< במדבר 15 >
וידבר יהוה אל משה לאמר׃ | 1 |
Yehova anawuza Mose kuti,
דבר אל בני ישראל ואמרת אלהם כי תבאו אל ארץ מושבתיכם אשר אני נתן לכם׃ | 2 |
“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo,
ועשיתם אשה ליהוה עלה או זבח לפלא נדר או בנדבה או במעדיכם לעשות ריח ניחח ליהוה מן הבקר או מן הצאן׃ | 3 |
ndipo mukamadzapereka kwa Yehova, nsembe yotentha pa moto ya ngʼombe kapena nkhosa monga fungo lokoma kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena nsembe zina, nsembe yapadera chifukwa cha lumbiro kapena nsembe yoperekedwa mwaufulu kapenanso yoperekedwa pa chikondwerero,
והקריב המקריב קרבנו ליהוה מנחה סלת עשרון בלול ברבעית ההין שמן׃ | 4 |
munthu amene akubweretsa zopereka zake, azikapereka kwa Yehova chopereka chachakudya cholemera kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta wokwana lita imodzi.
ויין לנסך רביעית ההין תעשה על העלה או לזבח לכבש האחד׃ | 5 |
Pamodzi ndi mwana wankhosa aliyense wa nsembe yopsereza kapena nsembe ina, muzikakonzanso lita imodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.’”
או לאיל תעשה מנחה סלת שני עשרנים בלולה בשמן שלשית ההין׃ | 6 |
“Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, muzikakonzanso chopereka cha chakudya cholemera makilogalamu awiri a ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita imodzi ndi theka,
ויין לנסך שלשית ההין תקריב ריח ניחח ליהוה׃ | 7 |
ndi vinyo wokwanira lita imodzi ndi theka ngati chopereka cha chakumwa. Muzikapereka monga nsembe yopereka fungo lokoma kwa Yehova.
וכי תעשה בן בקר עלה או זבח לפלא נדר או שלמים ליהוה׃ | 8 |
“‘Pamene mukukonza mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse: ya lumbiro lapadera kapena nsembe yachiyanjano kwa Yehova,
והקריב על בן הבקר מנחה סלת שלשה עשרנים בלול בשמן חצי ההין׃ | 9 |
pamodzi ndi mwana wangʼombe wamwamunayo muzibweretsa nsembe yachakudya yolemera makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta okwana malita awiri.
ויין תקריב לנסך חצי ההין אשה ריח ניחח ליהוה׃ | 10 |
Komanso muzibweretsa vinyo wokwanira malita awiri monga chopereka chachakumwa. Imeneyi idzakhala chopereka chotentha pa moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova.
ככה יעשה לשור האחד או לאיל האחד או לשה בכבשים או בעזים׃ | 11 |
Ngʼombe yayimuna iliyonse kapena nkhosa yayimuna iliyonse, mwana wankhosa aliyense kapena mbuzi yayingʼono, zizikonzedwa motere.
כמספר אשר תעשו ככה תעשו לאחד כמספרם׃ | 12 |
Ngakhale zingachuluke chotani, chitani izi kwa iliyonse ya nyamazo.
כל האזרח יעשה ככה את אלה להקריב אשה ריח ניחח ליהוה׃ | 13 |
“‘Mbadwa iliyonse ya mu Israeli izichita zimenezi pamene ibweretsa nsembe yotentha pa moto kuti ikhale fungo lokoma kwa Yehova.
וכי יגור אתכם גר או אשר בתוככם לדרתיכם ועשה אשה ריח ניחח ליהוה כאשר תעשו כן יעשה׃ | 14 |
Ku mibado yanu yonse ya mʼtsogolo, pamene mlendo kapena wina aliyense wokhala pakati panu apereka chopereka chotentha pa moto kuti chikhale fungo lokoma kwa Yehova, azichita mofanana ndi momwe inu mumachitira.
הקהל חקה אחת לכם ולגר הגר חקת עולם לדרתיכם ככם כגר יהיה לפני יהוה׃ | 15 |
Gulu lonse likhale ndi malamulo ofanana a inu kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya kwa mibado imene ikubwera. Inuyo ndi mlendo mudzakhala wofanana pamaso pa Yehova.
תורה אחת ומשפט אחד יהיה לכם ולגר הגר אתכם׃ | 16 |
Mudzakhale ndi malamulo ndi miyambo yofanana, inuyo ndi mlendo wokhala pakati panu.’”
וידבר יהוה אל משה לאמר׃ | 17 |
Yehova anawuza Mose kuti,
דבר אל בני ישראל ואמרת אלהם בבאכם אל הארץ אשר אני מביא אתכם שמה׃ | 18 |
“Yankhula ndi Aisraeli ndipo unene kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukutengeraniko
והיה באכלכם מלחם הארץ תרימו תרומה ליהוה׃ | 19 |
ndipo mukakadya chakudya cha mʼdzikolo, mukapereke gawo lina kwa Yehova monga chopereka.
ראשית ערסתכם חלה תרימו תרומה כתרומת גרן כן תרימו אתה׃ | 20 |
Pa buledi wanu woyamba, mukapereke mmodzi monga nsembe, ngati chopereka chochokera ku malo wopunthira tirigu.
מראשית ערסתיכם תתנו ליהוה תרומה לדרתיכם׃ | 21 |
Pa mibado yanu yonse muzidzapereka chopereka ichi kwa Yehova kuchokera ku zakudya zanu zoyamba za mʼnthaka.
וכי תשגו ולא תעשו את כל המצות האלה אשר דבר יהוה אל משה׃ | 22 |
“‘Ndipo ngati muchimwa mosadziwa posasunga ena mwa malamulo awa amene Yehova wapereka kwa Mose,
את כל אשר צוה יהוה אליכם ביד משה מן היום אשר צוה יהוה והלאה לדרתיכם׃ | 23 |
lina lililonse mwa malamulo a Yehova amene wapereka kwa inu kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Yehova anawapereka mpaka mibado ya mʼtsogolo,
והיה אם מעיני העדה נעשתה לשגגה ועשו כל העדה פר בן בקר אחד לעלה לריח ניחח ליהוה ומנחתו ונסכו כמשפט ושעיר עזים אחד לחטת׃ | 24 |
ndipo ngati zimenezi zachitika osati mwadala ndipo gulu lonse silinadziwe, zikatero gulu lonselo lipereke mwana wangʼombe wamwamuna monga nsembe yopsereza kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova pamodzinso ndi chopereka chachakudya ndi chopereka cha chakumwa ndi mbuzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo potsata zimene zinalamulidwa.
וכפר הכהן על כל עדת בני ישראל ונסלח להם כי שגגה הוא והם הביאו את קרבנם אשה ליהוה וחטאתם לפני יהוה על שגגתם׃ | 25 |
Wansembe apereke nsembe yopepesera machimo a gulu lonse la Aisraeli, ndipo adzakhululukidwa, pakuti linali tchimo lochita mosadziwa. Ndipo chifukwa cha tchimo lawolo, abweretse kwa Yehova nsembe yotentha pa moto ndi nsembe yopepesera machimo.
ונסלח לכל עדת בני ישראל ולגר הגר בתוכם כי לכל העם בשגגה׃ | 26 |
Gulu lonse la Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo adzakhululukidwa chifukwa anthu onsewo anachimwa mosadziwa.
ואם נפש אחת תחטא בשגגה והקריבה עז בת שנתה לחטאת׃ | 27 |
“‘Koma ngati munthu mmodzi achimwa mosadziwa, ayenera kubweretsa mbuzi yayikazi ya chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo.
וכפר הכהן על הנפש השגגת בחטאה בשגגה לפני יהוה לכפר עליו ונסלח לו׃ | 28 |
Wansembe apereke nsembe yopepesera machimowo pamaso pa Yehova chifukwa cha munthu yemwe anachimwa mosadziwayo. Nsembe yopepesera tchimo lakelo ikaperekedwa, munthuyo adzakhululukidwa.
האזרח בבני ישראל ולגר הגר בתוכם תורה אחת יהיה לכם לעשה בשגגה׃ | 29 |
Lamulo lomweli ligwiritsidwe ntchito kwa aliyense wochimwa mosadziwa, kaya ndi mbadwa ya mu Israeli kapena mlendo.
והנפש אשר תעשה ביד רמה מן האזרח ומן הגר את יהוה הוא מגדף ונכרתה הנפש ההוא מקרב עמה׃ | 30 |
“‘Koma aliyense amene achimwa mwadala, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, nachitira chipongwe Yehova, ameneyo achotsedwe ndithu pakati pa anthu ake.
כי דבר יהוה בזה ואת מצותו הפר הכרת תכרת הנפש ההוא עונה בה׃ | 31 |
Popeza wanyoza mawu a Yehova ndi kuphwanya malamulo ake. Munthu ameneyo achotsedwe ndithu, kuchimwa kwake kudzakhala pa iyeyo.’”
ויהיו בני ישראל במדבר וימצאו איש מקשש עצים ביום השבת׃ | 32 |
Aisraeli ali mʼchipululu, munthu wina anapezeka akutola nkhuni tsiku la Sabata.
ויקריבו אתו המצאים אתו מקשש עצים אל משה ואל אהרן ואל כל העדה׃ | 33 |
Amene anamupeza akutola nkhunizo anabwera naye kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa gulu lonse
ויניחו אתו במשמר כי לא פרש מה יעשה לו׃ | 34 |
ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa sankadziwa choti achite naye.
ויאמר יהוה אל משה מות יומת האיש רגום אתו באבנים כל העדה מחוץ למחנה׃ | 35 |
Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Munthu ameneyu ayenera kuphedwa. Gulu lonse liyenera kumugenda ndi miyala kunja kwa msasa.”
ויציאו אתו כל העדה אל מחוץ למחנה וירגמו אתו באבנים וימת כאשר צוה יהוה את משה׃ | 36 |
Choncho gululo linamutengera kunja kwa msasa ndi kumupha pomugenda ndi miyala, monga momwe Yehova analamulira Mose.
ויאמר יהוה אל משה לאמר׃ | 37 |
Yehova anawuza Mose kuti,
דבר אל בני ישראל ואמרת אלהם ועשו להם ציצת על כנפי בגדיהם לדרתם ונתנו על ציצת הכנף פתיל תכלת׃ | 38 |
“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pa mibado yanu yonse muzisokerera mphonje pa ngodya za zovala zanu ndipo pa ngodya ya mphonje iliyonse azisokererapo chingwe chobiriwira.
והיה לכם לציצת וראיתם אתו וזכרתם את כל מצות יהוה ועשיתם אתם ולא תתרו אחרי לבבכם ואחרי עיניכם אשר אתם זנים אחריהם׃ | 39 |
Mudzakhala ndi mphonje zimenezi kuti mukaziona muzikakumbukira malamulo onse a Yehova ndi kuwamvera kuti musamatsatenso zilakolako za mʼmitima mwanu ndi za maso anu.
למען תזכרו ועשיתם את כל מצותי והייתם קדשים לאלהיכם׃ | 40 |
Motero mudzakumbukira kumvera malamulo anga ndipo mudzakhala opatulikira a Mulungu wanu.
אני יהוה אלהיכם אשר הוצאתי אתכם מארץ מצרים להיות לכם לאלהים אני יהוה אלהיכם׃ | 41 |
Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”