< במדבר 31 >

וידבר יהוה אל משה לאמר׃ 1
Yehova anawuza Mose kuti,
נקם נקמת בני ישראל מאת המדינים אחר תאסף אל עמיך׃ 2
“Uwabwezere zoyipa Amidiyani chifukwa cha zimene anachitira Aisraeli. Ukatha kuchita zimenezi, iwe udzamwalira.”
וידבר משה אל העם לאמר החלצו מאתכם אנשים לצבא ויהיו על מדין לתת נקמת יהוה במדין׃ 3
Ndipo Mose anati kwa Aisraeli, “Perekani zida kwa ena mwa anthu anu kuti akamenyane ndi Amidiyani ndi kuwabwezera choyipa mʼmalo mwa Yehova.
אלף למטה אלף למטה לכל מטות ישראל תשלחו לצבא׃ 4
Mutumize ku nkhondoko amuna 1,000 kuchokera ku fuko lililonse la Aisraeli.”
וימסרו מאלפי ישראל אלף למטה שנים עשר אלף חלוצי צבא׃ 5
Choncho amuna okwana 12,000 anatenga zida kukonzekera nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse la Aisraeli.
וישלח אתם משה אלף למטה לצבא אתם ואת פינחס בן אלעזר הכהן לצבא וכלי הקדש וחצצרות התרועה בידו׃ 6
Mose anawatumiza ku nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse pamodzi ndi Finehasi mwana wa Eliezara wansembe amene ananyamula zipangizo zochokera ku malo wopatulika ndi malipenga okaliza.
ויצבאו על מדין כאשר צוה יהוה את משה ויהרגו כל זכר׃ 7
Iwo anamenyana ndi Amidiyani monga momwe Yehova analamulira Mose ndipo anapha mwamuna aliyense.
ואת מלכי מדין הרגו על חלליהם את אוי ואת רקם ואת צור ואת חור ואת רבע חמשת מלכי מדין ואת בלעם בן בעור הרגו בחרב׃ 8
Mwa anthu ophedwawo munali Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani. Ndipo anaphanso ndi lupanga Balaamu mwana wa Beori.
וישבו בני ישראל את נשי מדין ואת טפם ואת כל בהמתם ואת כל מקנהם ואת כל חילם בזזו׃ 9
Aisraeli anagwira ukapolo amayi a Chimidiyani ndi ana awo ndipo analandanso ngʼombe, ziweto zawo zina zonse ndi katundu wawo yense.
ואת כל עריהם במושבתם ואת כל טירתם שרפו באש׃ 10
Anawotcha mizinda yonse imene Amidiyani ankakhalamo pamodzi ndi misasa yawo yonse.
ויקחו את כל השלל ואת כל המלקוח באדם ובבהמה׃ 11
Anatenga zonse zimene analanda ku nkhondoko, anthu ndi zoweta zomwe.
ויבאו אל משה ואל אלעזר הכהן ואל עדת בני ישראל את השבי ואת המלקוח ואת השלל אל המחנה אל ערבת מואב אשר על ירדן ירחו׃ 12
Ndipo anabwera nawo akapolowo ndi zolanda ku nkhondozo kwa Mose ndi kwa wansembe Eliezara ndi kwa gulu lonse la Aisraeli ku misasa yawo ku chigwa cha Mowabu, mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko.
ויצאו משה ואלעזר הכהן וכל נשיאי העדה לקראתם אל מחוץ למחנה׃ 13
Mose, wansembe Eliezara ndi atsogoleri onse a gululo anapita kukakumana nawo kunja kwa misasa.
ויקצף משה על פקודי החיל שרי האלפים ושרי המאות הבאים מצבא המלחמה׃ 14
Mose anakwiya nawo akuluakulu a magulu a ankhondowo: olamulira 1,000 ndi olamulira 100, amene ankachokera ku nkhondo.
ויאמר אליהם משה החייתם כל נקבה׃ 15
Iye anafunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani mwawaleka amoyo amayi onsewa?”
הן הנה היו לבני ישראל בדבר בלעם למסר מעל ביהוה על דבר פעור ותהי המגפה בעדת יהוה׃ 16
Paja iwo ndi amene ankatsatira uphungu wa Balaamu ndiponso ndi amene anachititsa Aisraeli kuti asiye Yehova pa zimene zinachitika ku Peori, kotero mliri unagwera anthu a Yehova.
ועתה הרגו כל זכר בטף וכל אשה ידעת איש למשכב זכר הרגו׃ 17
Tsopano iphani munthu wamwamuna aliyense. Ndiponso iphani mayi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna,
וכל הטף בנשים אשר לא ידעו משכב זכר החיו לכם׃ 18
koma sungani mtsikana aliyense amene sanagonepo ndi mwamuna.
ואתם חנו מחוץ למחנה שבעת ימים כל הרג נפש וכל נגע בחלל תתחטאו ביום השלישי וביום השביעי אתם ושביכם׃ 19
“Inu nonse amene mwaphapo wina wake, kapena kukhudza aliyense amene anaphedwa mukhale kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachitatu mudziyeretse nokha pamodzi ndi akapolo anu.
וכל בגד וכל כלי עור וכל מעשה עזים וכל כלי עץ תתחטאו׃ 20
Muyeretsenso zovala zanu ndi china chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ubweya wa mbuzi kapenanso ndi mtengo.”
ויאמר אלעזר הכהן אל אנשי הצבא הבאים למלחמה זאת חקת התורה אשר צוה יהוה את משה׃ 21
Tsono wansembe Eliezara anati kwa asilikali amene anapita ku nkhondo aja, “Lamulo limene Yehova anapereka kwa Mose ndi ili:
אך את הזהב ואת הכסף את הנחשת את הברזל את הבדיל ואת העפרת׃ 22
Golide, siliva, mkuwa, chitsulo, chiwaya, mtovu
כל דבר אשר יבא באש תעבירו באש וטהר אך במי נדה יתחטא וכל אשר לא יבא באש תעבירו במים׃ 23
ndi china chilichonse chimene sichingapse ndi moto muchidutsitse pa moto, ndipo chidzayeretsedwa. Komanso chiyeretsedwe ndi madzi oyeretsa. Ndipo chilichonse chimene chingapse ndi moto muchidutsitse mʼmadzimo.
וכבסתם בגדיכם ביום השביעי וטהרתם ואחר תבאו אל המחנה׃ 24
Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muchape zovala zanu ndipo mudzayera. Mukatero mutha kulowa mu msasa.”
ויאמר יהוה אל משה לאמר׃ 25
Yehova anawuza Mose kuti,
שא את ראש מלקוח השבי באדם ובבהמה אתה ואלעזר הכהן וראשי אבות העדה׃ 26
“Iwe ndi wansembe Eliezara ndiponso akuluakulu a mabanja a anthuwa, muwerenge anthu onse ndi ziweto zomwe zinagwidwa ku nkhondo.
וחצית את המלקוח בין תפשי המלחמה היצאים לצבא ובין כל העדה׃ 27
Mugawe zolanda ku nkhondozo magawo awiri, lina la ankhondo amene anapita ku nkhondo, lina la anthu onse.
והרמת מכס ליהוה מאת אנשי המלחמה היצאים לצבא אחד נפש מחמש המאות מן האדם ומן הבקר ומן החמרים ומן הצאן׃ 28
Pa gawo la ankhondowo, mutengeko gawo la Yehova, pa zofunkha 500 zilizonse mutengeko chimodzi, pa akapolo, ngʼombe, bulu ndi nkhosa.
ממחציתם תקחו ונתתה לאלעזר הכהן תרומת יהוה׃ 29
Utenge zimenezo pa theka la gawo la ankhondowo ndipo upereke kwa wansembe Eliezara kuti zikhale zopereka zanu kwa Yehova.
וממחצת בני ישראל תקח אחד אחז מן החמשים מן האדם מן הבקר מן החמרים ומן הצאן מכל הבהמה ונתתה אתם ללוים שמרי משמרת משכן יהוה׃ 30
Kuchokera pa theka la gawo la Aisraeli, utengeko cholanda chimodzi pa makumi asanu aliwonse, pa anthu, ngʼombe, abulu, nkhosa, mbuzi kapena zoweta zina. Uzipereke kwa Alevi amene ntchito yawo ndi yosamalira tenti ya Yehova.”
ויעש משה ואלעזר הכהן כאשר צוה יהוה את משה׃ 31
Ndipo Mose ndi wansembe Eliezara anachita monga Yehova analamulira Mose.
ויהי המלקוח יתר הבז אשר בזזו עם הצבא צאן שש מאות אלף ושבעים אלף וחמשת אלפים׃ 32
Zotsala pa zolanda ku nkhondo zimene ankhondowo anatenga zinali nkhosa 675,000,
ובקר שנים ושבעים אלף׃ 33
Ngʼombe 72,000,
וחמרים אחד וששים אלף׃ 34
abulu 61,000,
ונפש אדם מן הנשים אשר לא ידעו משכב זכר כל נפש שנים ושלשים אלף׃ 35
ndi atsikana omwe sanagonepo ndi mwamuna 32,000.
ותהי המחצה חלק היצאים בצבא מספר הצאן שלש מאות אלף ושלשים אלף ושבעת אלפים וחמש מאות׃ 36
Gawo la ankhondo amene anapita ku nkhondo linali: nkhosa 337,500,
ויהי המכס ליהוה מן הצאן שש מאות חמש ושבעים׃ 37
mwa zimenezi gawo la Yehova linali 675;
והבקר ששה ושלשים אלף ומכסם ליהוה שנים ושבעים׃ 38
ngʼombe zinalipo 36,000 ndipo gawo la Yehova linali 72;
וחמרים שלשים אלף וחמש מאות ומכסם ליהוה אחד וששים׃ 39
abulu analipo 30,500 ndipo gawo la Yehova linali 61;
ונפש אדם ששה עשר אלף ומכסם ליהוה שנים ושלשים נפש׃ 40
anthu analipo 16,000 ndipo gawo la Yehova linali 32.
ויתן משה את מכס תרומת יהוה לאלעזר הכהן כאשר צוה יהוה את משה׃ 41
Mose anapereka kwa wansembe Eliezara gawo limene linali loyenera kupereka kwa Yehova monga momwe Yehova analamulira Mose.
וממחצית בני ישראל אשר חצה משה מן האנשים הצבאים׃ 42
Pa gawo la Aisraeli, Mose anapatula theka limodzi kuchotsa pa zolanda ku nkhondo zonse zimene zinabwera ndi ankhondo aja.
ותהי מחצת העדה מן הצאן שלש מאות אלף ושלשים אלף שבעת אלפים וחמש מאות׃ 43
Tsono gawo la Aisraeli linali ili: nkhosa 337,500,
ובקר ששה ושלשים אלף׃ 44
ngʼombe 36,000,
וחמרים שלשים אלף וחמש מאות׃ 45
abulu 30,500,
ונפש אדם ששה עשר אלף׃ 46
anthu 16,000.
ויקח משה ממחצת בני ישראל את האחז אחד מן החמשים מן האדם ומן הבהמה ויתן אתם ללוים שמרי משמרת משכן יהוה כאשר צוה יהוה את משה׃ 47
Kuchoka pa gawo la Aisraelilo, Mose anatengapo chimodzi pa zolanda ku nkhondo makumi asanu aliwonse, anthu ndi nyama, ndipo anazipereka kwa Alevi amene ankayangʼanira tenti ya Yehova monga Yehova analamulira Mose.
ויקרבו אל משה הפקדים אשר לאלפי הצבא שרי האלפים ושרי המאות׃ 48
Pamenepo omwe ankayangʼanira magulu a ankhondo olamulira 1,000 ndi olamulira 100 anabwera kwa Mose,
ויאמרו אל משה עבדיך נשאו את ראש אנשי המלחמה אשר בידנו ולא נפקד ממנו איש׃ 49
iwo anati kwa iye, “Ife anthu anu tawerenga ankhondo amene timawalamulira. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene wasowa.
ונקרב את קרבן יהוה איש אשר מצא כלי זהב אצעדה וצמיד טבעת עגיל וכומז לכפר על נפשתינו לפני יהוה׃ 50
Ndipo tabweretsa zopereka kwa Yehova zimene munthu aliyense anapeza: ziwiya zagolide, zibangiri, zigwinjiri, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda kuti tichitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova.”
ויקח משה ואלעזר הכהן את הזהב מאתם כל כלי מעשה׃ 51
Ndipo Mose ndi wansembe Eliezara analandira kuchokera kwa atsogoleriwo golide pamodzi ndi zipangizo zonse zosula.
ויהי כל זהב התרומה אשר הרימו ליהוה ששה עשר אלף שבע מאות וחמשים שקל מאת שרי האלפים ומאת שרי המאות׃ 52
Golide yense wochokera kwa atsogoleri a 1,000 ndi atsogoleri a 100 zomwe Mose ndi Eliezara anapereka ngati mphatso kwa Yehova zinali zolemera makilogalamu 200.
אנשי הצבא בזזו איש לו׃ 53
Wankhondo aliyense anatenga zomwe analanda yekha ku nkhondo.
ויקח משה ואלעזר הכהן את הזהב מאת שרי האלפים והמאות ויבאו אתו אל אהל מועד זכרון לבני ישראל לפני יהוה׃ 54
Mose ndi Eliezara wansembe analandira golide kuchokera kwa atsogoleri a 1,000 ndi atsogoleri a 100 ndi kukamuyika mu tenti ya msonkhano ngati chikumbutso cha Aisraeli pamaso pa Yehova.

< במדבר 31 >