< ויקרא 23 >

וידבר יהוה אל משה לאמר׃ 1
Yehova anawuza Mose kuti,
דבר אל בני ישראל ואמרת אלהם מועדי יהוה אשר תקראו אתם מקראי קדש אלה הם מועדי׃ 2
“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Awa ndi masiku anga osankhika a chikondwerero, masiku osankhika olemekeza Yehova amene uyenera kulengeza kuti akhale masiku opatulika a misonkhano.
ששת ימים תעשה מלאכה וביום השביעי שבת שבתון מקרא קדש כל מלאכה לא תעשו שבת הוא ליהוה בכל מושבתיכם׃ 3
“‘Pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata lopuma, tsiku la msonkhano wopatulika. Kulikonse kumene inu mukukhala musamagwire ntchito iliyonse tsiku limeneli popeza ndi tsiku la Sabata la Yehova.
אלה מועדי יהוה מקראי קדש אשר תקראו אתם במועדם׃ 4
“‘Awa ndiwo masiku osankhidwa a zikondwerero za Yehova, masiku woyera a misonkhano amene muti mudzalengeze pa nthawi yake:
בחדש הראשון בארבעה עשר לחדש בין הערבים פסח ליהוה׃ 5
Chikondwerero cha Paska chiziyamba madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba.
ובחמשה עשר יום לחדש הזה חג המצות ליהוה שבעת ימים מצות תאכלו׃ 6
Tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku lolemekeza Yehova ndipo muziyamba Chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri.
ביום הראשון מקרא קדש יהיה לכם כל מלאכת עבדה לא תעשו׃ 7
Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse.
והקרבתם אשה ליהוה שבעת ימים ביום השביעי מקרא קדש כל מלאכת עבדה לא תעשו׃ 8
Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito yolemetsa.’”
וידבר יהוה אל משה לאמר׃ 9
Yehova anawuza Mose kuti,
דבר אל בני ישראל ואמרת אלהם כי תבאו אל הארץ אשר אני נתן לכם וקצרתם את קצירה והבאתם את עמר ראשית קצירכם אל הכהן׃ 10
“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo ndi kukolola za mʼminda mwanu, mudzabwere kwa wansembe ndi mtolo wa tirigu woyambirira kucha wa mʼminda mwanu.
והניף את העמר לפני יהוה לרצנכם ממחרת השבת יניפנו הכהן׃ 11
Wansembeyo auweyule mtolowo pamaso pa Yehova kotero mtolowo udzalandiridwa mʼmalo mwanu. Wansembe auweyule tsiku lotsatana ndi la Sabata.
ועשיתם ביום הניפכם את העמר כבש תמים בן שנתו לעלה ליהוה׃ 12
Pa tsiku limene muweyula mtolowo, muperekenso mwana wankhosa wa mwamuna wa chaka chimodzi, wopanda chilema kuti akhale nsembe yopsereza ya kwa Yehova.
ומנחתו שני עשרנים סלת בלולה בשמן אשה ליהוה ריח ניחח ונסכה יין רביעת ההין׃ 13
Chopereka chachakudya chake chikhale cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta kuti chikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Yehova, ya fungo lokoma. Ndipo chopereka cha chakumwa chake chikhale vinyo wa malita anayi ndi theka.
ולחם וקלי וכרמל לא תאכלו עד עצם היום הזה עד הביאכם את קרבן אלהיכם חקת עולם לדרתיכם בכל משבתיכם׃ 14
Musadye buledi aliyense kapena tirigu wokazinga, kapena wamuwisi mpaka tsiku limene mwabwera ndi chopereka ichi kwa Mulungu wanu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.
וספרתם לכם ממחרת השבת מיום הביאכם את עמר התנופה שבע שבתות תמימת תהיינה׃ 15
“‘Kuyambira tsiku lotsatana ndi la Sabata lija, tsiku limene munabwera ndi mtolo wa nsembe yoweyula, muziwerenga masabata asanu ndi awiri athunthu.
עד ממחרת השבת השביעת תספרו חמשים יום והקרבתם מנחה חדשה ליהוה׃ 16
Ndiye kuti muwerenge masiku makumi asanu kuchokera pa tsiku lotsatana ndi Sabata la chisanu ndi chiwiri, ndipo kenaka mupereke nsembe ya tirigu watsopano kwa Yehova.
ממושבתיכם תביאו לחם תנופה שתים שני עשרנים סלת תהיינה חמץ תאפינה בכורים ליהוה׃ 17
Kuchokera kulikonse kumene mukukhala, mubwere pamaso pa Yehova ndi buledi muwiri wa ufa wosalala wa makilogalamu awiri, ophikidwa ndi yisiti kuti akhale nsembe yoweyula ya zakudya zoyamba kucha.
והקרבתם על הלחם שבעת כבשים תמימם בני שנה ופר בן בקר אחד ואילם שנים יהיו עלה ליהוה ומנחתם ונסכיהם אשה ריח ניחח ליהוה׃ 18
Pamodzi ndi bulediyu muperekenso ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri, aliyense akhale wa chaka chimodzi ndi wopanda chilema. Pakhalenso ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa zazimuna ziwiri. Zimenezi zidzakhala nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova pamodzi ndi nsembe za zakudya ndi nsembe za zakumwa. Zonsezi zikhale nsembe zopsereza za fungo lokomera Yehova.
ועשיתם שעיר עזים אחד לחטאת ושני כבשים בני שנה לזבח שלמים׃ 19
Kenaka mupereke mbuzi imodzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndiponso ana ankhosa awiri, aliyense wa chaka chimodzi kuti akhale nsembe yachiyanjano.
והניף הכהן אתם על לחם הבכורים תנופה לפני יהוה על שני כבשים קדש יהיו ליהוה לכהן׃ 20
Wansembe aweyule ana ankhosa awiriwo pamaso pa Yehova monga nsembe yoweyula, pamodzi ndi buledi wa tirigu woyambirira kucha. Zimenezi ndi zopereka zopatulika za Yehova zopatsidwa kwa ansembe.
וקראתם בעצם היום הזה מקרא קדש יהיה לכם כל מלאכת עבדה לא תעשו חקת עולם בכל מושבתיכם לדרתיכם׃ 21
Pa tsiku lomwelo mulengeze za msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.
ובקצרכם את קציר ארצכם לא תכלה פאת שדך בקצרך ולקט קצירך לא תלקט לעני ולגר תעזב אתם אני יהוה אלהיכם׃ 22
“‘Pamene mukukolola zinthu mʼmunda mwanu, musakolole munda wanu mpaka mʼmalire mwenimweni, ndipo musatole khunkha lake. Zimenezo musiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
וידבר יהוה אל משה לאמר׃ 23
Yehova anawuza Mose kuti,
דבר אל בני ישראל לאמר בחדש השביעי באחד לחדש יהיה לכם שבתון זכרון תרועה מקרא קדש׃ 24
“Uza Aisraeli kuti, ‘Tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, likhale tsiku lopumula, la msonkhano wopatulika, mulilengeze poyimba lipenga.
כל מלאכת עבדה לא תעשו והקרבתם אשה ליהוה׃ 25
Musagwire ntchito zolemetsa koma mupereke nsembe yopsereza kwa Yehova.’”
וידבר יהוה אל משה לאמר׃ 26
Yehova anawuza Mose kuti,
אך בעשור לחדש השביעי הזה יום הכפרים הוא מקרא קדש יהיה לכם ועניתם את נפשתיכם והקרבתם אשה ליהוה׃ 27
“Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri ndi tsiku lochita Mwambo Wopepesera Machimo. Muzichita msonkhano wopatulika. Muzidzichepetsa pamaso pa Yehova ndi kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova.
וכל מלאכה לא תעשו בעצם היום הזה כי יום כפרים הוא לכפר עליכם לפני יהוה אלהיכם׃ 28
Tsiku limeneli musamagwire ntchito chifukwa ndi tsiku la Mwambo Wopepesera Machimo, kupepesera machimo anu pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
כי כל הנפש אשר לא תענה בעצם היום הזה ונכרתה מעמיה׃ 29
Munthu aliyense amene sasala zakudya pa tsiku limeneli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake.
וכל הנפש אשר תעשה כל מלאכה בעצם היום הזה והאבדתי את הנפש ההוא מקרב עמה׃ 30
Aliyense wogwira ntchito tsiku limeneli ndidzamuwononga pakati pa anthu a mtundu wake.
כל מלאכה לא תעשו חקת עולם לדרתיכם בכל משבתיכם׃ 31
Inu musadzagwire ntchito iliyonse. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.
שבת שבתון הוא לכם ועניתם את נפשתיכם בתשעה לחדש בערב מערב עד ערב תשבתו שבתכם׃ 32
Limeneli kwa inu ndi tsiku la Sabata lopumula, ndipo muyenera kusala zakudya. Kuyambira madzulo a tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi mpaka madzulo ena otsatirawo muzisunga tsikulo ngati Sabata lanu.”
וידבר יהוה אל משה לאמר׃ 33
Yehova anawuza Mose kuti,
דבר אל בני ישראל לאמר בחמשה עשר יום לחדש השביעי הזה חג הסכות שבעת ימים ליהוה׃ 34
“Uwawuze Aisraeli kuti pa masiku asanu ndi awiri kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri pazikhala Chikondwerero cha Misasa cholemekeza Yehova.
ביום הראשון מקרא קדש כל מלאכת עבדה לא תעשו׃ 35
Tsiku loyamba ndi la msonkhano wopatulika, musagwire ntchito zolemetsa.
שבעת ימים תקריבו אשה ליהוה ביום השמיני מקרא קדש יהיה לכם והקרבתם אשה ליהוה עצרת הוא כל מלאכת עבדה לא תעשו׃ 36
Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Kumeneku ndi kutsekera kwa msonkhano waukulu. Musagwire ntchito zolemetsa.
אלה מועדי יהוה אשר תקראו אתם מקראי קדש להקריב אשה ליהוה עלה ומנחה זבח ונסכים דבר יום ביומו׃ 37
(“‘Amenewa ndi masiku osankhika a chikondwerero cha Yehova, amene muziwalengeza kuti ndi nthawi ya msonkhano wopatulika. Masiku amenewa muzipereka nsembe zopsereza, nsembe za chakudya, nsembe zanyama ndi zopereka zachakumwa za tsiku ndi tsiku.
מלבד שבתת יהוה ומלבד מתנותיכם ומלבד כל נדריכם ומלבד כל נדבותיכם אשר תתנו ליהוה׃ 38
Zopereka zimenezi ndi zowonjezera pa zopereka za Yehova za pa Sabata, zopereka zanu zolumbira ndiponso mphatso zanu zaufulu zopereka kwa Yehova.)
אך בחמשה עשר יום לחדש השביעי באספכם את תבואת הארץ תחגו את חג יהוה שבעת ימים ביום הראשון שבתון וביום השמיני שבתון׃ 39
“‘Choncho kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutakolola zinthu mʼmunda mwanu, muchite chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Tsiku loyamba ndi tsiku lopumula, ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu ndi lopumulanso.
ולקחתם לכם ביום הראשון פרי עץ הדר כפת תמרים וענף עץ עבת וערבי נחל ושמחתם לפני יהוה אלהיכם שבעת ימים׃ 40
Pa tsiku loyamba muzitenga zipatso zabwino kwambiri zothyola mʼmitengo, nthambi za kanjedza, nthambi zazikulu za mitengo ya masamba ambiri, ndi za misondozi yakumtsinje, ndipo muzikondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu kwa masiku asanu ndi awiri.
וחגתם אתו חג ליהוה שבעת ימים בשנה חקת עולם לדרתיכם בחדש השביעי תחגו אתו׃ 41
Chaka chilichonse muzichita chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse. Muzichita chikondwerero chimenechi mwezi wachisanu ndi chiwiri.
בסכת תשבו שבעת ימים כל האזרח בישראל ישבו בסכת׃ 42
Muzikhala mʼmisasa masiku asanu ndi awiri. Onse amene ali mbadwa mʼdziko la Israeli azikhala mʼmisasa
למען ידעו דרתיכם כי בסכות הושבתי את בני ישראל בהוציאי אותם מארץ מצרים אני יהוה אלהיכם׃ 43
kuti zidzukulu zanu zidzadziwe kuti ndine amene ndinakhazika Aisraeli mʼmisasa nditawatulutsa ku Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
וידבר משה את מעדי יהוה אל בני ישראל׃ 44
Choncho Mose analengeza kwa Aisraeli masiku osankhika a zikondwerero za Yehova.

< ויקרא 23 >