< איכה 2 >
איכה יעיב באפו אדני את בת ציון השליך משמים ארץ תפארת ישראל ולא זכר הדם רגליו ביום אפו׃ | 1 |
Haa, Ambuye waphimba mwana wamkazi wa Ziyoni ndi mtambo wa mkwiyo wake! Iye wataya pansi ulemerero wa Israeli kuchoka kumwamba. Pa tsiku la mkwiyo wake Iye sanakumbukirenso popondapo mapazi ake.
בלע אדני לא חמל את כל נאות יעקב הרס בעברתו מבצרי בת יהודה הגיע לארץ חלל ממלכה ושריה׃ | 2 |
Ambuye anawononga midzi yonse ya Yakobo mopanda chifundo; mu mkwiyo wake anagwetsa malinga a mwana wamkazi wa Yuda. Anagwetsa pansi mochititsa manyazi maufumu ndi akalonga ake.
גדע בחרי אף כל קרן ישראל השיב אחור ימינו מפני אויב ויבער ביעקב כאש להבה אכלה סביב׃ | 3 |
Atakwiya kwambiri, Ambuye anathyola nyanga iliyonse ya Israeli. Anabweza dzanja lake lamanja pamene mdani anamuyandikira. Ambuye anatentha fuko la Yakobo ngati moto wonyeketsa umene umawononga zinthu zonse zomwe zili pafupi.
דרך קשתו כאויב נצב ימינו כצר ויהרג כל מחמדי עין באהל בת ציון שפך כאש חמתו׃ | 4 |
Wakokera uta wake pa ife ngati ndife adani; wayimiritsa dzanja lake pa ife ngati ndife adani, ndipo anapha onse amene tinkawayangʼana monyadira. Ukali wake ukuyaka ngati moto pa tenti ya mwana wamkazi wa Ziyoni.
היה אדני כאויב בלע ישראל בלע כל ארמנותיה שחת מבצריו וירב בבת יהודה תאניה ואניה׃ | 5 |
Ambuye ali ngati mdani; wawonongeratu Israeli; wawonongeratu nyumba zake zonse zaufumu ndipo wawononga malinga ake. Iye wachulukitsa kubuma ndi kulira kwa mwana wamkazi wa Yuda.
ויחמס כגן שכו שחת מועדו שכח יהוה בציון מועד ושבת וינאץ בזעם אפו מלך וכהן׃ | 6 |
Wagwetsa malo ake okhalamo ngati khumbi la mʼmunda; wawononga malo ake a msonkhano. Yehova wayiwalitsa Ziyoni maphwando ake oyikika ndi masabata ake. Mokwiya kwambiri, Iye ananyoza mfumu ndi wansembe.
זנח אדני מזבחו נאר מקדשו הסגיר ביד אויב חומת ארמנותיה קול נתנו בבית יהוה כיום מועד׃ | 7 |
Ambuye wakana guwa lake la nsembe ndipo wasiya malo ake opatulika. Iye wapereka makoma a nyumba zake zaufumu kwa mdani wake; adaniwo anafuwula mʼnyumba ya Yehova ngati kuti ndi pa tsiku la chikondwerero.
חשב יהוה להשחית חומת בת ציון נטה קו לא השיב ידו מבלע ויאבל חל וחומה יחדו אמללו׃ | 8 |
Yehova anatsimikiza kugwetsa makoma a mwana wamkazi wa Ziyoni. Anawayesa ndi chingwe ndipo sanafune kuleka kuwagwetsa. Analiritsa malinga ndi makoma; onse anawonongeka pamodzi.
טבעו בארץ שעריה אבד ושבר בריחיה מלכה ושריה בגוים אין תורה גם נביאיה לא מצאו חזון מיהוה׃ | 9 |
Zipata za Yerusalemu zalowa pansi; wathyola ndi kuwononga mipiringidzo yake. Mfumu ndi akalonga ake agwidwa ukapolo pakati pa mitundu ya anthu, palibenso lamulo, ndipo aneneri ake sakupeza masomphenya kuchokera kwa Yehova.
ישבו לארץ ידמו זקני בת ציון העלו עפר על ראשם חגרו שקים הורידו לארץ ראשן בתולת ירושלם׃ | 10 |
Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala chete pansi; awaza fumbi pa mitu yawo ndipo avala ziguduli. Anamwali a Yerusalemu aweramitsa mitu yawo pansi.
כלו בדמעות עיני חמרמרו מעי נשפך לארץ כבדי על שבר בת עמי בעטף עולל ויונק ברחבות קריה׃ | 11 |
Maso anga atopa ndi kulira, ndazunzika mʼmoyo mwanga, mtima wanga wadzaza ndi chisoni chifukwa anthu anga akuwonongeka, chifukwa ana ndi makanda akukomoka mʼmisewu ya mu mzinda.
לאמתם יאמרו איה דגן ויין בהתעטפם כחלל ברחבות עיר בהשתפך נפשם אל חיק אמתם׃ | 12 |
Anawo akufunsa amayi awo kuti, “Kodi tirigu ndi vinyo zili kuti?” pamene akukomoka ngati anthu olasidwa mʼmisewu ya mʼmizinda, pamene miyoyo yawo ikufowoka mʼmanja mwa amayi awo.
מה אעודך מה אדמה לך הבת ירושלם מה אשוה לך ואנחמך בתולת בת ציון כי גדול כים שברך מי ירפא לך׃ | 13 |
Ndinganene chiyani za iwe? Ndingakufanizire ndi chiyani, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu? Kodi ndingakufanizire ndi yani kuti ndikutonthoze, iwe namwali wa Ziyoni? Chilonda chako ndi chozama ngati nyanja, kodi ndani angakuchiritse?
נביאיך חזו לך שוא ותפל ולא גלו על עונך להשיב שביתך ויחזו לך משאות שוא ומדוחים׃ | 14 |
Masomphenya a aneneri ako anali abodza ndi achabechabe. Iwo sanakupulumutse kuti usapite ku ukapolo poyika poyera mphulupulu zako. Mauthenga amene anakupatsa anali achabechabe ndi osocheretsa.
ספקו עליך כפים כל עברי דרך שרקו וינעו ראשם על בת ירושלם הזאת העיר שיאמרו כלילת יפי משוש לכל הארץ׃ | 15 |
Onse oyenda mʼnjira yako akukuwombera mʼmanja; akugwedeza mitu yawo ndi kukunyodola iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu: “Kodi mzinda uja ndi uwu umene unkatchedwa wokongola kotheratu, chimwemwe cha dziko lonse lapansi?”
פצו עליך פיהם כל אויביך שרקו ויחרקו שן אמרו בלענו אך זה היום שקוינהו מצאנו ראינו׃ | 16 |
Adani ako onse akutsekulira pakamwa ndi kukunyoza; iwo akunyogodola ndi kukukuta mano awo, ndipo akuti, “Tamumeza. Tsiku ili ndi lomwe timayembekezera; tili ndi moyo kuti tilione.”
עשה יהוה אשר זמם בצע אמרתו אשר צוה מימי קדם הרס ולא חמל וישמח עליך אויב הרים קרן צריך׃ | 17 |
Yehova wachita chimene anakonzeratu; wakwaniritsa mawu ake, amene anatsimikiza kale lomwe. Wakuwononga mopanda chifundo, walola mdani kuti akondwere chifukwa cha kugwa kwako, wakweza mphamvu za adani ako.
צעק לבם אל אדני חומת בת ציון הורידי כנחל דמעה יומם ולילה אל תתני פוגת לך אל תדם בת עינך׃ | 18 |
Mitima ya anthu ikufuwulira Ambuye. Iwe khoma la mwana wamkazi wa Ziyoni, misozi yako itsike ngati mtsinje usana ndi usiku; usadzipatse wekha mpumulo, maso ako asaleke kukhetsa misozi.
קומי רני בליל לראש אשמרות שפכי כמים לבך נכח פני אדני שאי אליו כפיך על נפש עולליך העטופים ברעב בראש כל חוצות׃ | 19 |
Dzuka, fuwula usiku, pamene alonda ayamba kulondera; khuthula mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye. Kweza manja ako kwa Iye chifukwa cha miyoyo ya ana ako, amene akukomoka ndi njala mʼmisewu yonse ya mu mzinda.
ראה יהוה והביטה למי עוללת כה אם תאכלנה נשים פרים עללי טפחים אם יהרג במקדש אדני כהן ונביא׃ | 20 |
Inu Yehova, onani, ndipo ganizirani: kodi ndani amene mwamuchitirapo zinthu ngati izi? Kodi amayi adye ana awo, amene amawasamalira? Kodi ansembe ndi aneneri awaphere mʼmalo opatulika a Ambuye?
שכבו לארץ חוצות נער וזקן בתולתי ובחורי נפלו בחרב הרגת ביום אפך טבחת לא חמלת׃ | 21 |
Anyamata ndi okalamba aligone pamodzi pa fumbi la mʼmisewu ya mu mzinda; anyamata anga ndi anamwali anga aphedwa ndi lupanga. Inu Yehova mwawapha pa tsiku la mkwiyo wanu; mwawapha mopanda chifundo.
תקרא כיום מועד מגורי מסביב ולא היה ביום אף יהוה פליט ושריד אשר טפחתי ורביתי איבי כלם׃ | 22 |
Ngati momwe mumayitanira pa tsiku la phwando, chimodzimodzinso mwandiyitanira zoopsa mbali zonse. Pa tsiku limene Yehova wakwiya palibe amene angathawe ndi kukhala ndi moyo; mdani wanga wawononga onse amene ndinkawasamala ndi kuwalera.