< תהילים 29 >

מזמור לדוד הבו ליהוה בני אלים הבו ליהוה כבוד ועז׃ 1
Salimo la Davide. Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
הבו ליהוה כבוד שמו השתחוו ליהוה בהדרת קדש׃ 2
Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake, pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.
קול יהוה על המים אל הכבוד הרעים יהוה על מים רבים׃ 3
Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi; Mulungu waulemerero abangula, Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
קול יהוה בכח קול יהוה בהדר׃ 4
Liwu la Yehova ndi lamphamvu; liwu la Yehova ndi laulemerero.
קול יהוה שבר ארזים וישבר יהוה את ארזי הלבנון׃ 5
Liwu la Yehova limathyola mikungudza; Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
וירקידם כמו עגל לבנון ושרין כמו בן ראמים׃ 6
Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe, Siriyoni ngati mwana wa njati:
קול יהוה חצב להבות אש׃ 7
Liwu la Yehova limakantha ngati kungʼanima kwa mphenzi.
קול יהוה יחיל מדבר יחיל יהוה מדבר קדש׃ 8
Liwu la Yehova limagwedeza chipululu; Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
קול יהוה יחולל אילות ויחשף יערות ובהיכלו כלו אמר כבוד׃ 9
Liwu la Yehova limapindapinda mibawa ndi kuyeretsa nkhalango. Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”
יהוה למבול ישב וישב יהוה מלך לעולם׃ 10
Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira, Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.
יהוה עז לעמו יתן יהוה יברך את עמו בשלום׃ 11
Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake; Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.

< תהילים 29 >