< תהילים 139 >

למנצח לדוד מזמור יהוה חקרתני ותדע׃ 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Inu Yehova, mwandisanthula ndipo mukundidziwa.
אתה ידעת שבתי וקומי בנתה לרעי מרחוק׃ 2
Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka; mumazindikira maganizo anga muli kutali.
ארחי ורבעי זרית וכל דרכי הסכנתה׃ 3
Mumapenyetsetsa pamene ndikutuluka ndi kugona kwanga; mumadziwa njira zanga zonse.
כי אין מלה בלשוני הן יהוה ידעת כלה׃ 4
Mawu asanatuluke pa lilime langa mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova.
אחור וקדם צרתני ותשת עלי כפכה׃ 5
Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo komwe; mwasanjika dzanja lanu pa ine.
פלאיה דעת ממני נשגבה לא אוכל לה׃ 6
Nzeru zimenezi ndi zopitirira nzeru zanga, ndi zapamwamba kuti ine ndizipeze.
אנה אלך מרוחך ואנה מפניך אברח׃ 7
Kodi ndingapite kuti kufuna kuzemba Mzimu wanu? Kodi ndingathawire kuti kuchoka pamaso panu?
אם אסק שמים שם אתה ואציעה שאול הנך׃ (Sheol h7585) 8
Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko; ndikakagona ku malo a anthu akufa, Inu muli komweko. (Sheol h7585)
אשא כנפי שחר אשכנה באחרית ים׃ 9
Ngati ndiwulukira kotulukira dzuwa, ngati ndikakhala ku malekezero a nyanja,
גם שם ידך תנחני ותאחזני ימינך׃ 10
kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandigwiriziza.
ואמר אך חשך ישופני ולילה אור בעדני׃ 11
Ndikanena kuti, “Zoonadi, mdima udzandibisa ndithu ndipo kuwunika kukhale mdima mondizungulira,”
גם חשך לא יחשיך ממך ולילה כיום יאיר כחשיכה כאורה׃ 12
komabe mdimawo sudzakhala mdima kwa Inu; usiku udzawala ngati masana, pakuti mdima uli ngati kuwunika kwa Inu.
כי אתה קנית כליתי תסכני בבטן אמי׃ 13
Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga; munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.
אודך על כי נוראות נפליתי נפלאים מעשיך ונפשי ידעת מאד׃ 14
Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa; ntchito zanu ndi zodabwitsa, zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
לא נכחד עצמי ממך אשר עשיתי בסתר רקמתי בתחתיות ארץ׃ 15
Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi, pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.
גלמי ראו עיניך ועל ספרך כלם יכתבו ימים יצרו ולא אחד בהם׃ 16
Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe. Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.
ולי מה יקרו רעיך אל מה עצמו ראשיהם׃ 17
Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu, ndi zosawerengeka ndithu!
אספרם מחול ירבון הקיצתי ועודי עמך׃ 18
Ndikanaziwerenga, zikanakhala zochuluka kuposa mchenga; pamene ndadzuka, ndili nanube.
אם תקטל אלוה רשע ואנשי דמים סורו מני׃ 19
Ndi bwino mukanangopha anthu oyipa, Inu Mulungu! Chokereni inu anthu owononga anzanu!
אשר יאמרך למזמה נשא לשוא עריך׃ 20
Amayankhula za Inu ndi zolinga zoyipa; adani anu amagwiritsa ntchito dzina lanu molakwika.
הלוא משנאיך יהוה אשנא ובתקוממיך אתקוטט׃ 21
Kodi ine sindidana nawo amene amakudani, Inu Yehova? Kodi sindinyansidwa nawo amene amakuwukirani?
תכלית שנאה שנאתים לאויבים היו לי׃ 22
Ndimadana nawo kwathunthu; ndi adani anga.
חקרני אל ודע לבבי בחנני ודע שרעפי׃ 23
Santhuleni, Inu Mulungu ndipo mudziwe mtima wanga; Yeseni ndipo mudziwe zolingalira zanga.
וראה אם דרך עצב בי ונחני בדרך עולם׃ 24
Onani ngati muli mayendedwe aliwonse oyipa mwa ine, ndipo munditsogolere mʼnjira yanu yamuyaya.

< תהילים 139 >