< מלאכי 1 >
משא דבר יהוה אל ישראל ביד מלאכי׃ | 1 |
Uthenga: Mawu a Yehova kwa Israeli kudzera mwa Malaki.
אהבתי אתכם אמר יהוה ואמרתם במה אהבתנו הלוא אח עשו ליעקב נאם יהוה ואהב את יעקב׃ | 2 |
Yehova akuti, “Ine ndakukondani. Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi mwatikonda motani?’” Yehova akuti, “Kodi Esau sanali mʼbale wake wa Yakobo? Komatu Ine ndinakonda Yakobo,
ואת עשו שנאתי ואשים את הריו שממה ואת נחלתו לתנות מדבר׃ | 3 |
koma ndinamuda Esau, ndipo dziko lake lamapiri ndalisandutsa chipululu ndipo cholowa chake ndasiyira ankhandwe a mʼchipululu.”
כי תאמר אדום רששנו ונשוב ונבנה חרבות כה אמר יהוה צבאות המה יבנו ואני אהרוס וקראו להם גבול רשעה והעם אשר זעם יהוה עד עולם׃ | 4 |
Mwina Edomu nʼkunena kuti, “Ngakhale taphwanyidwa, tidzamanganso mʼmabwinja.” Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Iwo angathe kumanganso, koma Ine ndidzazigwetsanso. Iwo adzatchedwa dziko loyipa, la anthu amene Yehova wayipidwa nawo mpaka muyaya.
ועיניכם תראינה ואתם תאמרו יגדל יהוה מעל לגבול ישראל׃ | 5 |
Inu mudzaziona zimenezi ndi maso anu ndipo mudzati, ‘Yehova ndi Wamkulu, ukulu wake umafika ngakhale kunja kwa malire a Israeli!’
בן יכבד אב ועבד אדניו ואם אב אני איה כבודי ואם אדונים אני איה מוראי אמר יהוה צבאות לכם הכהנים בוזי שמי ואמרתם במה בזינו את שמך׃ | 6 |
“Mwana amalemekeza abambo ake, ndipo wantchito amaopa abwana ake. Ngati Ine ndine abambo anu, ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiopa kuli kuti?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndinu, inu ansembe, amene mumanyoza dzina langa. “Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi timanyoza dzina lanu bwanji?’
מגישים על מזבחי לחם מגאל ואמרתם במה גאלנוך באמרכם שלחן יהוה נבזה הוא׃ | 7 |
“Inu mwanyoza dzina langa popereka chakudya chodetsedwa pa guwa langa lansembe. “Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi ife takunyozani bwanji?’ “Mwandinyoza ponena kuti tebulo la Yehova ndi lonyozeka.
וכי תגשון עור לזבח אין רע וכי תגישו פסח וחלה אין רע הקריבהו נא לפחתך הירצך או הישא פניך אמר יהוה צבאות׃ | 8 |
Mukamapereka nsembe nyama zosaona, kodi sicholakwa? Mukamapereka nsembe nyama zachilema kapena zodwala, kodi sicholakwa? Kayeseni kuzipereka kwa bwanamkubwa wanu! Kodi akasangalatsidwa nanu? Kodi akazilandira? Akutero Yehova Wamphamvuzonse.
ועתה חלו נא פני אל ויחננו מידכם היתה זאת הישא מכם פנים אמר יהוה צבאות׃ | 9 |
“Tsopano tayesani kupempha Mulungu kuti akuchitireni chifundo. Kodi ndi zopereka zotere mʼmanja mwanu, Iye angakulandireni?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse.
מי גם בכם ויסגר דלתים ולא תאירו מזבחי חנם אין לי חפץ בכם אמר יהוה צבאות ומנחה לא ארצה מידכם׃ | 10 |
“Ndikulakalaka mmodzi wa inu akanatseka zitseko za Nyumba ya Mulungu, kuti musayatsemo moto pachabe pa guwa langa lansembe! Ine sindikukondwera nanu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse, “ndipo Ine sindidzalandira zopereka za mʼmanja mwanu.
כי ממזרח שמש ועד מבואו גדול שמי בגוים ובכל מקום מקטר מגש לשמי ומנחה טהורה כי גדול שמי בגוים אמר יהוה צבאות׃ | 11 |
Dzina langa lidzalemekezedwa pakati pa mitundu ya anthu, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo. Mʼmalo monse adzapereka nsembe zofukiza ndi zopereka zangwiro mʼdzina langa, chifukwa dzina langa lidzakhala lalikulu pakati pa mitundu ya anthu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
ואתם מחללים אותו באמרכם שלחן אדני מגאל הוא וניבו נבזה אכלו׃ | 12 |
“Koma inu mumalinyoza ponena kuti tebulo la Ambuye, ‘ndi lodetsedwa,’ ndipo chakudya chake, ‘nʼchonyozeka!’
ואמרתם הנה מתלאה והפחתם אותו אמר יהוה צבאות והבאתם גזול ואת הפסח ואת החולה והבאתם את המנחה הארצה אותה מידכם אמר יהוה׃ | 13 |
Ndipo inu mumati, ‘Ndi zotopetsa zimenezi!’ Ndipo mumandinyogodola Ine,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Pamene inu mubweretsa nyama zakuba, zolumala kapena zodwala ndi kupereka nsembe, kodi Ine ndizilandire kuchokera mʼmanja mwanu?” Akutero Yehova.
וארור נוכל ויש בעדרו זכר ונדר וזבח משחת לאדני כי מלך גדול אני אמר יהוה צבאות ושמי נורא בגוים׃ | 14 |
“Atembereredwe munthu wachinyengo amene ali ndi nyama yayimuna yabwino mʼgulu la ziweto zake ndipo analumbira kuyipereka, koma mʼmalo mwake nʼkupereka nsembe kwa Ambuye nyama yosayenera. Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakuti ndine mfumu yayikulu, dzina langa liyenera kuopedwa pakati pa anthu a mitundu yonse.’”