< תהילים 106 >

הללויה הודו ליהוה כי טוב כי לעולם חסדו׃ 1
Tamandani Yehova. Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake ndi chosatha.
מי ימלל גבורות יהוה ישמיע כל תהלתו׃ 2
Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova kapena kumutamanda mokwanira?
אשרי שמרי משפט עשה צדקה בכל עת׃ 3
Odala ndi amene amasunga chilungamo, amene amachita zolungama nthawi zonse.
זכרני יהוה ברצון עמך פקדני בישועתך׃ 4
Mundikumbukire Yehova, pamene mukuonetsa kukoma mtima kwanu kwa anthu anu, bwerani mudzandithandize pamene mukuwapulumutsa iwo,
לראות בטובת בחיריך לשמח בשמחת גויך להתהלל עם נחלתך׃ 5
kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika, kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani.
חטאנו עם אבותינו העוינו הרשענו׃ 6
Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu; tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.
אבותינו במצרים לא השכילו נפלאותיך לא זכרו את רב חסדיך וימרו על ים בים סוף׃ 7
Pamene makolo athu anali mu Igupto, sanalingalire za zozizwitsa zanu; iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka, ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.
ויושיעם למען שמו להודיע את גבורתו׃ 8
Komabe Iye anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake, kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.
ויגער בים סוף ויחרב ויוליכם בתהמות כמדבר׃ 9
Anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inawuma; anawatsogolera mʼnyanja yakuya ngati akuyenda mʼchipululu.
ויושיעם מיד שונא ויגאלם מיד אויב׃ 10
Anawapulumutsa mʼdzanja la amaliwongo; anawawombola mʼdzanja la mdani.
ויכסו מים צריהם אחד מהם לא נותר׃ 11
Madzi anamiza adani awo, palibe mmodzi wa iwo anapulumuka.
ויאמינו בדבריו ישירו תהלתו׃ 12
Kenaka iwo anakhulupirira malonjezo ake ndi kuyimba nyimbo zamatamando.
מהרו שכחו מעשיו לא חכו לעצתו׃ 13
Koma posachedwa anayiwala zimene Iye anachita, ndipo sanayembekezere uphungu wake.
ויתאוו תאוה במדבר וינסו אל בישימון׃ 14
Mʼchipululu, anadzipereka ku zilakolako zawo; mʼdziko lopanda kanthu anayesa Mulungu.
ויתן להם שאלתם וישלח רזון בנפשם׃ 15
Choncho Iye anawapatsa chimene anapempha, koma anatumiza nthenda yowondetsa.
ויקנאו למשה במחנה לאהרן קדוש יהוה׃ 16
Mʼmisasa, anachitira nsanje Mose ndi Aaroni, amene Yehova anadzipatulira.
תפתח ארץ ותבלע דתן ותכס על עדת אבירם׃ 17
Nthaka inatsekuka ndipo inameza Datani; inakwirira gulu la Abiramu.
ותבער אש בעדתם להבה תלהט רשעים׃ 18
Moto unayaka pakati pa otsatira awo; lawi lamoto linapsereza anthu oyipa.
יעשו עגל בחרב וישתחוו למסכה׃ 19
Iwo anapanga mwana wangʼombe pa Horebu ndi kulambira fano loyengedwa kuchokera ku chitsulo.
וימירו את כבודם בתבנית שור אכל עשב׃ 20
Anasinthanitsa ulemerero wawo ndi fano la ngʼombe yayimuna imene imadya udzu.
שכחו אל מושיעם עשה גדלות במצרים׃ 21
Anayiwala Mulungu amene anawapulumutsa, amene anachita zinthu zazikulu mu Igupto,
נפלאות בארץ חם נוראות על ים סוף׃ 22
zozizwitsa mʼdziko la Hamu ndi machitidwe ake woopsa pa Nyanja Yofiira.
ויאמר להשמידם לולי משה בחירו עמד בפרץ לפניו להשיב חמתו מהשחית׃ 23
Choncho Iye anawawuza kuti adzawawononga, pakanapanda Mose, mtumiki wake wosankhidwa, kuyima pamaso pake, ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usawawononge.
וימאסו בארץ חמדה לא האמינו לדברו׃ 24
Motero iwo ananyoza dziko lokoma; sanakhulupirire malonjezo ake.
וירגנו באהליהם לא שמעו בקול יהוה׃ 25
Anangʼungʼudza mʼmatenti mwawo ndipo sanamvere Yehova.
וישא ידו להם להפיל אותם במדבר׃ 26
Kotero Iye analumbira atakweza dzanja lake, kuti adzachititsa kuti iwowo afere mʼchipululu,
ולהפיל זרעם בגוים ולזרותם בארצות׃ 27
kuchititsa kuti zidzukulu zawo zifere pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsa mʼdziko lonse.
ויצמדו לבעל פעור ויאכלו זבחי מתים׃ 28
Iwo anayamba kupembedza Baala-Peori ndi kudya nsembe zoperekedwa kwa milungu yopanda moyo;
ויכעיסו במעלליהם ותפרץ בם מגפה׃ 29
anaputa mkwiyo wa Yehova pa machitidwe awo oyipa, ndipo mliri unabuka pakati pawo.
ויעמד פינחס ויפלל ותעצר המגפה׃ 30
Koma Finehasi anayimirira ndi kulowererapo, ndipo mliri unaleka.
ותחשב לו לצדקה לדר ודר עד עולם׃ 31
Chimenechi ndicho chinayesedwa chilungamo chake, kwa mibado yosatha imene ikubwera.
ויקציפו על מי מריבה וירע למשה בעבורם׃ 32
Pa madzi a ku Meriba iwo anakwiyitsa Yehova ndipo mavuto anabwera kwa Mose chifukwa cha anthuwo,
כי המרו את רוחו ויבטא בשפתיו׃ 33
pakuti iwowo anawukira mzimu wa Mulungu, ndipo pa milomo ya Mose panatuluka mawu osayenera.
לא השמידו את העמים אשר אמר יהוה להם׃ 34
Aisraeliwo sanawononge mitundu ya anthu monga momwe Yehova anawalamulira.
ויתערבו בגוים וילמדו מעשיהם׃ 35
Koma anasakanizana ndi anthu a mitundu inayo ndi kuphunzira miyambo yawo.
ויעבדו את עצביהם ויהיו להם למוקש׃ 36
Ndipo anapembedza mafano awo, amene anakhala msampha kwa iwowo.
ויזבחו את בניהם ואת בנותיהם לשדים׃ 37
Anapereka nsembe ana awo aamuna ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.
וישפכו דם נקי דם בניהם ובנותיהם אשר זבחו לעצבי כנען ותחנף הארץ בדמים׃ 38
Anakhetsa magazi a anthu osalakwa, magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi, amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanaani, ndipo dziko linayipitsidwa ndi magazi awo.
ויטמאו במעשיהם ויזנו במעלליהם׃ 39
Iwo anadzidetsa okha ndi zimene anachita; ndi machitidwe awo amakhala ngati munthu wachigololo.
ויחר אף יהוה בעמו ויתעב את נחלתו׃ 40
Tsono Yehova anakwiya ndi anthu ake ndipo ananyansidwa ndi cholowa chake.
ויתנם ביד גוים וימשלו בהם שנאיהם׃ 41
Iye anawapereka kwa anthu a mitundu ina, ndipo adani awo anawalamulira.
וילחצום אויביהם ויכנעו תחת ידם׃ 42
Adani awo anawazunza ndi kuwakhazika pansi pa mphamvu yawo.
פעמים רבות יצילם והמה ימרו בעצתם וימכו בעונם׃ 43
Iye ankawapulumutsa nthawi zambiri, koma iwo ankatsimikiza za kuwukira ndipo anawonongeka mʼmachimo awo.
וירא בצר להם בשמעו את רנתם׃ 44
Koma Iye anaona kuzunzika kwawo pamene anamva kulira kwawo;
ויזכר להם בריתו וינחם כרב חסדו׃ 45
Chifukwa cha iwo Iye anakumbukira pangano lake ndipo anawalezera mtima chifukwa cha kukula kwa chikondi chake.
ויתן אותם לרחמים לפני כל שוביהם׃ 46
Iye anachititsa kuti amene anawagwira iwo ukapolo awamvere chisoni.
הושיענו יהוה אלהינו וקבצנו מן הגוים להדות לשם קדשך להשתבח בתהלתך׃ 47
Tipulumutseni Inu Yehova Mulungu wathu, ndipo mutisonkhanitse kuchoka kwa anthu a mitundu ina kuti tithe kuyamika dzina lanu loyera ndi kunyadira mʼmatamando anu.
ברוך יהוה אלהי ישראל מן העולם ועד העולם ואמר כל העם אמן הללו יה׃ 48
Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, Kuyambira muyaya mpaka muyaya. Anthu onse anene kuti, “Ameni!” Tamandani Yehova.

< תהילים 106 >