< תהילים 48 >

שיר מזמור לבני קרח גדול יהוה ומהלל מאד בעיר אלהינו הר קדשו׃ 1
Nyimbo. Salimo la ana a Kora. Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
יפה נוף משוש כל הארץ הר ציון ירכתי צפון קרית מלך רב׃ 2
Lokongola mu utali mwake, chimwemwe cha dziko lonse lapansi. Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni, mzinda wa Mfumu yayikulu.
אלהים בארמנותיה נודע למשגב׃ 3
Mulungu ali mu malinga ake; Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.
כי הנה המלכים נועדו עברו יחדו׃ 4
Pamene mafumu anasonkhana pamodzi, pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
המה ראו כן תמהו נבהלו נחפזו׃ 5
iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri; anathawa ndi mantha aakulu.
רעדה אחזתם שם חיל כיולדה׃ 6
Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera, ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
ברוח קדים תשבר אניות תרשיש׃ 7
Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.
כאשר שמענו כן ראינו בעיר יהוה צבאות בעיר אלהינו אלהים יכוננה עד עולם סלה׃ 8
Monga momwe tinamvera, kotero ife tinaona mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse, mu mzinda wa Mulungu wathu. Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.
דמינו אלהים חסדך בקרב היכלך׃ 9
Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu, ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
כשמך אלהים כן תהלתך על קצוי ארץ צדק מלאה ימינך׃ 10
Monga dzina lanu, Inu Mulungu, matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
ישמח הר ציון תגלנה בנות יהודה למען משפטיך׃ 11
Phiri la Ziyoni likukondwera, midzi ya Yuda ndi yosangalala chifukwa cha maweruzo anu.
סבו ציון והקיפוה ספרו מגדליה׃ 12
Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo, werengani nsanja zake.
שיתו לבכם לחילה פסגו ארמנותיה למען תספרו לדור אחרון׃ 13
Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake, penyetsetsani malinga ake, kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
כי זה אלהים אלהינו עולם ועד הוא ינהגנו על מות׃ 14
Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha; Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.

< תהילים 48 >