< נחמיה 4 >
ויהי כאשר שמע סנבלט כי אנחנו בונים את החומה ויחר לו ויכעס הרבה וילעג על היהודים׃ | 1 |
Sanibalati atamva kuti tikumanganso khoma anapsa mtima nayamba kuseka ndi kunyogodola Ayuda kwambiri.
ויאמר לפני אחיו וחיל שמרון ויאמר מה היהודים האמללים עשים היעזבו להם היזבחו היכלו ביום היחיו את האבנים מערמות העפר והמה שרופות׃ | 2 |
Ndipo anayankhula pamaso pa abale ake ndi asilikali a Samariya kuti, “Kodi Ayuda ofowokawa akuchita chiyani? Kodi iwo nʼkumanganso khoma? Kodi adzaperekanso nsembe? Kodi adzatsiriza ntchitoyi tsiku limodzi? Kodi adzachita kutenga miyala yakale ija ndi mmene inapseramo?”
וטוביה העמני אצלו ויאמר גם אשר הם בונים אם יעלה שועל ופרץ חומת אבניהם׃ | 3 |
Tobiya wa ku Amoni, amene anali naye anati, “Chimene akumangacho ngati nkhandwe itakwerapo, itha kugwetsa khoma lawolo!”
שמע אלהינו כי היינו בוזה והשב חרפתם אל ראשם ותנם לבזה בארץ שביה׃ | 4 |
Tsono ndinayamba kupemphera kuti, “Timvereni, Inu Mulungu wathu, mmene akutinyozera. Mulole kuti mawu awo onyoza awabwerere, ndipo atengedwe ukapolo ku dziko lachilendo.
ואל תכס על עונם וחטאתם מלפניך אל תמחה כי הכעיסו לנגד הבונים׃ | 5 |
Musawakhululukire mphulupulu zawo kapena kufafaniza machimo awo pamaso panu popeza aputa ukali wanu pamaso pa anthu omanga khoma.”
ונבנה את החומה ותקשר כל החומה עד חציה ויהי לב לעם לעשות׃ | 6 |
Choncho ife tinamangabe khomalo kufikira lonse litafika theka la msinkhu wake, chifukwa chakuti anthu anagwira ntchitoyo ndi mtima wawo wonse.
ויהי כאשר שמע סנבלט וטוביה והערבים והעמנים והאשדודים כי עלתה ארוכה לחמות ירושלם כי החלו הפרצים להסתם ויחר להם מאד׃ | 7 |
Koma pamene Sanibalati, Tobiya, Aarabu, Aamoni ndi anthu a ku Asidodi anamva kuti ntchito yokonzanso makoma a Yerusalemu ikupitirirabe ndipo kuti mipata ikutsekedwa, anapsa mtima kwambiri.
ויקשרו כלם יחדו לבוא להלחם בירושלם ולעשות לו תועה׃ | 8 |
Tsono onse anapangana za chiwembu kuti abwere ndi kudzathira nkhondo anthu a ku Yerusalemu ndi kuyambitsa mapokoso pakati pawo.
ונתפלל אל אלהינו ונעמיד משמר עליהם יומם ולילה מפניהם׃ | 9 |
Koma ife tinapemphera kwa Mulungu wathu ndipo tinayika alonda otiteteza kwa adaniwo usiku ndi usana.
ויאמר יהודה כשל כח הסבל והעפר הרבה ואנחנו לא נוכל לבנות בחומה׃ | 10 |
Pa nthawi yomweyi anthu a ku Yuda anati, “Mphamvu za anthu onyamula zinyalala zikutha ndipo pali zinyalala zambiri. Choncho ife sititha kumanga khomali.”
ויאמרו צרינו לא ידעו ולא יראו עד אשר נבוא אל תוכם והרגנום והשבתנו את המלאכה׃ | 11 |
Adani athunso anati, “Iwo asanadziwe izi, kapena kutiona, tidzakhala tili pakati pawo ndipo tidzawapha ndi kuyimitsa ntchitoyo.”
ויהי כאשר באו היהודים הישבים אצלם ויאמרו לנו עשר פעמים מכל המקמות אשר תשובו עלינו׃ | 12 |
Ndipo Ayuda amene ankhala pafupi ndi adani athuwo anabwera kakhumi konse kuchokera konse kumene ankakhala kudzatiwuza kuti tibwereko ku ntchito.
ואעמיד מתחתיות למקום מאחרי לחומה בצחחיים ואעמיד את העם למשפחות עם חרבתיהם רמחיהם וקשתתיהם׃ | 13 |
Choncho kumbuyo kwa khoma, cha mʼmunsi mwake komanso malo amene anali asanathe ndinayikamo anthu mʼmabanja atatenga malupanga, mikondo ndi mauta awo.
וארא ואקום ואמר אל החרים ואל הסגנים ואל יתר העם אל תיראו מפניהם את אדני הגדול והנורא זכרו והלחמו על אחיכם בניכם ובנתיכם נשיכם ובתיכם׃ | 14 |
Popeza anthu ankachita mantha, tsono ndinawawuza anthu olemekezeka, akuluakulu ndiponso anthu onse kuti, “Musawaope. Kumbukirani kuti Ambuye ndi wamkulu ndipo ndi woopsa. Choncho menyerani nkhondo abale anu, ana aamuna ndi aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.”
ויהי כאשר שמעו אויבינו כי נודע לנו ויפר האלהים את עצתם ונשוב כלנו אל החומה איש אל מלאכתו׃ | 15 |
Adani athu atamva kuti ife tadziwa za chiwembu chawo, anadziwanso kuti Yehova walepheretsa zimene ankafuna kutichita. Choncho tinabwerera aliyense ku ntchito yake yomanga khoma.
ויהי מן היום ההוא חצי נערי עשים במלאכה וחצים מחזיקים והרמחים המגנים והקשתות והשרינים והשרים אחרי כל בית יהודה׃ | 16 |
Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo mwake, theka la antchito anga linkagwira ntchito, pamene theka linalo limatenga mikondo, zishango, mauta ndi kuvala malaya azitsulo. Akuluakulu ankalimbikitsa Ayuda onse
הבונים בחומה והנשאים בסבל עמשים באחת ידו עשה במלאכה ואחת מחזקת השלח׃ | 17 |
amene ankamanga khoma. Anthu onyamula zinyalala aja ankagwira ntchito ndi dzanja limodzi, dzanja linali atanyamula chida chankhondo.
והבונים איש חרבו אסורים על מתניו ובונים והתוקע בשופר אצלי׃ | 18 |
Mʼmisiri aliyense ankamangirira lupanga lake mʼchiwuno mwake akamagwira ntchito. Koma munthu woyimba lipenga anali pambali panga nthawi zonse.
ואמר אל החרים ואל הסגנים ואל יתר העם המלאכה הרבה ורחבה ואנחנו נפרדים על החומה רחוקים איש מאחיו׃ | 19 |
Ndipo ine ndinati kwa anthu olemekezeka ndi anthu ena onse, “Ntchitoyi ndi yayikulu ndipo ili padera lalikulu ndipo ifeyo takhala motayanatayana kwambiri pa khoma.
במקום אשר תשמעו את קול השופר שמה תקבצו אלינו אלהינו ילחם לנו׃ | 20 |
Tsono kulikonse kumene muliko, mukamva kulira kwa lipenga bwerani mudzasonkhane kumene kuli ine kuno. Mulungu wathu adzatimenyera nkhondo.”
ואנחנו עשים במלאכה וחצים מחזיקים ברמחים מעלות השחר עד צאת הכוכבים׃ | 21 |
Choncho enafe tinapitiriza kugwira ntchito, pamene theka lina linkanyamula mikondo kuyambira mʼbandakucha mpaka nyenyezi zitaoneka.
גם בעת ההיא אמרתי לעם איש ונערו ילינו בתוך ירושלם והיו לנו הלילה משמר והיום מלאכה׃ | 22 |
Pa nthawi imeneyo ndinawuzanso anthuwo kuti, “Aliyense pamodzi ndi wantchito wake agone mu Yerusalemu kuti tikhale ndi otilondera usiku ndi kuti masana tizigwira ntchito.”
ואין אני ואחי ונערי ואנשי המשמר אשר אחרי אין אנחנו פשטים בגדינו איש שלחו המים׃ | 23 |
Choncho ine, anzanga, antchito anga, ndi anthu otiteteza amene ankanditsata panalibe ndi mmodzi yemwe anavula zovala zake pogona. Aliyense anasunga chida chake chankhondo pambali pake.