< מִשְׁלֵי 11 >

מאזני מרמה תועבת יהוה ואבן שלמה רצונו׃ 1
Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa, koma amakondwera ndi muyeso woyenera.
בא זדון ויבא קלון ואת צנועים חכמה׃ 2
Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi, koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.
תמת ישרים תנחם וסלף בוגדים ושדם׃ 3
Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera, koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.
לא יועיל הון ביום עברה וצדקה תציל ממות׃ 4
Chuma sichithandiza pa tsiku lawukali wa Mulungu, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
צדקת תמים תישר דרכו וברשעתו יפל רשע׃ 5
Chilungamo cha anthu angwiro chimawongolera moyo wawo, koma ntchito zoyipa zimagwetsa mwini wake yemweyo.
צדקת ישרים תצילם ובהות בגדים ילכדו׃ 6
Chilungamo cha anthu oyera mtima chimawapulumutsa, koma anthu onyenga adzagwidwa ndi zilakolako zawo zomwe.
במות אדם רשע תאבד תקוה ותוחלת אונים אבדה׃ 7
Pamene munthu woyipa wafa, chiyembekezo chake chimathanso. Chiyembekezo cha munthu wosalungama chimawonongeka.
צדיק מצרה נחלץ ויבא רשע תחתיו׃ 8
Munthu wolungama amapulumutsidwa ku mavuto, koma mʼmalo mwake amagwa mʼmavutomo ndi anthu oyipa.
בפה חנף ישחת רעהו ובדעת צדיקים יחלצו׃ 9
Munthu wosapembedza amawononga mnansi wake ndi pakamwa pake, koma munthu wolungama amapulumuka chifukwa cha kudziwa zinthu.
בטוב צדיקים תעלץ קריה ובאבד רשעים רנה׃ 10
Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, mzinda wonse umakondwera, ndipo oyipa akamawonongeka anthu amafuwula mwachimwemwe.
בברכת ישרים תרום קרת ובפי רשעים תהרס׃ 11
Mzinda umakwezeka chifukwa cha madalitso a anthu oyera mtima, koma umawonongedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oyipa.
בז לרעהו חסר לב ואיש תבונות יחריש׃ 12
Munthu wonyoza mnzake ndi wopanda nzeru, koma munthu wanzeru zomvetsa zinthu amakhala chete.
הולך רכיל מגלה סוד ונאמן רוח מכסה דבר׃ 13
Amene amanka nachita ukazitape amawulula zinsinsi; koma munthu wokhulupirika amasunga pakamwa pake.
באין תחבלות יפל עם ותשועה ברב יועץ׃ 14
Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa; koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso.
רע ירוע כי ערב זר ושנא תקעים בוטח׃ 15
Woperekera mlendo chikole adzapeza mavuto, koma wodana ndi za chikole amakhala pa mtendere.
אשת חן תתמך כבוד ועריצים יתמכו עשר׃ 16
Mkazi wodekha amalandira ulemu, koma amuna ankhanza amangopata chuma.
גמל נפשו איש חסד ועכר שארו אכזרי׃ 17
Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.
רשע עשה פעלת שקר וזרע צדקה שכר אמת׃ 18
Munthu woyipa amalandira malipiro wopanda phindu, koma wochita chilungamo amakolola mphotho yeniyeni.
כן צדקה לחיים ומרדף רעה למותו׃ 19
Munthu wochita za chilungamo amapeza moyo, koma wothamangira zoyipa adzafa.
תועבת יהוה עקשי לב ורצונו תמימי דרך׃ 20
Yehova amanyansidwa ndi anthu a mtima wokhotakhota koma amakondwera ndi anthu a makhalidwe angwiro.
יד ליד לא ינקה רע וזרע צדיקים נמלט׃ 21
Zoonadi, anthu oyipa adzalangidwa, koma anthu olungama adzapulumuka.
נזם זהב באף חזיר אשה יפה וסרת טעם׃ 22
Monga imaonekera mphete yagolide ikakhala pa mphuno ya nkhumba, ndi momwenso amaonekera mkazi wokongola wamʼkamwa.
תאות צדיקים אך טוב תקות רשעים עברה׃ 23
Zokhumba za anthu olungama zimathera pa zabwino zokhazokha, koma chiyembekezo cha anthu oyipa chimathera mu ukali wa Mulungu.
יש מפזר ונוסף עוד וחושך מישר אך למחסור׃ 24
Munthu wina amapatsako anzake zinthu mwaufulu nʼkumangolemererabe; wina amamana chomwe akanatha kupereka, koma kumanka nasawukabe.
נפש ברכה תדשן ומרוה גם הוא יורא׃ 25
Munthu wopereka mowolowamanja adzalemera; iye amene amathandiza ena iyenso adzathandizidwa.
מנע בר יקבהו לאום וברכה לראש משביר׃ 26
Anthu amatemberera womana anzake chakudya, koma madalitso amakhala pamutu pa munthu amene amagulitsa chakudyacho.
שחר טוב יבקש רצון ודרש רעה תבואנו׃ 27
Iye amene amafunafuna zabwino mwakhama amapeza zabwinozo, koma wofunafuna zoyipa zidzamupeza.
בוטח בעשרו הוא יפל וכעלה צדיקים יפרחו׃ 28
Aliyense amene amadalira chuma chake adzafota, koma wolungama adzaphukira ngati tsamba lobiriwira.
עוכר ביתו ינחל רוח ועבד אויל לחכם לב׃ 29
Wovutitsa a mʼnyumba mwake adzalowa mʼmavuto, ndipo chitsiru chidzakhala kapolo wa munthu wa nzeru.
פרי צדיק עץ חיים ולקח נפשות חכם׃ 30
Chipatso cha ntchito zabwino ndi moyo, ndipo kusatsata malamulo kumawonongetsa moyo.
הן צדיק בארץ ישלם אף כי רשע וחוטא׃ 31
Ngati anthu olungama amalandira mphotho zawo pa dziko lapansi, kuli bwanji anthu osapembedza ndi ochimwa!

< מִשְׁלֵי 11 >