< תהילים 21 >

למנצח מזמור לדוד יהוה בעזך ישמח מלך ובישועתך מה יגיל מאד׃ 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu, chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka!
תאות לבו נתתה לו וארשת שפתיו בל מנעת סלה׃ 2
Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake. (Sela)
כי תקדמנו ברכות טוב תשית לראשו עטרת פז׃ 3
Inu munayilandira ndi madalitso ochuluka ndipo munayiveka chipewa chaufumu chagolide weniweni pa mutu wake.
חיים שאל ממך נתתה לו ארך ימים עולם ועד׃ 4
Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa masiku ochuluka kwamuyaya.
גדול כבודו בישועתך הוד והדר תשוה עליו׃ 5
Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu; Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.
כי תשיתהו ברכות לעד תחדהו בשמחה את פניך׃ 6
Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya, Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu.
כי המלך בטח ביהוה ובחסד עליון בל ימוט׃ 7
Pakuti mfumu imadalira Yehova; kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba, iyo sidzagwedezeka.
תמצא ידך לכל איביך ימינך תמצא שנאיך׃ 8
Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse; dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu.
תשיתמו כתנור אש לעת פניך יהוה באפו יבלעם ותאכלם אש׃ 9
Pa nthawi ya kuonekera kwanu mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha. Mu ukali wake Yehova adzawameza, ndipo moto wake udzawatha.
פרימו מארץ תאבד וזרעם מבני אדם׃ 10
Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi, zidzukulu zawo pakati pa anthu.
כי נטו עליך רעה חשבו מזמה בל יוכלו׃ 11
Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawo sadzapambana;
כי תשיתמו שכם במיתריך תכונן על פניהם׃ 12
pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawo pamene mudzawaloza ndi mivi yanu.
רומה יהוה בעזך נשירה ונזמרה גבורתך׃ 13
Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu, ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu.

< תהילים 21 >