< תהילים 116 >

אהבתי כי ישמע יהוה את קולי תחנוני׃ 1
Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga; Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.
כי הטה אזנו לי ובימי אקרא׃ 2
Pakuti ananditchera khutu, ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.
אפפוני חבלי מות ומצרי שאול מצאוני צרה ויגון אמצא׃ (Sheol h7585) 3
Zingwe za imfa zinandizinga, zoopsa za ku dziko la anthu akufa zinandigwera; ndinapeza mavuto ndi chisoni. (Sheol h7585)
ובשם יהוה אקרא אנה יהוה מלטה נפשי׃ 4
Pamenepo ndinayitana dzina la Yehova: “Inu Yehova, pulumutseni!”
חנון יהוה וצדיק ואלהינו מרחם׃ 5
Yehova ndi wokoma mtima ndi wolungama Mulungu wathu ndi wodzaza ndi chifundo.
שמר פתאים יהוה דלותי ולי יהושיע׃ 6
Yehova amateteza munthu wodzichepetsa mtima; pamene ndinali ndi chosowa chachikulu, Iye anandipulumutsa.
שובי נפשי למנוחיכי כי יהוה גמל עליכי׃ 7
Pumula iwe moyo wanga, pakuti Yehova wakuchitira zokoma.
כי חלצת נפשי ממות את עיני מן דמעה את רגלי מדחי׃ 8
Pakuti Inu Yehova mwapulumutsa moyo wanga ku imfa, maso anga ku misozi, mapazi anga kuti angapunthwe,
אתהלך לפני יהוה בארצות החיים׃ 9
kuti ine ndiyende pamaso pa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.
האמנתי כי אדבר אני עניתי מאד׃ 10
Ine ndinakhulupirira; choncho ndinati, “Ndasautsidwa kwambiri.”
אני אמרתי בחפזי כל האדם כזב׃ 11
Ndipo ndili mʼnkhawa yanga ndinati, “Anthu onse ndi abodza.”
מה אשיב ליהוה כל תגמולוהי עלי׃ 12
Ndingamubwezere chiyani Yehova, chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira?
כוס ישועות אשא ובשם יהוה אקרא׃ 13
Ndidzakweza chikho cha chipulumutso ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.
נדרי ליהוה אשלם נגדה נא לכל עמו׃ 14
Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova pamaso pa anthu ake onse.
יקר בעיני יהוה המותה לחסידיו׃ 15
Imfa ya anthu oyera mtima ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova.
אנה יהוה כי אני עבדך אני עבדך בן אמתך פתחת למוסרי׃ 16
Inu Yehova, zoonadi ndine mtumiki wanu: ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; Inu mwamasula maunyolo anga.
לך אזבח זבח תודה ובשם יהוה אקרא׃ 17
Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.
נדרי ליהוה אשלם נגדה נא לכל עמו׃ 18
Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova pamaso pa anthu ake onse,
בחצרות בית יהוה בתוככי ירושלם הללו יה׃ 19
mʼmabwalo a nyumba ya Yehova, mʼkati mwako iwe Yerusalemu. Tamandani Yehova.

< תהילים 116 >