< תהילים 50 >

מזמור לאסף אל אלהים יהוה דבר ויקרא ארץ ממזרח שמש עד מבאו׃ 1
Salimo la Asafu. Wamphamvuyo, Yehova Mulungu, akuyankhula ndi kuyitanitsa dziko lapansi kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.
מציון מכלל יפי אלהים הופיע׃ 2
Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiri Mulungu akuwala.
יבא אלהינו ואל יחרש אש לפניו תאכל וסביביו נשערה מאד׃ 3
Mulungu wathu akubwera ndipo sadzakhala chete; moto ukunyeketsa patsogolo pake, ndipo pomuzungulira pali mphepo yamkuntho
יקרא אל השמים מעל ואל הארץ לדין עמו׃ 4
Iye akuyitanitsa zamumlengalenga ndi za pa dziko lapansi kuti aweruze anthu ake.
אספו לי חסידי כרתי בריתי עלי זבח׃ 5
Mundisonkhanitsire okhulupirika anga, amene anachita pangano ndi ine pochita nsembe.
ויגידו שמים צדקו כי אלהים שפט הוא סלה׃ 6
Ndipo mayiko akumwamba akulengeza chilungamo chake, pakuti Mulungu mwini ndi woweruza.
שמעה עמי ואדברה ישראל ואעידה בך אלהים אלהיך אנכי׃ 7
Imvani inu anthu anga, ndipo Ine ndidzayankhula, iwe Israeli, ndipo Ine ndidzayankhula mokutsutsa; ndine Mulungu, Mulungu wako.
לא על זבחיך אוכיחך ועולתיך לנגדי תמיד׃ 8
Sindikudzudzula chifukwa cha nsembe zako, kapena nsembe zako zopsereza zimene zili pamaso panga nthawi zonse.
לא אקח מביתך פר ממכלאתיך עתודים׃ 9
Ine sindikufuna ngʼombe yayimuna kuchokera mʼkhola lako kapena mbuzi za mʼkhola lako,
כי לי כל חיתו יער בהמות בהררי אלף׃ 10
pakuti nyama iliyonse yakunkhalango ndi yanga ndiponso ngʼombe za ku mapiri ochuluka.
ידעתי כל עוף הרים וזיז שדי עמדי׃ 11
Ine ndimadziwa mbalame iliyonse mʼmapiri ndiponso zolengedwa zonse zakutchire ndi zanga.
אם ארעב לא אמר לך כי לי תבל ומלאה׃ 12
Ndikanakhala ndi njala sindikanakuwuzani, pakuti dziko lonse ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndi zanga.
האוכל בשר אבירים ודם עתודים אשתה׃ 13
Kodi ndimadya nyama ya ngʼombe zazimuna kapena kumwa magazi a mbuzi?
זבח לאלהים תודה ושלם לעליון נדריך׃ 14
“Pereka nsembe zachiyamiko kwa Mulungu, kwaniritsa malonjezo ako kwa Wammwambamwamba.
וקראני ביום צרה אחלצך ותכבדני׃ 15
Ndipo undiyitane pa tsiku lako la masautso; Ine ndidzakulanditsa, ndipo udzandilemekeza.”
ולרשע אמר אלהים מה לך לספר חקי ותשא בריתי עלי פיך׃ 16
Koma kwa woyipa, Mulungu akuti, “Kodi uli ndi mphamvu yanji kuti uzinena malamulo anga kapena kutenga pangano langa pa milomo yako?
ואתה שנאת מוסר ותשלך דברי אחריך׃ 17
Iwe umadana ndi malangizo anga ndipo umaponyera kumbuyo kwako mawu anga.
אם ראית גנב ותרץ עמו ועם מנאפים חלקך׃ 18
Ukaona wakuba umamutsatira, umachita maere ako pamodzi ndi achigololo
פיך שלחת ברעה ולשונך תצמיד מרמה׃ 19
Umagwiritsa ntchito pakamwa pako pa zinthu zoyipa ndipo umakonza lilime lako kuchita chinyengo.
תשב באחיך תדבר בבן אמך תתן דפי׃ 20
Nthawi zonse umayankhula motsutsana ndi mʼbale wako ndipo umasinjirira mwana wa amayi ako enieni.
אלה עשית והחרשתי דמית היות אהיה כמוך אוכיחך ואערכה לעיניך׃ 21
Wachita zimenezi ndipo Ine ndinali chete; umaganiza kuti ndine wofanana nawe koma ndidzakudzudzula ndipo ndidzakutsutsa pamaso pako.
בינו נא זאת שכחי אלוה פן אטרף ואין מציל׃ 22
“Ganizira izi, iwe amene umayiwala Mulungu kuti ndingakukadzule popanda wokupulumutsa:
זבח תודה יכבדנני ושם דרך אראנו בישע אלהים׃ 23
Iye amene amapereka nsembe yamayamiko amandilemekeza, ndipo amakonza njira zake kuti ndimuonetse chipulumutso cha Mulungu.”

< תהילים 50 >