< ויקרא 25 >
וידבר יהוה אל משה בהר סיני לאמר׃ | 1 |
Yehova anawuza Mose pa phiri la Sinai kuti,
דבר אל בני ישראל ואמרת אלהם כי תבאו אל הארץ אשר אני נתן לכם ושבתה הארץ שבת ליהוה׃ | 2 |
“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukadzalowa mʼdziko limene ndikukupatsani, nthakayo iyenera kumakasunga Sabata la Yehova.
שש שנים תזרע שדך ושש שנים תזמר כרמך ואספת את תבואתה׃ | 3 |
Pa zaka zisanu ndi chimodzi muzikalima minda yanu, ndipo kwa zaka zisanu ndi chimodzi muzikasadza mitengo yanu ya mpesa ndi kuthyola zipatso zake.
ובשנה השביעת שבת שבתון יהיה לארץ שבת ליהוה שדך לא תזרע וכרמך לא תזמר׃ | 4 |
Koma chaka chachisanu ndi chiwiri ndi chaka choti nthaka ipume, chaka cha Sabata la Yehova. Musalime mʼminda yanu kapena kusadza mitengo yanu ya mpesa.
את ספיח קצירך לא תקצור ואת ענבי נזירך לא תבצר שנת שבתון יהיה לארץ׃ | 5 |
Musakolole zimene zinamera zokha mʼmunda mwanu. Musakakolole kapena kuthyola mphesa za mʼmitengo imene simunasadze. Chaka chimenechi nʼchoti nthaka ipumule.
והיתה שבת הארץ לכם לאכלה לך ולעבדך ולאמתך ולשכירך ולתושבך הגרים עמך׃ | 6 |
Chaka chimene nthakayo ipumula mudzakhala ndi chakudya chokwanira inuyo, akapolo anu aamuna ndi aakazi, antchito ndi alendo okhala nanu.
ולבהמתך ולחיה אשר בארצך תהיה כל תבואתה לאכל׃ | 7 |
Ziweto zanu pamodzi ndi nyama za mʼdziko lanu zizidzadya zipatso za mʼnthaka.
וספרת לך שבע שבתת שנים שבע שנים שבע פעמים והיו לך ימי שבע שבתת השנים תשע וארבעים שנה׃ | 8 |
“‘Muzichotsera Masabata asanu ndi awiri a zaka, ndi kuchulukitsa zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawirinso kuti Masabata asanu ndi awiri a zakawo akwane zaka 49.
והעברת שופר תרועה בחדש השבעי בעשור לחדש ביום הכפרים תעבירו שופר בכל ארצכם׃ | 9 |
Ndipo pa tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri mulize lipenga mofuwula. Tsiku lochita mwambo wopepesera machimo muziliza lipenga mʼdziko lanu lonse.
וקדשתם את שנת החמשים שנה וקראתם דרור בארץ לכל ישביה יובל הוא תהיה לכם ושבתם איש אל אחזתו ואיש אל משפחתו תשבו׃ | 10 |
Mupatule chaka cha makumi asanu, ndipo mulengeze kuti pakhale ufulu mʼdziko lonse kwa onse amene ali mʼmenemo. Kwa inu chakachi chidzakhala choyimba lipenga la chikondwerero. Aliyense wa inu adzayenera kubwerera pa munda wake, ndipo aliyense wa inu adzabwerera ku fuko lake.
יובל הוא שנת החמשים שנה תהיה לכם לא תזרעו ולא תקצרו את ספיחיה ולא תבצרו את נזריה׃ | 11 |
Kwa inu chakachi chidzakhaladi chaka choyimba lipenga kukondwerera zaka makumi asanu. Pa chaka chimenechi musadzale kanthu ndipo musakolole mbewu zomera zokha kapenanso kuthyola mphesa pa mitengo yosasadzira.
כי יובל הוא קדש תהיה לכם מן השדה תאכלו את תבואתה׃ | 12 |
Chimenechi ndi chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Choncho chikhale chaka chopatulika kwa inu. Muzidya zokhazo zimene zakololedwa mʼminda.
בשנת היובל הזאת תשבו איש אל אחזתו׃ | 13 |
“‘Chaka chimenechi ndi choliza lipenga, kukondwerera zaka makumi asanu, ndipo aliyense abwerere pa malo ake.
וכי תמכרו ממכר לעמיתך או קנה מיד עמיתך אל תונו איש את אחיו׃ | 14 |
“‘Ngati unagulitsa kapena kugula malo ako kwa mnzako wa mʼdzikomo, pasakhale kuchenjeretsana.
במספר שנים אחר היובל תקנה מאת עמיתך במספר שני תבואת ימכר לך׃ | 15 |
Ugule kwa mnzako potsata chiwerengero cha zaka zimene zatha kuyambira pa chikondwerero cha chaka cha makumi asanu chapita. Ndipo mnzakoyo akugulitse potsata chiwerengero cha zaka zokolola zomwe zatsala.
לפי רב השנים תרבה מקנתו ולפי מעט השנים תמעיט מקנתו כי מספר תבואת הוא מכר לך׃ | 16 |
Zaka zikakhala zochuluka, uwonjezere mtengo, ndipo zaka zikakhala zochepa, uchepetse mtengo, pakuti chimene iye akukugulitsa ndi zaka zokolola.
ולא תונו איש את עמיתו ויראת מאלהיך כי אני יהוה אלהיכם׃ | 17 |
Musachenjeretsane koma muope Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
ועשיתם את חקתי ואת משפטי תשמרו ועשיתם אתם וישבתם על הארץ לבטח׃ | 18 |
“‘Tsatirani malangizo anga ndipo mverani mosamala malamulo anga ndipo mudzakhala mʼdzikomo mwamtendere.
ונתנה הארץ פריה ואכלתם לשבע וישבתם לבטח עליה׃ | 19 |
Ndipo nthaka idzakupatsani zipatso zake. Mudzadya mpaka kukhuta ndiponso mudzakhala mʼdzikomo mwamtendere.
וכי תאמרו מה נאכל בשנה השביעת הן לא נזרע ולא נאסף את תבואתנו׃ | 20 |
Mwina nʼkafunsa kuti, ‘Kodi chaka chachisanu ndi chiwiri tidzadya chiyani ngati sitidzala kapena kukolola mbewu zathu?’
וצויתי את ברכתי לכם בשנה הששית ועשת את התבואה לשלש השנים׃ | 21 |
Ine ndidzatumiza madalitso ambiri chaka chachisanu ndi chimodzi moti nthaka yanu idzabala zinthu zokwanira kudya zaka zitatu.
וזרעתם את השנה השמינת ואכלתם מן התבואה ישן עד השנה התשיעת עד בוא תבואתה תאכלו ישן׃ | 22 |
Pamene mukudzala chaka chachisanu ndi chitatu, muzidzadya chakudya chogonera ndipo mudzapitirira kudya mpaka nthawi yokolola mʼchaka chachisanu ndi chinayi.
והארץ לא תמכר לצמתת כי לי הארץ כי גרים ותושבים אתם עמדי׃ | 23 |
“‘Malo asagulitsidwe mpaka muyaya chifukwa dzikolo ndi langa. Inu ndinu alendo okhala ndi Ine.
ובכל ארץ אחזתכם גאלה תתנו לארץ׃ | 24 |
Malo onse amene ali mʼmanja mwanu mudzalole kuti amene anakugulitsani awawombole.
כי ימוך אחיך ומכר מאחזתו ובא גאלו הקרב אליו וגאל את ממכר אחיו׃ | 25 |
“‘Ngati Mwisraeli mnzanu wasauka nagulitsako gawo lina la malo ake, mʼbale wake wapaphata abwere kudzawombola malo amene mʼbale wakeyo wagulitsa.
ואיש כי לא יהיה לו גאל והשיגה ידו ומצא כדי גאלתו׃ | 26 |
Koma ngati munthuyo alibe wachibale woti nʼkuwombola malowo koma pambuyo pake iye mwini nʼkulemera ndi kupeza zokwanira kuwombolera, awombole malowo.
וחשב את שני ממכרו והשיב את העדף לאיש אשר מכר לו ושב לאחזתו׃ | 27 |
Awerengerane zaka kuyambira pamene anagulitsa mundawo ndipo amubwezere amene anagulayo ndalama zimene akanayenera kuzipereka mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Atatero angathe kubwerera pa malo ake.
ואם לא מצאה ידו די השיב לו והיה ממכרו ביד הקנה אתו עד שנת היובל ויצא ביבל ושב לאחזתו׃ | 28 |
Koma ngati sakhala nazo zokwanira kuti amubwezere amene anagula malowo, gawo limene anagulitsalo lidzakhala mʼmanja mwa munthu amene anagulayo mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Malowo adzabwezedwa chaka chimenechi, ndipo iye adzatha kubwerera pa malo ake.
ואיש כי ימכר בית מושב עיר חומה והיתה גאלתו עד תם שנת ממכרו ימים תהיה גאלתו׃ | 29 |
“‘Ngati munthu agulitsa nyumba ya mu mzinda umene uli mu linga, angathe kuyiwombola nyumbayo chisanathe chaka chathunthu chigulitsire. Mu nthawi imeneyi wogulitsayo atha kuyiwombola.
ואם לא יגאל עד מלאת לו שנה תמימה וקם הבית אשר בעיר אשר לא חמה לצמיתת לקנה אתו לדרתיו לא יצא ביבל׃ | 30 |
Ngati nyumbayo siwomboledwa chisanathe chaka chimodzicho, nyumbayo idzakhala ya amene anagulayo ndi zidzukulu zake mpaka muyaya. Sidzabwezedwanso kwa mwini wake mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu.
ובתי החצרים אשר אין להם חמה סביב על שדה הארץ יחשב גאלה תהיה לו וביבל יצא׃ | 31 |
Koma nyumba za mʼmizinda yosazingidwa ndi linga ziwomboledwe monga mmene achitira ndi minda ya mʼdzikomo.
וערי הלוים בתי ערי אחזתם גאלת עולם תהיה ללוים׃ | 32 |
“‘Alevi ali ndi ufulu owombola nyumba zawo za mʼmidzi yawo nthawi ina iliyonse.
ואשר יגאל מן הלוים ויצא ממכר בית ועיר אחזתו ביבל כי בתי ערי הלוים הוא אחזתם בתוך בני ישראל׃ | 33 |
Koma ngati Mlevi sawombola nyumba imene inagulitsidwa mʼmudzi mwake, ndiye kuti idzabwezedwe mʼchaka choliza lipenga pokondwerera zaka makumi asanu, popeza nyumba zimenezi zili mʼmidzi ya Alevi ndi yawo pakati pa Aisraeli.
ושדה מגרש עריהם לא ימכר כי אחזת עולם הוא להם׃ | 34 |
Koma malo owetera ziweto a mʼmidzi yawoyo sayenera kugulitsidwa. Awa ndi malo awo mpaka muyaya.
וכי ימוך אחיך ומטה ידו עמך והחזקת בו גר ותושב וחי עמך׃ | 35 |
“‘Ngati mʼbale wako akhala wosauka kuti sangathe kudzisamalira yekha, umuthandize. Ukhale naye ngati mlendo kapena ngati munthu amene ukhala naye kwa kanthawi.
אל תקח מאתו נשך ותרבית ויראת מאלהיך וחי אחיך עמך׃ | 36 |
Usalandire chiwongoladzanja chilichonse kuchokera kwa iye kapena kuwonjezerapo kanthu kena, koma uziopa Mulungu kuti mʼbale wakoyo akhale nawe.
את כספך לא תתן לו בנשך ובמרבית לא תתן אכלך׃ | 37 |
Musakongoze mnzanu ndalama kuti mulandire chiwongoladzanja, kapena kumugulitsa chakudya kuti mupeze phindu.
אני יהוה אלהיכם אשר הוצאתי אתכם מארץ מצרים לתת לכם את ארץ כנען להיות לכם לאלהים׃ | 38 |
Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti ndikupatseni dziko la Kanaani ndi kuti ndikhale Mulungu wanu.
וכי ימוך אחיך עמך ונמכר לך לא תעבד בו עבדת עבד׃ | 39 |
“‘Ngati mʼbale wanu asauka ndipo adzigulitsa yekha kwa inu, musamugwiritse ntchito ngati kapolo.
כשכיר כתושב יהיה עמך עד שנת היבל יעבד עמך׃ | 40 |
Akhale ngati wantchito kapena ngati mlendo. Akugwirireni ntchito mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu.
ויצא מעמך הוא ובניו עמו ושב אל משפחתו ואל אחזת אבתיו ישוב׃ | 41 |
Kenaka iye ndi ana ake achoke, ndipo apite ku fuko lake ndi kubwerera ku malo a makolo ake.
כי עבדי הם אשר הוצאתי אתם מארץ מצרים לא ימכרו ממכרת עבד׃ | 42 |
Chifukwa Aisraeli ndi atumiki anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto, asagulitsidwe ngati akapolo.
לא תרדה בו בפרך ויראת מאלהיך׃ | 43 |
Musawalamulire mwankhanza koma wopani Mulungu wanu.
ועבדך ואמתך אשר יהיו לך מאת הגוים אשר סביבתיכם מהם תקנו עבד ואמה׃ | 44 |
“‘Kunena za akapolo aamuna ndi aakazi, amenewa mungathe kuwagula kuchokera kwa mitundu ya anthu imene yakuzungulirani.
וגם מבני התושבים הגרים עמכם מהם תקנו וממשפחתם אשר עמכם אשר הולידו בארצכם והיו לכם לאחזה׃ | 45 |
Mungathenso kugula akapolo kuchokera kwa alendo amene akukhala nanu kapena kuchokera ku mabanja amene mukukhala nawo amene ndi mbadwa za mʼdziko lanu. Iwowa akhoza kukhala akapolo anu.
והתנחלתם אתם לבניכם אחריכם לרשת אחזה לעלם בהם תעבדו ובאחיכם בני ישראל איש באחיו לא תרדה בו בפרך׃ | 46 |
Akapolowo mungathe kuwasiya mʼmanja mwa ana anu inu mutafa kuti akhale cholowa chawo moyo wawo wonse. Koma musawalamulire mwankhanza Aisraeli anzanu.
וכי תשיג יד גר ותושב עמך ומך אחיך עמו ונמכר לגר תושב עמך או לעקר משפחת גר׃ | 47 |
“‘Ngati mlendo kapena munthu amene akukhala nanu kwa kanthawi kochepa alemera ndipo mmodzi wa abale anu amene akukhala naye pafupi nʼkusauka, nadzigulitsa yekha kwa mlendo amene akukhala pakati panuyo kapena kwa mmodzi wa fuko la munthu wongokhala pafupi nayeyo,
אחרי נמכר גאלה תהיה לו אחד מאחיו יגאלנו׃ | 48 |
wodzigulitsayo ali ndi ufulu wowomboledwa. Mmodzi mwa abale ake angathe kumuwombola:
או דדו או בן דדו יגאלנו או משאר בשרו ממשפחתו יגאלנו או השיגה ידו ונגאל׃ | 49 |
amalume ake kapena mwana wa amalume ake, kapena wachibale wa mu fuko lake. Kapena ngati iye mwini alemera, atha kudziwombola yekha.
וחשב עם קנהו משנת המכרו לו עד שנת היבל והיה כסף ממכרו במספר שנים כימי שכיר יהיה עמו׃ | 50 |
Iye pamodzi ndi munthu amene anamugulayo awerengerane kuyambira chaka chimene anadzigulitsa kwa iyeyo mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Mtengo wodziwombolera ukhale wofanana ndi zakazo. Ndipo nthawi imene anali ndi mbuye wakeyo iwerengedwe ngati nthawi ya munthu wantchito.
אם עוד רבות בשנים לפיהן ישיב גאלתו מכסף מקנתו׃ | 51 |
Ngati patsala zaka zambiri, iye ayenera kulipira mtengo woposera umene anamugulira.
ואם מעט נשאר בשנים עד שנת היבל וחשב לו כפי שניו ישיב את גאלתו׃ | 52 |
Ngati kwatsala zaka zochepa kuti ifike nthawi ya chaka chokondwerera zaka makumi asanu, iye awerengerane ndi mbuye wake, ndipo apereke ndalama za zowomboledwera molingana ndi zaka zotsalazo.
כשכיר שנה בשנה יהיה עמו לא ירדנו בפרך לעיניך׃ | 53 |
Azikhala naye ngati wantchito wolembedwa chaka ndi chaka. Ndipo muonetsetse kuti mbuye wakeyo sakumulamulira mwankhanza.
ואם לא יגאל באלה ויצא בשנת היבל הוא ובניו עמו׃ | 54 |
“‘Ngakhale munthuyo atapanda kuwomboledwa mwa njira zimenezi, iye ndi ana ake ayenera kumasulidwa mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu,
כי לי בני ישראל עבדים עבדי הם אשר הוצאתי אותם מארץ מצרים אני יהוה אלהיכם׃ | 55 |
pakuti Aisraeli ndi atumiki anga. Iwo ndi atumiki anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.