< מלאכי 4 >
כי הנה היום בא בער כתנור והיו כל זדים וכל עשה רשעה קש ולהט אתם היום הבא אמר יהוה צבאות אשר לא יעזב להם שרש וענף׃ | 1 |
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndithu tsiku likubwera; lidzayaka ngati ngʼanjo. Anthu onse odzikuza, ndi aliyense ochita zoyipa adzapsa ngati chiputu, ndipo pa tsiku limene likubweralo adzapserera ndi moto. Sipadzatsalira muzu kapena nthambi.
וזרחה לכם יראי שמי שמש צדקה ומרפא בכנפיה ויצאתם ופשתם כעגלי מרבק׃ | 2 |
Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola.
ועסותם רשעים כי יהיו אפר תחת כפות רגליכם ביום אשר אני עשה אמר יהוה צבאות׃ | 3 |
Tsiku limenelo inu mudzapondereza anthu oyipa; adzakhala phulusa ku mapazi anu pa tsiku limene Ine ndidzachite zinthu zimenezi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
זכרו תורת משה עבדי אשר צויתי אותו בחרב על כל ישראל חקים ומשפטים׃ | 4 |
Kumbukirani zophunzitsa za mtumiki wanga Mose, malamulo ndi malangizo amene ndinamupatsa pa Horebu kuti awuze Aisraeli onse.
הנה אנכי שלח לכם את אליה הנביא לפני בוא יום יהוה הגדול והנורא׃ | 5 |
“Taonani, ndidzakutumizirani mneneri Eliya lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.
והשיב לב אבות על בנים ולב בנים על אבותם פן אבוא והכיתי את הארץ חרם׃ | 6 |
Iye adzabweza mitima ya makolo kwa ana awo, ndi mitima ya ana kwa makolo awo. Kupanda kutero ndidzabwera kudzakantha dziko lanu ndi temberero.”