< תהילים 43 >
שפטני אלהים וריבה ריבי מגוי לא חסיד מאיש מרמה ועולה תפלטני׃ | 1 |
Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu; ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza; mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa.
כי אתה אלהי מעוזי למה זנחתני למה קדר אתהלך בלחץ אויב׃ | 2 |
Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga. Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine? Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, woponderezedwa ndi mdani?
שלח אורך ואמתך המה ינחוני יביאוני אל הר קדשך ואל משכנותיך׃ | 3 |
Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanu kuti zinditsogolere; mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera, kumalo kumene inu mumakhala.
ואבואה אל מזבח אלהים אל אל שמחת גילי ואודך בכנור אלהים אלהי׃ | 4 |
Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu, kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa. Ndidzakutamandani ndi zeze, Inu Mulungu wanga.
מה תשתוחחי נפשי ומה תהמי עלי הוחילי לאלהים כי עוד אודנו ישועת פני ואלהי׃ | 5 |
Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni iwe moyo wanga? Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandabe Iye, Mpulumutsi wanga ndi Mulungu wanga.