< ויקרא 15 >
וידבר יהוה אל משה ואל אהרן לאמר׃ | 1 |
Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti,
דברו אל בני ישראל ואמרתם אלהם איש איש כי יהיה זב מבשרו זובו טמא הוא׃ | 2 |
“Yankhulani ndi Aisraeli ndipo muwawuze kuti, ‘Mwamuna aliyense akakhala ndi nthenda yotulutsa mafinya ku maliseche ake, zotulukazo ndi zonyansa ndithu.
וזאת תהיה טמאתו בזובו רר בשרו את זובו או החתים בשרו מזובו טמאתו הוא׃ | 3 |
Lamulo lokhudza kudziyipitsira ndi zotuluka ku maliseche a munthu nali: Malisechewo akamatulukabe mafinya, kaya aleka, munthuyo adzakhala wodetsedwa:
כל המשכב אשר ישכב עליו הזב יטמא וכל הכלי אשר ישב עליו יטמא׃ | 4 |
“‘Bedi lililonse limene munthu wotulutsa mafinyayo agonapo, ndiponso chinthu chilichonse chimene akhalepo chidzakhala chodetsedwa.
ואיש אשר יגע במשכבו יכבס בגדיו ורחץ במים וטמא עד הערב׃ | 5 |
Aliyense wokhudza bedi la munthuyo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
והישב על הכלי אשר ישב עליו הזב יכבס בגדיו ורחץ במים וטמא עד הערב׃ | 6 |
Aliyense wokhala pa chinthu chimene munthu wotulutsa mafinyayo anakhalapo, achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
והנגע בבשר הזב יכבס בגדיו ורחץ במים וטמא עד הערב׃ | 7 |
“‘Aliyense wokhudza thupi la munthu amene akutulutsa mafinyayo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
וכי ירק הזב בטהור וכבס בגדיו ורחץ במים וטמא עד הערב׃ | 8 |
“‘Munthu wotulutsa mafinya akalavulira malovu munthu wina amene ndi woyeretsedwa, munthu ameneyo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
וכל המרכב אשר ירכב עליו הזב יטמא׃ | 9 |
“‘Chilichonse chimene munthuyo akhalira akakwera pa kavalo chidzakhala chodetsedwa.
וכל הנגע בכל אשר יהיה תחתיו יטמא עד הערב והנושא אותם יכבס בגדיו ורחץ במים וטמא עד הערב׃ | 10 |
Ndipo aliyense wokhudza chimene anakhalira munthuyo adzakhala wodetsedwanso mpaka madzulo. Aliyense wonyamula chinthucho achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
וכל אשר יגע בו הזב וידיו לא שטף במים וכבס בגדיו ורחץ במים וטמא עד הערב׃ | 11 |
“‘Munthu wotulutsa mafinyayo akakhudza munthu aliyense asanasambe mʼmanja, wokhudzidwayo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
וכלי חרש אשר יגע בו הזב ישבר וכל כלי עץ ישטף במים׃ | 12 |
“‘Mʼphika wadothi umene munthu wotulutsa mafinyayo wakhudza awuphwanye, ndipo chiwiya chilichonse chamtengo achitsuke ndi madzi.
וכי יטהר הזב מזובו וספר לו שבעת ימים לטהרתו וכבס בגדיו ורחץ בשרו במים חיים וטהר׃ | 13 |
“‘Munthu wotulutsa mafinyayo akaona kuti wachira, awerenge masiku asanu ndi awiri akuyeretsedwa kwake kenaka achape zovala zake ndi kusamba pa kasupe, ndipo adzayeretsedwa.
וביום השמיני יקח לו שתי תרים או שני בני יונה ובא לפני יהוה אל פתח אהל מועד ונתנם אל הכהן׃ | 14 |
Pa tsiku la chisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri kapena mawunda a nkhunda awiri ndi kubwera nazo pamaso pa Yehova pa khomo pa tenti ya msonkhano ndipo azipereke kwa wansembe.
ועשה אתם הכהן אחד חטאת והאחד עלה וכפר עליו הכהן לפני יהוה מזובו׃ | 15 |
Wansembe apereke zimenezo: imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera machimo a munthu wotulutsa mafinya uja pamaso pa Yehova.
ואיש כי תצא ממנו שכבת זרע ורחץ במים את כל בשרו וטמא עד הערב׃ | 16 |
“‘Mwamuna akataya pansi mbewu yake yaumuna, asambe thupi lake lonse. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
וכל בגד וכל עור אשר יהיה עליו שכבת זרע וכבס במים וטמא עד הערב׃ | 17 |
Chovala chilichonse kapena chikopa chilichonse pomwe pagwera mbewu yaumunayo achichape, komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo.
ואשה אשר ישכב איש אתה שכבת זרע ורחצו במים וטמאו עד הערב׃ | 18 |
Mwamuna akagona ndi mkazi wake nataya mbewu yake yaumuna, onse awiriwo asambe. Komabe adzakhala odetsedwa mpaka madzulo.
ואשה כי תהיה זבה דם יהיה זבה בבשרה שבעת ימים תהיה בנדתה וכל הנגע בה יטמא עד הערב׃ | 19 |
“‘Mkazi akakhala wosamba ndipo ikakhala kuti ndi nthawi yake yeniyeni yosamba, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. Aliyense amene adzamukhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
וכל אשר תשכב עליו בנדתה יטמא וכל אשר תשב עליו יטמא׃ | 20 |
“‘Chilichonse chimene mkaziyo agonera pa nthawi yake yosamba chidzakhala chodetsedwa, ndipo chilichonse chimene adzakhalira chidzakhalanso chodetsedwa.
וכל הנגע במשכבה יכבס בגדיו ורחץ במים וטמא עד הערב׃ | 21 |
Aliyense wokhudza bedi lake achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
וכל הנגע בכל כלי אשר תשב עליו יכבס בגדיו ורחץ במים וטמא עד הערב׃ | 22 |
Aliyense wokhudza chimene wakhalapo achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
ואם על המשכב הוא או על הכלי אשר הוא ישבת עליו בנגעו בו יטמא עד הערב׃ | 23 |
Kaya ndi bedi kapena chinthu china chilichonse chimene anakhalapo, ngati munthu wina akhudza chinthucho, munthuyo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
ואם שכב ישכב איש אתה ותהי נדתה עליו וטמא שבעת ימים וכל המשכב אשר ישכב עליו יטמא׃ | 24 |
“‘Mwamuna aliyense akagona naye ndipo magazi osamba kwake ndi kumukhudza, munthuyo adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri, ndipo bedi limene wagonapo lidzakhalanso lodetsedwa.
ואשה כי יזוב זוב דמה ימים רבים בלא עת נדתה או כי תזוב על נדתה כל ימי זוב טמאתה כימי נדתה תהיה טמאה הוא׃ | 25 |
“‘Mkazi akataya magazi masiku ambiri, wosakhala pa nthawi yake yosamba, kapena akamasambabe kupitirira nthawi yake yosamba, mkaziyo adzakhala wodetsedwa nthawi yonse imene akutaya magazi, monga momwe amakhalira pa masiku ake osamba.
כל המשכב אשר תשכב עליו כל ימי זובה כמשכב נדתה יהיה לה וכל הכלי אשר תשב עליו טמא יהיה כטמאת נדתה׃ | 26 |
Bedi lililonse limene mkaziyo adzagonapo pa masiku onse pamene ali wotaya magazi, ndiponso chilichonse chimene wakhalira chidzakhala chodetsedwa monga mmene chimakhalira chodetsedwa pa nthawi yake yosamba.
וכל הנוגע בם יטמא וכבס בגדיו ורחץ במים וטמא עד הערב׃ | 27 |
Aliyense amene adzakhudza zinthu zimenezo adzakhala wodetsedwa ndipo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
ואם טהרה מזובה וספרה לה שבעת ימים ואחר תטהר׃ | 28 |
“‘Nthawi yosamba ikatha, mkaziyo awerenge masiku asanu ndi awiri, ndipo masikuwo akatha adzakhala woyeretsedwa.
וביום השמיני תקח לה שתי תרים או שני בני יונה והביאה אותם אל הכהן אל פתח אהל מועד׃ | 29 |
Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mkaziyo atenge njiwa ziwiri kapena mawunda awiri, ndipo abwere nazo kwa wansembe pa khomo la Tenti ya Msonkhano.
ועשה הכהן את האחד חטאת ואת האחד עלה וכפר עליה הכהן לפני יהוה מזוב טמאתה׃ | 30 |
Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera mkaziyo pamaso pa Yehova chifukwa cha matenda ake wosamba aja.
והזרתם את בני ישראל מטמאתם ולא ימתו בטמאתם בטמאם את משכני אשר בתוכם׃ | 31 |
“‘Choncho muwayeretsa ana a Israeli nʼkudetsedwa kwawo kuti angafe pochita tchimo lowadetsa limene polichita limadetsa malo anga wokhalamo amene ali pakati pawo.’”
זאת תורת הזב ואשר תצא ממנו שכבת זרע לטמאה בה׃ | 32 |
Amenewa ndi malamulo a munthu amene akutuluka mafinya kumaliseche kwake, komanso a munthu aliyense amene wadetsedwa ndi mbewu yaumuna,
והדוה בנדתה והזב את זובו לזכר ולנקבה ולאיש אשר ישכב עם טמאה׃ | 33 |
mkazi wodwala chifukwa cha msambo komanso a mwamuna kapena mkazi amene akutulutsa mafinya kumaliseche kwake ndi mwamuna wogona ndi mkazi amene akusamba.