< תהילים 10 >

למה יהוה תעמד ברחוק תעלים לעתות בצרה׃ 1
Nʼchifukwa chiyani Yehova mwayima patali? Chifukwa chiyani mukudzibisa nokha pa nthawi ya mavuto?
בגאות רשע ידלק עני יתפשו במזמות זו חשבו׃ 2
Mwa kunyada kwake munthu woyipa asaka wofowoka, amene akodwa mʼnjira zimene iye wakonza.
כי הלל רשע על תאות נפשו ובצע ברך נאץ יהוה׃ 3
Iye amatamandira zokhumba za mu mtima wake; amadalitsa aumbombo ndi kuchitira chipongwe Yehova.
רשע כגבה אפו בל ידרש אין אלהים כל מזמותיו׃ 4
Mwa kunyada kwake woyipa safunafuna Mulungu; mʼmaganizo ake wonse mulibe malo a Mulungu.
יחילו דרכו בכל עת מרום משפטיך מנגדו כל צורריו יפיח בהם׃ 5
Zinthu zake zimamuyendera bwino; iye ndi wamwano ndipo malamulo anu ali nawo kutali; amanyogodola adani ake onse.
אמר בלבו בל אמוט לדר ודר אשר לא ברע׃ 6
Iye amadziyankhulira kuti, “Palibe chimene chidzandigwedeze. Ndidzakhala wokondwa nthawi zonse ndipo sindidzakhala pa mavuto.”
אלה פיהו מלא ומרמות ותך תחת לשונו עמל ואון׃ 7
Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi zoopseza; zovutitsa ndi zoyipa zili pansi pa lilime lake.
ישב במארב חצרים במסתרים יהרג נקי עיניו לחלכה יצפנו׃ 8
Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi, kuchokera pobisalapo amapha anthu osalakwa, amayangʼanayangʼana mwachinsinsi anthu oti awawononge.
יארב במסתר כאריה בסכה יארב לחטוף עני יחטף עני במשכו ברשתו׃ 9
Amabisalira anthu ngati mkango pa zitsamba. Amabisalira kuti agwire anthu opanda mphamvu; amagwira anthu opanda mphamvu ndi kuwakokera mu ukonde wake.
ודכה ישח ונפל בעצומיו חלכאים׃ 10
Anthuwo amawapondaponda ndipo amakomoka; amakhala pansi pa mphamvu zake.
אמר בלבו שכח אל הסתיר פניו בל ראה לנצח׃ 11
Iye amati mu mtima mwake, “Mulungu wayiwala, wabisa nkhope yake ndipo sakuonanso.”
קומה יהוה אל נשא ידך אל תשכח עניים׃ 12
Dzukani Yehova! Onetsani dzanja lanu Inu Mulungu. Musayiwale anthu opanda mphamvu.
על מה נאץ רשע אלהים אמר בלבו לא תדרש׃ 13
Nʼchifukwa chiyani munthu woyipa amachitira chipongwe Mulungu? Chifukwa chiyani amati mu mtima mwake, “Iye sandiyimba mlandu?”
ראתה כי אתה עמל וכעס תביט לתת בידך עליך יעזב חלכה יתום אתה היית עוזר׃ 14
Komatu Inu Mulungu, mumazindikira mavuto ndi zosautsa, mumaganizira zochitapo kanthu. Wovutikayo amadzipereka yekha kwa Inu pakuti Inu ndi mthandizi wa ana amasiye.
שבר זרוע רשע ורע תדרוש רשעו בל תמצא׃ 15
Thyolani dzanja la woyipitsitsa ndi la munthu woyipa; muzengeni mlandu chifukwa cha zoyipa zake zimene sizikanadziwika.
יהוה מלך עולם ועד אבדו גוים מארצו׃ 16
Yehova ndi Mfumu kwamuyaya; mitundu ya anthu idzawonongeka kuchoka mʼdziko lake.
תאות ענוים שמעת יהוה תכין לבם תקשיב אזנך׃ 17
Mumamva Inu Yehova, zokhumba za osautsidwa; mumawalimbikitsa ndipo mumamva kulira kwawo.
לשפט יתום ודך בל יוסיף עוד לערץ אנוש מן הארץ׃ 18
Kuteteza ana amasiye ndi oponderezedwa, ndi cholinga chakuti munthu amene ali wa dziko lapansi asaopsenso.

< תהילים 10 >