< תהילים 33 >
רננו צדיקים ביהוה לישרים נאוה תהלה׃ | 1 |
Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama, nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo.
הודו ליהוה בכנור בנבל עשור זמרו לו׃ | 2 |
Mutamandeni Yehova ndi pangwe; muyimbireni Iye nyimbo pa zeze wa zingwe khumi.
שירו לו שיר חדש היטיבו נגן בתרועה׃ | 3 |
Muyimbireni nyimbo yatsopano; imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe.
כי ישר דבר יהוה וכל מעשהו באמונה׃ | 4 |
Pakuti mawu a Yehova ndi olungama ndi owona; Iye ndi wokhulupirika pa zonse zimene amachita.
אהב צדקה ומשפט חסד יהוה מלאה הארץ׃ | 5 |
Yehova amakonda chilungamo ndipo amaweruza molungama; dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chake chosatha.
בדבר יהוה שמים נעשו וברוח פיו כל צבאם׃ | 6 |
Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa, zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.
כנס כנד מי הים נתן באצרות תהומות׃ | 7 |
Iye amasonkhanitsa pamodzi madzi a mʼnyanja mʼmitsuko; amayika zozama mʼnyumba zosungiramo.
ייראו מיהוה כל הארץ ממנו יגורו כל ישבי תבל׃ | 8 |
Dziko lonse lapansi liope Yehova; anthu onse amulemekeze Iye.
כי הוא אמר ויהי הוא צוה ויעמד׃ | 9 |
Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo; Iye analamulira ndipo zinakhazikika.
יהוה הפיר עצת גוים הניא מחשבות עמים׃ | 10 |
Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina; Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri.
עצת יהוה לעולם תעמד מחשבות לבו לדר ודר׃ | 11 |
Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya, zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.
אשרי הגוי אשר יהוה אלהיו העם בחר לנחלה לו׃ | 12 |
Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova, anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.
משמים הביט יהוה ראה את כל בני האדם׃ | 13 |
Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi ndi kuona anthu onse;
ממכון שבתו השגיח אל כל ישבי הארץ׃ | 14 |
kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira onse amene amakhala pa dziko lapansi.
היצר יחד לבם המבין אל כל מעשיהם׃ | 15 |
Iye amene amapanga mitima ya onse, amaona zonse zimene akuchita.
אין המלך נושע ברב חיל גבור לא ינצל ברב כח׃ | 16 |
Palibe mfumu imene imapulumutsidwa chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo; palibe msilikali amene amathawa ndi mphamvu zake zazikulu.
שקר הסוס לתשועה וברב חילו לא ימלט׃ | 17 |
Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso, ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa.
הנה עין יהוה אל יראיו למיחלים לחסדו׃ | 18 |
Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye; amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,
להציל ממות נפשם ולחיותם ברעב׃ | 19 |
kuwawombola iwo ku imfa ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala.
נפשנו חכתה ליהוה עזרנו ומגננו הוא׃ | 20 |
Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo; Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.
כי בו ישמח לבנו כי בשם קדשו בטחנו׃ | 21 |
Mwa Iye mitima yathu imakondwera, pakuti ife timadalira dzina lake loyera.
יהי חסדך יהוה עלינו כאשר יחלנו לך׃ | 22 |
Chikondi chanu chosatha chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.