< מִשְׁלֵי 24 >
אל תקנא באנשי רעה ואל תתאו להיות אתם׃ | 1 |
Usachitire nsanje anthu oyipa, usalakalake kuti uzikhala nawo,
כי שד יהגה לבם ועמל שפתיהם תדברנה׃ | 2 |
pakuti mitima yawo imalingalira chiwawa, ndipo pakamwa pawo pamayankhula zoyambitsa mavuto.
בחכמה יבנה בית ובתבונה יתכונן׃ | 3 |
Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu odziwa zinthu;
ובדעת חדרים ימלאו כל הון יקר ונעים׃ | 4 |
Munthu wodziwa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chamtengowapatali ndiponso chabwino.
גבר חכם בעוז ואיש דעת מאמץ כח׃ | 5 |
Munthu wodziwa zinthu ali ndi mphamvu yayikulu kuposa munthu wanyonga zambiri, ndipo munthu wachidziwitso amaposa munthu wamphamvu.
כי בתחבלות תעשה לך מלחמה ותשועה ברב יועץ׃ | 6 |
Pafunika malangizo kuti ukamenye nkhondo. Pakakhala aphungu ambiri kupambana kumakhalapo.
ראמות לאויל חכמות בשער לא יפתח פיהו׃ | 7 |
Nzeru ndi chinthu chapatali kwambiri kwa chitsiru; chilibe choti chiyankhule pabwalo la milandu pa chipata.
מחשב להרע לו בעל מזמות יקראו׃ | 8 |
Amene amakonzekera kuchita zoyipa adzatchedwa mvundulamadzi.
זמת אולת חטאת ותועבת לאדם לץ׃ | 9 |
Kukonzekera kuchita za uchitsiru ndi tchimo, ndipo munthu wonyoza amanyansa anthu.
התרפית ביום צרה צר כחכה׃ | 10 |
Ngati utaya mtima nthawi ya mavuto ndiye kuti mphamvu yako ndi yochepadi!
הצל לקחים למות ומטים להרג אם תחשוך׃ | 11 |
Uwapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe; uwalanditse amene akuyenda movutika kupita kokaphedwa.
כי תאמר הן לא ידענו זה הלא תכן לבות הוא יבין ונצר נפשך הוא ידע והשיב לאדם כפעלו׃ | 12 |
Ukanena kuti, “Koma ife sitinadziwe kanthu za izi,” kodi Iye amene amasanthula mtima sazindikira zimenezi? Kodi Iye amene amateteza moyo wako sazidziwa zimenezi? Kodi Iye sadzalipira munthu malingana ndi ntchito zake?
אכל בני דבש כי טוב ונפת מתוק על חכך׃ | 13 |
Mwana wanga, uzidya uchi popeza ndi wabwino; uchi wochokera mʼchisa cha njuchi ndi wokoma ukawulawa.
כן דעה חכמה לנפשך אם מצאת ויש אחרית ותקותך לא תכרת׃ | 14 |
Udziwe kuti nzeru ndi yoteronso pa moyo wako; ngati uyipeza nzeruyo, zinthu zidzakuyendera bwino mʼtsogolo, ndipo chiyembekezo chako sichidzapita pachabe.
אל תארב רשע לנוה צדיק אל תשדד רבצו׃ | 15 |
Usachite zachifwamba nyumba ya munthu wolungama ngati munthu woyipa. Usachite nayo nkhondo nyumba yake;
כי שבע יפול צדיק וקם ורשעים יכשלו ברעה׃ | 16 |
paja munthu wolungama akagwa kasanu nʼkawiri amadzukiriranso. Koma woyipa adzathedwa tsoka likadzawafikira.
בנפל אויביך אל תשמח ובכשלו אל יגל לבך׃ | 17 |
Usamakondwera ndi kugwa kwa mdani wako. Mtima wako usamasangalale iye akapunthwa.
פן יראה יהוה ורע בעיניו והשיב מעליו אפו׃ | 18 |
Kuopa kuti Yehova ataziona zimenezi nayipidwa nazo, angaleke kukwiyira mdaniyo.
אל תתחר במרעים אל תקנא ברשעים׃ | 19 |
Usavutike mtima chifukwa cha anthu ochita zoyipa kapena kuchitira nsanje anthu oyipa,
כי לא תהיה אחרית לרע נר רשעים ידעך׃ | 20 |
paja munthu woyipa alibe tsogolo. Moyo wa anthu oyipa adzawuzimitsa ngati nyale.
ירא את יהוה בני ומלך עם שונים אל תתערב׃ | 21 |
Mwana wanga, uziopa Yehova ndi mfumu, ndipo usamagwirizana ndi anthu owachitira mwano,
כי פתאם יקום אידם ופיד שניהם מי יודע׃ | 22 |
awiri amenewa amagwetsa tsoka mwadzidzidzi. Ndani angadziwe mavuto amene angagwetse?
גם אלה לחכמים הכר פנים במשפט בל טוב׃ | 23 |
Malangizo enanso a anthu anzeru ndi awa: Kukondera poweruza mlandu si chinthu chabwino:
אמר לרשע צדיק אתה יקבהו עמים יזעמוהו לאמים׃ | 24 |
Aliyense amene amawuza munthu wolakwa kuti, “Iwe ndi munthu wosalakwa,” anthu a mitundu yonse adzamutemberera, ndi mitundu ya anthu idzayipidwa naye.
ולמוכיחים ינעם ועליהם תבוא ברכת טוב׃ | 25 |
Koma olanga anthu oyipa zinthu zidzawayendera bwino ndipo madalitso ochuluka adzakhala pa iwo.
שפתים ישק משיב דברים נכחים׃ | 26 |
Woyankhula mawu owona ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni.
הכן בחוץ מלאכתך ועתדה בשדה לך אחר ובנית ביתך׃ | 27 |
Ugwiriretu ntchito zako zonse, makamaka za ku munda ndipo pambuyo pake uyambe kumanga nyumba.
אל תהי עד חנם ברעך והפתית בשפתיך׃ | 28 |
Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa, kapena kugwiritsa ntchito pakamwa pako kunena zachinyengo.
אל תאמר כאשר עשה לי כן אעשה לו אשיב לאיש כפעלו׃ | 29 |
Usanene kuti, “Ine ndidzamuchitira iye monga momwe wandichitira ine; ndidzamubwezera munthu ameneyo zimene anandichitira.”
על שדה איש עצל עברתי ועל כרם אדם חסר לב׃ | 30 |
Ndinkayenda mʼmbali mwa munda wa munthu waulesi ndinadutsa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru.
והנה עלה כלו קמשנים כסו פניו חרלים וגדר אבניו נהרסה׃ | 31 |
Ndinapeza kuti paliponse mʼmundamo munali mutamera minga, mʼnthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utawonongeka.
ואחזה אנכי אשית לבי ראיתי לקחתי מוסר׃ | 32 |
Tsono nditaona ndinayamba kuganizira mu mtima mwanga ndipo ndinatolapo phunziro ili:
מעט שנות מעט תנומות מעט חבק ידים לשכב׃ | 33 |
Ukati, “Bwanji ndigone pangʼono,” kapena “Ndiwodzereko pangʼono,” kapenanso “Ndipinde manja pangʼono kuti ndipumule,”
ובא מתהלך רישך ומחסריך כאיש מגן׃ | 34 |
umphawi udzafika pa iwe ngati mbala ndipo usiwa udzakupeza ngati munthu wachifwamba.