< תהילים 109 >
למנצח לדוד מזמור אלהי תהלתי אל תחרש׃ | 1 |
Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Salimo la Davide. Mulungu amene ndimakutamandani, musakhale chete,
כי פי רשע ופי מרמה עלי פתחו דברו אתי לשון שקר׃ | 2 |
pakuti anthu oyipa ndi achinyengo atsekula pakamwa pawo kutsutsana nane; iwo ayankhula motsutsana nane ndi malilime abodza.
ודברי שנאה סבבוני וילחמוני חנם׃ | 3 |
Andizungulira ndi mawu audani, amandinena popanda chifukwa.
תחת אהבתי ישטנוני ואני תפלה׃ | 4 |
Mʼmalo mwa chikondi changa amandineneza, koma ine ndine munthu wapemphero.
וישימו עלי רעה תחת טובה ושנאה תחת אהבתי׃ | 5 |
Iwo amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino, ndi udani mʼmalo mwa chikondi changa.
הפקד עליו רשע ושטן יעמד על ימינו׃ | 6 |
Sankhani munthu woyipa kuti amutsutse iye; lolani wotsutsa ayime ku dzanja lake lamanja.
בהשפטו יצא רשע ותפלתו תהיה לחטאה׃ | 7 |
Pamene aweruzidwa, apezeke kuti ndi wolakwa, ndipo mapemphero ake amutsutse.
יהיו ימיו מעטים פקדתו יקח אחר׃ | 8 |
Masiku ake akhale owerengeka; munthu wina atenge malo ake a utsogoleri.
יהיו בניו יתומים ואשתו אלמנה׃ | 9 |
Ana ake akhale amasiye ndipo mkazi wake akhale wopanda mwamuna.
ונוע ינועו בניו ושאלו ודרשו מחרבותיהם׃ | 10 |
Ana ake akhale oyendayenda ndi opemphapempha; apirikitsidwe kuchoka pa mabwinja a nyumba zawo.
ינקש נושה לכל אשר לו ויבזו זרים יגיעו׃ | 11 |
Wokongoza alande zonse zimene ali nazo; alendo afunkhe ntchito za manja ake.
אל יהי לו משך חסד ואל יהי חונן ליתומיו׃ | 12 |
Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima kapena kumvera chisoni ana ake amasiye.
יהי אחריתו להכרית בדור אחר ימח שמם׃ | 13 |
Zidzukulu zake zithe nʼkufa, mayina awo afafanizidwe mu mʼbado wotsatirawo.
יזכר עון אבתיו אל יהוה וחטאת אמו אל תמח׃ | 14 |
Mphulupulu za makolo ake zikumbukiridwe pamaso pa Yehova; tchimo la amayi ake lisadzafafanizidwe.
יהיו נגד יהוה תמיד ויכרת מארץ זכרם׃ | 15 |
Machimo awo akhale pamaso pa Yehova nthawi zonse, kuti Iye achotse chikumbutso chawo pa dziko lapansi.
יען אשר לא זכר עשות חסד וירדף איש עני ואביון ונכאה לבב למותת׃ | 16 |
Pakuti iye sanaganizirepo zochita chifundo, koma anazunza mpaka kuwapha anthu osauka ndi osweka mtima.
ויאהב קללה ותבואהו ולא חפץ בברכה ותרחק ממנו׃ | 17 |
Anakonda kutemberera, matembererowo abwerere kwa iye; sanakondwe nʼkudalitsa anthu ena, choncho madalitso akhale kutali naye.
וילבש קללה כמדו ותבא כמים בקרבו וכשמן בעצמותיו׃ | 18 |
Anavala kutemberera ngati chovala; kutemberera kunalowa mʼthupi lake ngati madzi, kulowa mʼmafupa ake ngati mafuta.
תהי לו כבגד יעטה ולמזח תמיד יחגרה׃ | 19 |
Matemberero akhale ngati chofunda chodzikutira nacho, ngati lamba wovala tsiku ndi tsiku.
זאת פעלת שטני מאת יהוה והדברים רע על נפשי׃ | 20 |
Awa akhale malipiro ochokera kwa Yehova pa onditsutsa anga, kwa iwo amene amayankhula zoyipa za ine.
ואתה יהוה אדני עשה אתי למען שמך כי טוב חסדך הצילני׃ | 21 |
Koma Inu Ambuye Wamphamvuzonse, muchite nane molingana ndi dzina lanu, chifukwa cha ubwino wa chikondi chanu, pulumutseni.
כי עני ואביון אנכי ולבי חלל בקרבי׃ | 22 |
Pakuti ndine wosauka ndi wosowa, ndipo mtima wanga ukuwawa mʼkati mwanga.
כצל כנטותו נהלכתי ננערתי כארבה׃ | 23 |
Ndikuzimirira ngati mthunzi wa kumadzulo, ndapirikitsidwa ngati dzombe.
ברכי כשלו מצום ובשרי כחש משמן׃ | 24 |
Mawondo anga afowoka chifukwa cha kusala zakudya, thupi langa lawonda ndi mutu wanga womwe.
ואני הייתי חרפה להם יראוני יניעון ראשם׃ | 25 |
Ndine chinthu chotonzedwa kwa otsutsana nane; akandiona, amapukusa mitu yawo.
עזרני יהוה אלהי הושיעני כחסדך׃ | 26 |
Thandizeni Inu Yehova Mulungu wanga; pulumutseni molingana ndi chikondi chanu.
וידעו כי ידך זאת אתה יהוה עשיתה׃ | 27 |
Adaniwo adziwe kuti limeneli ndi dzanja lanu, kuti Inu Yehova mwachita zimenezi.
יקללו המה ואתה תברך קמו ויבשו ועבדך ישמח׃ | 28 |
Angathe kutemberera, koma Inu mudzadalitsa; pamene iwo andiputa adzachititsidwa manyazi, koma mtumiki wanu adzasangalala.
ילבשו שוטני כלמה ויעטו כמעיל בשתם׃ | 29 |
Onditsutsa adzavekedwa mnyozo, ndipo adzadzifunditsa manyazi ngati chovala.
אודה יהוה מאד בפי ובתוך רבים אהללנו׃ | 30 |
Ndi pakamwa panga ndidzathokoza Yehova kwambiri; ndidzamutamanda mʼgulu lalikulu la anthu.
כי יעמד לימין אביון להושיע משפטי נפשו׃ | 31 |
Popeza Iye amayima ku dzanja lamanja la munthu wosowayo, kupulumutsa moyo wake kwa iwo amene agamula molakwa.