< תהילים 103 >
לדוד ברכי נפשי את יהוה וכל קרבי את שם קדשו׃ | 1 |
Salimo la Davide. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga; ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.
ברכי נפשי את יהוה ואל תשכחי כל גמוליו׃ | 2 |
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga, ndipo usayiwale zabwino zake zonse.
הסלח לכל עונכי הרפא לכל תחלאיכי׃ | 3 |
Amene amakhululuka machimo ako onse ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,
הגואל משחת חייכי המעטרכי חסד ורחמים׃ | 4 |
amene awombola moyo wako ku dzenje ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu,
המשביע בטוב עדיך תתחדש כנשר נעוריכי׃ | 5 |
amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino, kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.
עשה צדקות יהוה ומשפטים לכל עשוקים׃ | 6 |
Yehova amachita chilungamo ndipo amaweruza molungama onse opsinjika.
יודיע דרכיו למשה לבני ישראל עלילותיו׃ | 7 |
Iye anadziwitsa Mose njira zake, ntchito zake kwa Aisraeli.
רחום וחנון יהוה ארך אפים ורב חסד׃ | 8 |
Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.
לא לנצח יריב ולא לעולם יטור׃ | 9 |
Iye sadzatsutsa nthawi zonse, kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya;
לא כחטאינו עשה לנו ולא כעונתינו גמל עלינו׃ | 10 |
satichitira molingana ndi machimo athu, kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu.
כי כגבה שמים על הארץ גבר חסדו על יראיו׃ | 11 |
Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa;
כרחק מזרח ממערב הרחיק ממנו את פשעינו׃ | 12 |
monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo, koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.
כרחם אב על בנים רחם יהוה על יראיו׃ | 13 |
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
כי הוא ידע יצרנו זכור כי עפר אנחנו׃ | 14 |
pakuti Iye amadziwa momwe tinawumbidwira, amakumbukira kuti ndife fumbi.
אנוש כחציר ימיו כציץ השדה כן יציץ׃ | 15 |
Kunena za munthu, masiku ake ali ngati udzu, amaphuka ngati duwa la mʼmunda;
כי רוח עברה בו ואיננו ולא יכירנו עוד מקומו׃ | 16 |
koma mphepo imawombapo ndipo silionekanso ndipo malo ake sakumbukirikanso.
וחסד יהוה מעולם ועד עולם על יראיו וצדקתו לבני בנים׃ | 17 |
Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa, ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo;
לשמרי בריתו ולזכרי פקדיו לעשותם׃ | 18 |
iwo amene amasunga pangano lake ndi kukumbukira kumvera malangizo ake.
יהוה בשמים הכין כסאו ומלכותו בכל משלה׃ | 19 |
Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba ndipo ufumu wake umalamulira onse.
ברכו יהוה מלאכיו גברי כח עשי דברו לשמע בקול דברו׃ | 20 |
Tamandani Yehova, inu angelo ake, amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula, amene mumamvera mawu ake.
ברכו יהוה כל צבאיו משרתיו עשי רצונו׃ | 21 |
Tamandani Yehova, zolengedwa zonse zakumwamba, inu atumiki ake amene mumachita chifuniro chake.
ברכו יהוה כל מעשיו בכל מקמות ממשלתו ברכי נפשי את יהוה׃ | 22 |
Tamandani Yehova, ntchito yake yonse kulikonse mu ulamuliro wake. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.