< תהילים 62 >

למנצח על ידותון מזמור לדוד אך אל אלהים דומיה נפשי ממנו ישועתי׃ 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kutsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Davide. Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha; chipulumutso changa chimachokera kwa Iye.
אך הוא צורי וישועתי משגבי לא אמוט רבה׃ 2
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.
עד אנה תהותתו על איש תרצחו כלכם כקיר נטוי גדר הדחויה׃ 3
Kodi nonsenu mudzalimbana naye munthu mpaka liti? Kodi mudzamugwetsa pansi ngati khoma losalimba, ngati mpanda wogwedezeka?
אך משאתו יעצו להדיח ירצו כזב בפיו יברכו ובקרבם יקללו סלה׃ 4
Iwo akufunitsitsa kumugwetsa kuti achoke pa malo ake apamwamba. Iwo amakondweretsedwa ndi mabodza. Ndi pakamwa pawo amadalitsa koma mʼmitima yawo amatemberera.
אך לאלהים דומי נפשי כי ממנו תקותי׃ 5
Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga; chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.
אך הוא צורי וישועתי משגבי לא אמוט׃ 6
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka.
על אלהים ישעי וכבודי צור עזי מחסי באלהים׃ 7
Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu: Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga.
בטחו בו בכל עת עם שפכו לפניו לבבכם אלהים מחסה לנו סלה׃ 8
Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu; khuthulani mitima yanu kwa Iye, pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu. (Sela)
אך הבל בני אדם כזב בני איש במאזנים לעלות המה מהבל יחד׃ 9
Anthu wamba ndi mpweya chabe; anthu apamwamba ndi bodza chabe; ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe; iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe
אל תבטחו בעשק ובגזל אל תהבלו חיל כי ינוב אל תשיתו לב׃ 10
Musadalire kulanda mwachinyengo kapena katundu wobedwa; ngakhale chuma chanu chichuluke, musayike mtima wanu pa icho.
אחת דבר אלהים שתים זו שמעתי כי עז לאלהים׃ 11
Mulungu wayankhula kamodzi, ine ndamvapo zinthu ziwiri; choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu,
ולך אדני חסד כי אתה תשלם לאיש כמעשהו׃ 12
komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika. Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthu molingana ndi ntchito zake.

< תהילים 62 >