< תהילים 3 >

מזמור לדוד בברחו מפני אבשלום בנו יהוה מה רבו צרי רבים קמים עלי׃ 1
Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu. Inu Yehova, achulukadi adani anga! Achulukadi amene andiwukira!
רבים אמרים לנפשי אין ישועתה לו באלהים סלה׃ 2
Ambiri akunena za ine kuti, “Mulungu sadzamupulumutsa.” (Sela)
ואתה יהוה מגן בעדי כבודי ומרים ראשי׃ 3
Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza, Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
קולי אל יהוה אקרא ויענני מהר קדשו סלה׃ 4
Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera. (Sela)
אני שכבתי ואישנה הקיצותי כי יהוה יסמכני׃ 5
Ine ndimagona ndi kupeza tulo; ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.
לא אירא מרבבות עם אשר סביב שתו עלי׃ 6
Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.
קומה יהוה הושיעני אלהי כי הכית את כל איבי לחי שני רשעים שברת׃ 7
Dzukani, Inu Yehova! Pulumutseni, Inu Mulungu wanga. Akantheni adani anga onse pa msagwada; gululani mano a anthu oyipa.
ליהוה הישועה על עמך ברכתך סלה׃ 8
Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso akhale pa anthu anu. (Sela)

< תהילים 3 >