< מִשְׁלֵי 9 >
חכמות בנתה ביתה חצבה עמודיה שבעה׃ | 1 |
Nzeru inamanga nyumba yake; inayimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri.
טבחה טבחה מסכה יינה אף ערכה שלחנה׃ | 2 |
Inapha ziweto zake ndipo yasakaniza vinyo wake; inasakaniza vinyo wake ndi kuyala tebulo lake.
שלחה נערתיה תקרא על גפי מרמי קרת׃ | 3 |
Nzeruyo inatuma adzakazi ake, kuti akakhale pamwamba penipeni pa mzinda ndi kukalengeza kuti,
מי פתי יסר הנה חסר לב אמרה לו׃ | 4 |
“Aliyense amene ali munthu wamba, abwere kuno!” Kwa onse opanda nzeru inkanena kuti,
לכו לחמו בלחמי ושתו ביין מסכתי׃ | 5 |
“Bwerani, dzadyeni chakudya changa ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza.
עזבו פתאים וחיו ואשרו בדרך בינה׃ | 6 |
Lekani zopusa zanu kuti mukhale ndi moyo; yendani njira ya nzeru yomvetsa zinthu.”
יסר לץ לקח לו קלון ומוכיח לרשע מומו׃ | 7 |
Aliyense amene amayesa kukonza munthu wonyoza amadziputira minyozo; aliyense amene amadzudzula munthu woyipa amadetsa mbiri yake.
אל תוכח לץ פן ישנאך הוכח לחכם ויאהבך׃ | 8 |
Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe; dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.
תן לחכם ויחכם עוד הודע לצדיק ויוסף לקח׃ | 9 |
Ukalangiza munthu wanzeru ndiye adzapitirira kukhala wanzeru; ukaphunzitsa munthu wolungama ndiye adzawonjezera kuphunzira kwake.
תחלת חכמה יראת יהוה ודעת קדשים בינה׃ | 10 |
Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru; kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.
כי בי ירבו ימיך ויוסיפו לך שנות חיים׃ | 11 |
Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka, ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.
אם חכמת חכמת לך ולצת לבדך תשא׃ | 12 |
Ngati ndiwe wanzeru, nzeru yakoyo idzakupindulitsa; ngati ndiwe wonyoza ena, udzavutika wekha.
אשת כסילות המיה פתיות ובל ידעה מה׃ | 13 |
Uchitsiru ndi mkazi waphokoso, wopulikira ndiponso wosadziwa zinthu.
וישבה לפתח ביתה על כסא מרמי קרת׃ | 14 |
Iye amakhala pa mpando, pa khomo la nyumba yake, pamalo aatali a mu mzinda,
לקרא לעברי דרך המישרים ארחותם׃ | 15 |
kuti aziyitana anthu ongodutsa, amene akunka nayenda njira zawo.
מי פתי יסר הנה וחסר לב ואמרה לו׃ | 16 |
Amati, “Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,” ndipo kwa wopanda nzeru amati,
מים גנובים ימתקו ולחם סתרים ינעם׃ | 17 |
“Madzi akuba ndiye amatsekemera; chakudya chodya mobisa ndi chokoma!”
ולא ידע כי רפאים שם בעמקי שאול קראיה׃ (Sheol ) | 18 |
Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko, ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya. (Sheol )