< במדבר 19 >

וידבר יהוה אל משה ואל אהרן לאמר׃ 1
Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni:
זאת חקת התורה אשר צוה יהוה לאמר דבר אל בני ישראל ויקחו אליך פרה אדמה תמימה אשר אין בה מום אשר לא עלה עליה על׃ 2
“Lamulo limene Yehova wapereka ndi ili: Uzani Aisraeli kuti abweretse ngʼombe yayikazi yofiira yopanda chilema chilichonse imenenso sinakhalepo pa goli.
ונתתם אתה אל אלעזר הכהן והוציא אתה אל מחוץ למחנה ושחט אתה לפניו׃ 3
Muyipereke kwa Eliezara, wansembe ndipo apite nayo kunja kwa msasa. Iphedwe iye ali pomwepo.
ולקח אלעזר הכהן מדמה באצבעו והזה אל נכח פני אהל מועד מדמה שבע פעמים׃ 4
Ndipo Eliezara wansembe atengeko ena mwa magazi a ngʼombeyo ndi chala chake ndi kuwaza kasanu nʼkawiri ku tsogolo kwa tenti ya msonkhano.
ושרף את הפרה לעיניו את ערה ואת בשרה ואת דמה על פרשה ישרף׃ 5
Wansembeyo akuona, ngʼombeyo ayiwotche ­­chikopa chake, mnofu wake, magazi ake ndi zamʼkati zake.
ולקח הכהן עץ ארז ואזוב ושני תולעת והשליך אל תוך שרפת הפרה׃ 6
Wansembe atenge mtengo wamkungudza, hisope ndi kansalu kofiira ndipo aponye zimenezo pakati pa moto umene akuwotchera ngʼombeyo.
וכבס בגדיו הכהן ורחץ בשרו במים ואחר יבוא אל המחנה וטמא הכהן עד הערב׃ 7
Zitatha izi, wansembeyo ayenera kuchapa zovala zake ndiponso asambe ndi madzi. Iye angathe kupita ku msasa, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
והשרף אתה יכבס בגדיו במים ורחץ בשרו במים וטמא עד הערב׃ 8
Munthu amene amawotcha ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
ואסף איש טהור את אפר הפרה והניח מחוץ למחנה במקום טהור והיתה לעדת בני ישראל למשמרת למי נדה חטאת הוא׃ 9
“Munthu amene ndi woyeretsedwa achotse phulusa la ngʼombeyo ndi kuliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa msasa. Aisraeli adzasunge phulusalo kuti azikaligwiritsa ntchito polithira mʼmadzi woyeretsera ndi wochotsera tchimo.
וכבס האסף את אפר הפרה את בגדיו וטמא עד הערב והיתה לבני ישראל ולגר הגר בתוכם לחקת עולם׃ 10
Munthu wochotsa phulusa la ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Ili likhale lamulo la nthawi zonse kwa Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo.
הנגע במת לכל נפש אדם וטמא שבעת ימים׃ 11
“Aliyense wokhudza mtembo wa munthu wina aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.
הוא יתחטא בו ביום השלישי וביום השביעי יטהר ואם לא יתחטא ביום השלישי וביום השביעי לא יטהר׃ 12
Adziyeretse yekha ndi madzi pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ndipo adzayeretsedwa. Koma ngati sadziyeretsa yekha pa tsiku la chitatu ndi lachisanu ndi chiwiri sadzakhala woyeretsedwa.
כל הנגע במת בנפש האדם אשר ימות ולא יתחטא את משכן יהוה טמא ונכרתה הנפש ההוא מישראל כי מי נדה לא זרק עליו טמא יהיה עוד טמאתו בו׃ 13
Aliyense amene akhudza mtembo wa munthu nʼkulephera kudziyeretsa yekha, ndiye kuti wadetsa Nyumba ya Yehova. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraeli. Iye ndi wodetsedwa chifukwa sanamuwaze madzi oyeretsa; kudetsedwa kwake kukhalabe pa iyeyo.
זאת התורה אדם כי ימות באהל כל הבא אל האהל וכל אשר באהל יטמא שבעת ימים׃ 14
“Pamene munthu wamwalira mu tenti, lamulo lomwe ligwire ntchito ndi ili: Aliyense wolowa mu tentimo ndi amene anali momwemo adzakhala odetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri,
וכל כלי פתוח אשר אין צמיד פתיל עליו טמא הוא׃ 15
ndiponso chiwiya chilichonse chopanda chivundikiro chidzakhala chodetsedwa.
וכל אשר יגע על פני השדה בחלל חרב או במת או בעצם אדם או בקבר יטמא שבעת ימים׃ 16
“Aliyense wokhudza munthu amene waphedwera kunja ndi lupanga kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe, kapena aliyense wokhudza fupa la munthu kapena manda, munthu ameneyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri.
ולקחו לטמא מעפר שרפת החטאת ונתן עליו מים חיים אל כלי׃ 17
“Za munthu wodetsedwayo: ikani phulusa lochokera ku nsembe ya chiyeretso mu mtsuko ndi kuthiramo madzi abwino.
ולקח אזוב וטבל במים איש טהור והזה על האהל ועל כל הכלים ועל הנפשות אשר היו שם ועל הנגע בעצם או בחלל או במת או בקבר׃ 18
Tsono munthu woyeretsedwa atenge hisope, amuviyike mʼmadzi ndi kuwaza tentiyo ndi zipangizo zonse, pamodzi ndi anthu anali mʼmenemo. Ayenera kuwazanso aliyense wakhudza fupa kapena, munthu wochita kuphedwa, kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe kapenanso amene wakhudza manda.
והזה הטהר על הטמא ביום השלישי וביום השביעי וחטאו ביום השביעי וכבס בגדיו ורחץ במים וטהר בערב׃ 19
Munthu woyeretsedwa ndiye awaze munthu wodetsedwayo pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri amuyeretse. Munthu amene akuyeretsedwayo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi, ndipo madzulo ake adzakhala woyeretsedwa.
ואיש אשר יטמא ולא יתחטא ונכרתה הנפש ההוא מתוך הקהל כי את מקדש יהוה טמא מי נדה לא זרק עליו טמא הוא׃ 20
Koma ngati munthu wodetsedwayo sadziyeretsa yekha, ndiye kuti ayenera kuchotsedwa pakati pa gulu chifukwa anadetsa malo wopatulika a Yehova, popeza sanawazidwe madzi oyeretsa ndiye kuti ndi wodetsedwa.
והיתה להם לחקת עולם ומזה מי הנדה יכבס בגדיו והנגע במי הנדה יטמא עד הערב׃ 21
Ili ndi lamulo lokhazikika kwa iwo. “Munthu amene amawaza madzi oyeretsawo ayenera kuchapa zovala zake ndipo yense wokhudza madzi oyeretserawo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
וכל אשר יגע בו הטמא יטמא והנפש הנגעת תטמא עד הערב׃ 22
Chilichonse chimene munthu wodetsedwayo achikhudze chidzakhala chodetsedwa ndiponso aliyense wochikhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.”

< במדבר 19 >