga mwa chilungamo changa, monga mwa moyo wanga wangwiro, Inu Wammwambamwamba.
יגמר נא רע רשעים ותכונן צדיק ובחן לבות וכליות אלהים צדיק׃ | 9 |
Inu Mulungu wolungama, amene mumasanthula maganizo ndi mitima, thetsani chiwawa cha anthu oyipa ndipo wolungama akhale motetezedwa.
מגני על אלהים מושיע ישרי לב׃ | 10 |
Chishango changa ndi Mulungu Wammwambamwamba, amene amapulumutsa olungama mtima.
אלהים שופט צדיק ואל זעם בכל יום׃ | 11 |
Mulungu amaweruza molungama, Mulungu amene amaonetsa ukali wake tsiku ndi tsiku.
אם לא ישוב חרבו ילטוש קשתו דרך ויכוננה׃ | 12 |
Ngati munthu satembenuka, Mulungu adzanola lupanga lake, Iye adzawerama ndi kukoka uta.
ולו הכין כלי מות חציו לדלקים יפעל׃ | 13 |
Mulungu wakonza zida zake zoopsa; Iye wakonzekera mivi yake yoyaka moto.
הנה יחבל און והרה עמל וילד שקר׃ | 14 |
Taonani, munthu woyipa amalingalira zoyipa zokhazokha nthawi zonse. Zochita zake ndi zosokoneza ndi zovutitsa anthu ena.
בור כרה ויחפרהו ויפל בשחת יפעל׃ | 15 |
Iye amene akumba dzenje ndi kulizamitsa amagwera mʼdzenje limene wakumbalo.
ישוב עמלו בראשו ועל קדקדו חמסו ירד׃ | 16 |
Mavuto amene amayambitsa amamubwerera mwini; chiwawa chake chimatsikira pa mutu wake womwe.
אודה יהוה כצדקו ואזמרה שם יהוה עליון׃ | 17 |
Ine ndidzayamika Yehova chifukwa cha chilungamo chake; ndipo ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina la Yehova Wammwambamwamba.