< ויקרא 6 >
וידבר יהוה אל משה לאמר׃ | 1 |
Yehova anawuza Mose kuti,
נפש כי תחטא ומעלה מעל ביהוה וכחש בעמיתו בפקדון או בתשומת יד או בגזל או עשק את עמיתו׃ | 2 |
“Ngati munthu wina aliyense achimwa, nachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova chifukwa cha kunyenga mnzake pokana kumubwezera zimene anamusungitsa, kapena kumubera kapenanso kumulanda,
או מצא אבדה וכחש בה ונשבע על שקר על אחת מכל אשר יעשה האדם לחטא בהנה׃ | 3 |
kapena ndi kunama kuti sanatole chinthu chimene chinatayika, kapena kulumbira mwachinyengo pa chinthu chilichonse chimene munthu akachita amachimwa nacho,
והיה כי יחטא ואשם והשיב את הגזלה אשר גזל או את העשק אשר עשק או את הפקדון אשר הפקד אתו או את האבדה אשר מצא׃ | 4 |
ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kubweza zimene anabazo, zimene analanda mwachinyengozo, zimene anamusungitsazo, zimene anatolazo
או מכל אשר ישבע עליו לשקר ושלם אתו בראשו וחמשתיו יסף עליו לאשר הוא לו יתננו ביום אשמתו׃ | 5 |
kapena zimene analumbira monyengazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, iye ayenera kumubwezera mwini wake zinthu zonsezi ndi kuwonjezerapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse.
ואת אשמו יביא ליהוה איל תמים מן הצאן בערכך לאשם אל הכהן׃ | 6 |
Pambuyo pake apereke kwa Yehova nsembe yopalamula. Nsembe yake ikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake wogwirizana ndi nsembe yopepesera machimo.
וכפר עליו הכהן לפני יהוה ונסלח לו על אחת מכל אשר יעשה לאשמה בה׃ | 7 |
Kenaka wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa chilichonse chomwe anachita kuti akhale wopalamula.”
וידבר יהוה אל משה לאמר׃ | 8 |
Yehova anawuza Mose kuti,
צו את אהרן ואת בניו לאמר זאת תורת העלה הוא העלה על מוקדה על המזבח כל הלילה עד הבקר ואש המזבח תוקד בו׃ | 9 |
“Lamula Aaroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopsereza ndi ili: Nsembe yopserezayo izikhala pa moto pa guwa usiku wonse mpaka mmawa, ndipo moto wa paguwapo uzikhala ukuyaka nthawi zonse.
ולבש הכהן מדו בד ומכנסי בד ילבש על בשרו והרים את הדשן אשר תאכל האש את העלה על המזבח ושמו אצל המזבח׃ | 10 |
Tsono wansembe avale mkanjo wake wa nsalu yofewa ndi yosalala. Mʼkati avalenso kabudula wofewa, wosalala. Pambuyo pake atenge phulusa la nyama imene yatenthedwa pa guwa lansembe paja ndi kulithira pambali pa guwa lomwelo.
ופשט את בגדיו ולבש בגדים אחרים והוציא את הדשן אל מחוץ למחנה אל מקום טהור׃ | 11 |
Akatero avule zovala zakezo ndi kuvala zovala zina. Kenaka atulutse phulusalo ndi kukaliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa chithando.
והאש על המזבח תוקד בו לא תכבה ובער עליה הכהן עצים בבקר בבקר וערך עליה העלה והקטיר עליה חלבי השלמים׃ | 12 |
Moto wa pa guwa uzikhala ukuyaka nthawi zonse, usamazime. Mmawa uliwonse wansembe aziwonjezerapo nkhuni pa motopo ndi kukonza nsembe yopsereza, ndi kutentha mafuta a nsembe yachiyanjano pamenepo.
אש תמיד תוקד על המזבח לא תכבה׃ | 13 |
Moto uzikhala ukuyaka pa guwa nthawi zonse ndipo usazimepo.
וזאת תורת המנחה הקרב אתה בני אהרן לפני יהוה אל פני המזבח׃ | 14 |
“‘Lamulo la nsembe yachakudya ndi ili: ana a Aaroni azibwera nayo nsembeyo pamaso pa Yehova, patsogolo pa guwa.
והרים ממנו בקמצו מסלת המנחה ומשמנה ואת כל הלבנה אשר על המנחה והקטיר המזבח ריח ניחח אזכרתה ליהוה׃ | 15 |
Wansembe mmodzi atapeko dzanja limodzi la ufa wosalala wa nsembe yachakudya ija kuti ukhala ufa wachikumbutso ndi mafuta pamodzi ndi lubani yense amene ali pa nsembe ya chakudyacho, ndipo azitenthe pa guwa kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse kuti zikhale nsembe ya fungo lokomera Yehova.
והנותרת ממנה יאכלו אהרן ובניו מצות תאכל במקום קדש בחצר אהל מועד יאכלוה׃ | 16 |
Aaroni ndi ana ake azidya zimene zatsala koma azidya zopanda yisiti ku malo wopatulika, ku bwalo la tenti ya msonkhano.
לא תאפה חמץ חלקם נתתי אתה מאשי קדש קדשים הוא כחטאת וכאשם׃ | 17 |
Poziphika asathire yisiti. Ndawapatsa zotsalazo kuti zikhale gawo lawo la nsembe zanga zopsereza. Zonsezi ndi zopatulika kwambiri monga nsembe yopepesera tchimo ndiponso nsembe yopepesera machimo.
כל זכר בבני אהרן יאכלנה חק עולם לדרתיכם מאשי יהוה כל אשר יגע בהם יקדש׃ | 18 |
Mwana aliyense wamwamuna wa Aaroni azidyako za nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova. Ndi gawo lake lokhazikika la chopereka chopsereza kwa Yehova pa mibado yanu yonse. Chilichonse chimene chidzakhudza nsembezo chidzakhala chopatulika.’”
וידבר יהוה אל משה לאמר׃ | 19 |
Yehova anawuzanso Mose kuti,
זה קרבן אהרן ובניו אשר יקריבו ליהוה ביום המשח אתו עשירת האפה סלת מנחה תמיד מחציתה בבקר ומחציתה בערב׃ | 20 |
“Nsembe imene Aaroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Yehova pa tsiku limene wansembe akudzozedwa ndi iyi: ufa wosalala kilogalamu imodzi ngati chopereka chachakudya cha nthawi zonse. Azipereka theka limodzi mmawa ndipo theka linalo madzulo.
על מחבת בשמן תעשה מרבכת תביאנה תפיני מנחת פתים תקריב ריח ניחח ליהוה׃ | 21 |
Ipangidwe ndi mafuta pa chiwaya ndipo ubwere nayo ili yosakaniza bwino, yophikidwa mitandamitanda monga amachitira ndi nsembe yachakudya. Iphikidwe moti itulutse fungo lokomera Yehova.
והכהן המשיח תחתיו מבניו יעשה אתה חק עולם ליהוה כליל תקטר׃ | 22 |
Mwana wa fuko la Aaroni amene adzadzozedwe kukhala wansembe kulowa mʼmalo mwa Aaroni ndiye amene azidzakonza ndi kupereka nsembeyi kwa Yehova nthawi zonse monga kunalembedwera.
וכל מנחת כהן כליל תהיה לא תאכל׃ | 23 |
Nsembe iliyonse yachakudya ya wansembe izitenthedwa kwathunthu, isamadyedwe.”
וידבר יהוה אל משה לאמר׃ | 24 |
Yehova anawuza Mose kuti
דבר אל אהרן ואל בניו לאמר זאת תורת החטאת במקום אשר תשחט העלה תשחט החטאת לפני יהוה קדש קדשים הוא׃ | 25 |
“Uza Aaroni ndi ana ake kuti, ‘Malamulo a nsembe ya tchimo ndi awa: Nsembeyi iziphedwa pamaso pa Yehova pa malo pamene mumaphera nsembe yopsereza popeza ndi nsembe yopatulika.
הכהן המחטא אתה יאכלנה במקום קדש תאכל בחצר אהל מועד׃ | 26 |
Wansembe amene apereke nsembeyi adyere ku malo wopatulika ndiye kuti mʼbwalo la tenti ya msonkhano.
כל אשר יגע בבשרה יקדש ואשר יזה מדמה על הבגד אשר יזה עליה תכבס במקום קדש׃ | 27 |
Chilichonse chimene chidzakhudza nsembeyo chidzakhala chopatulika, ndipo ngati magazi ake agwera pa chovala, muchape chovalacho pa malo opatulika.
וכלי חרש אשר תבשל בו ישבר ואם בכלי נחשת בשלה ומרק ושטף במים׃ | 28 |
Mʼphika wadothi umene aphikira nyamayo auphwanye. Koma ngati yaphikidwa mu mʼphika wa mkuwa, awukweche ndi kuwutsukuluza ndi madzi.
כל זכר בכהנים יאכל אתה קדש קדשים הוא׃ | 29 |
Munthu wamwamuna aliyense wa mʼbanja la wansembe angathe kuyidya popeza nsembeyi ndi yopatulika kwambiri.
וכל חטאת אשר יובא מדמה אל אהל מועד לכפר בקדש לא תאכל באש תשרף׃ | 30 |
Koma nsembe yopepesera tchimo imene magazi ake amabwera nawo mu tenti ya msonkhano kudzachita mwambo wopepesera tchimo ku malo opatulika isadyedwe, mʼmalo mwake itenthedwe.’”