< שופטים 20 >
ויצאו כל בני ישראל ותקהל העדה כאיש אחד למדן ועד באר שבע וארץ הגלעד אל יהוה המצפה׃ | 1 |
Ndipo Aisraeli onse kuyambira ku dziko la Dani mpaka ku Beeriseba ndiponso ku dziko la Giliyadi ananyamuka ngati munthu mmodzi nakasonkhana pamaso pa Yehova ku Mizipa.
ויתיצבו פנות כל העם כל שבטי ישראל בקהל עם האלהים ארבע מאות אלף איש רגלי שלף חרב׃ | 2 |
Atsogoleri a anthu onse ndi a mafuko onse Aisraeli anali nawo pa msonkhano wa anthu a Mulungu. Onse pamodzi analipo asilikali oyenda pansi 400,000 atanyamula malupanga.
וישמעו בני בנימן כי עלו בני ישראל המצפה ויאמרו בני ישראל דברו איכה נהיתה הרעה הזאת׃ | 3 |
Anthu a fuko la Benjamini anali atamva kuti Aisraeli apita ku Mizipa. Tsono Aisraeli anati, “Tiwuzeni, zinthu zoyipa izi zinachitika bwanji.”
ויען האיש הלוי איש האשה הנרצחה ויאמר הגבעתה אשר לבנימן באתי אני ופילגשי ללון׃ | 4 |
Choncho Mlevi uja, mwamuna wa mkazi wophedwa uja anayankha nati, “Ine ndinapita ku Gibeya mʼdziko la Benjamini pamodzi ndi mzikazi wanga kuti tikagone kumeneko.
ויקמו עלי בעלי הגבעה ויסבו עלי את הבית לילה אותי דמו להרג ואת פילגשי ענו ותמת׃ | 5 |
Usiku anthu a ku Gibeya anandiwukira, nazinga nyumba munali ine. Ankafuna kundipha ndipo anagona ndi mzikazi wanga momukakamiza mpaka anafa.
ואחז בפילגשי ואנתחה ואשלחה בכל שדה נחלת ישראל כי עשו זמה ונבלה בישראל׃ | 6 |
Ine ndinatenga mzikazi wangayo ndi kumudula nthulinthuli ndikuzitumiza kwa fuko lililonse la Aisraeli. Anthu amenewa, zedi achita chinthu chonyansa kwambiri mʼdziko lino la Israeli.
הנה כלכם בני ישראל הבו לכם דבר ועצה הלם׃ | 7 |
Ndi zimenezotu inu Aisraeli nonse; yankhulaponi mawu ndi kupereka maganizo anu.”
ויקם כל העם כאיש אחד לאמר לא נלך איש לאהלו ולא נסור איש לביתו׃ | 8 |
Anthu onse anayimirira ngati munthu mmodzi nanena kuti, “Palibe mmodzi wa ife amene apite ku nyumba kwake. Palibe amene abwerere ku nyumba kwake.
ועתה זה הדבר אשר נעשה לגבעה עליה בגורל׃ | 9 |
Koma tsopano chimene ife tichite ndi dziko la Gibeya ndi ichi: Tidzapita kukamenyana nawo potsatira zimene maere anene.
ולקחנו עשרה אנשים למאה לכל שבטי ישראל ומאה לאלף ואלף לרבבה לקחת צדה לעם לעשות לבואם לגבע בנימן ככל הנבלה אשר עשה בישראל׃ | 10 |
Mʼmafuko onse a Aisraeli tidzasankha anthu khumi pa anthu 100 aliwonse: ndiye kuti anthu 100 pa anthu 1,000 aliwonse kapena anthu 1,000 pa anthu 10,000 aliwonse. Anthu amenewa adzasonkhanitsa zakudya za ankhondo, ndipo ankhondowo adzapita kukalipsira anthu a ku Geba mʼdziko la Benjamini chifukwa chochita chinthu chonyansa chotere mʼdziko la Israeli.”
ויאסף כל איש ישראל אל העיר כאיש אחד חברים׃ | 11 |
Choncho anthu a ku Israeli anasonkhana pamodzi nagwirizana chimodzi, kukalimbana ndi mzindawo.
וישלחו שבטי ישראל אנשים בכל שבטי בנימן לאמר מה הרעה הזאת אשר נהיתה בכם׃ | 12 |
Mafuko a Israeli anatumiza anthu kwa fuko lonse la Benjamini kukafunsa kuti, “Kodi zoyipa zachitika pakati panuzi ndi zotani?
ועתה תנו את האנשים בני בליעל אשר בגבעה ונמיתם ונבערה רעה מישראל ולא אבו בנימן לשמע בקול אחיהם בני ישראל׃ | 13 |
Tsono tikuti mutipatse anthu achabechabe a ku Gibeya kuti tiwaphe kuti tichotse chinthu choyipachi mʼdziko la Israeli.” Koma fuko la Benjamini silinafune kumvera zimene ananena Aisraeli anzawo.
ויאספו בני בנימן מן הערים הגבעתה לצאת למלחמה עם בני ישראל׃ | 14 |
Mʼmalo mwake, Abenjaminiwo anatuluka mʼmizinda yawo ku Gibeya kukamenyana ndi Aisraeli.
ויתפקדו בני בנימן ביום ההוא מהערים עשרים וששה אלף איש שלף חרב לבד מישבי הגבעה התפקדו שבע מאות איש בחור׃ | 15 |
Tsiku limenelo Abenjamini anasonkhanitsa kuchokera ku mizinda yawo ankhondo 26,000 amalupanga awo, osawerengera anthu ena 700 a ku Gibeya amene anasankhidwa.
מכל העם הזה שבע מאות איש בחור אטר יד ימינו כל זה קלע באבן אל השערה ולא יחטא׃ | 16 |
Mwa onsewa panali ankhondo 70 amanzere amene aliyense anali wodziwa kulasa ngakhale tsitsi limodzi ndi mwala osaphonya.
ואיש ישראל התפקדו לבד מבנימן ארבע מאות אלף איש שלף חרב כל זה איש מלחמה׃ | 17 |
Aisraeli, kupatula fuko la Benjamini, anasonkhanitsa anthu 400,000 a malupanga, onse odziwa bwino nkhondo.
ויקמו ויעלו בית אל וישאלו באלהים ויאמרו בני ישראל מי יעלה לנו בתחלה למלחמה עם בני בנימן ויאמר יהוה יהודה בתחלה׃ | 18 |
Ndipo Aisraeli ananyamuka kupita ku Beteli kukafunsira kwa Mulungu. Iwo anati, “Ndani mwa ife amene angayambe kukamenyana ndi fuko la Benjamini?” Yehova anayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo liyambe.”
ויקומו בני ישראל בבקר ויחנו על הגבעה׃ | 19 |
Mmawa mwake Israeli ananyamuka nakamanga msasa moyangʼanana ndi Gibeya.
ויצא איש ישראל למלחמה עם בנימן ויערכו אתם איש ישראל מלחמה אל הגבעה׃ | 20 |
Aisraeli anapita kukachita nkhondo ndi fuko la Benjamini ndipo anandandalika ankhondo awo moyangʼanana ndi Gibeya.
ויצאו בני בנימן מן הגבעה וישחיתו בישראל ביום ההוא שנים ועשרים אלף איש ארצה׃ | 21 |
A fuko la Benjamini anatuluka ku Gibeya ndipo tsiku limenelo anapha Aisraeli 22,000 ku nkhondoko.
ויתחזק העם איש ישראל ויספו לערך מלחמה במקום אשר ערכו שם ביום הראשון׃ | 22 |
Koma ankhondo a Israeli analimbikitsananso mtima ndipo anasonkhanitsanso kachiwiri ankhondo awo pa malo pamene anawandandalika poyamba paja.
ויעלו בני ישראל ויבכו לפני יהוה עד הערב וישאלו ביהוה לאמר האוסיף לגשת למלחמה עם בני בנימן אחי ויאמר יהוה עלו אליו׃ | 23 |
Aisraeli anapita kukalira pamaso pa Yehova mpaka madzulo. Iwo anafunsa Yehova kuti, “Kodi tipitenso kukamenyana ndi a fuko la Benjamini abale athu?” Yehova anayankha kuti, “Pitani mukalimbane nawo.”
ויקרבו בני ישראל אל בני בנימן ביום השני׃ | 24 |
Ndipo Aisraeli anayandikiranso pafupi ndi fuko la Benjamini tsiku lachiwiri lake kuti amenyane nawo.
ויצא בנימן לקראתם מן הגבעה ביום השני וישחיתו בבני ישראל עוד שמנת עשר אלף איש ארצה כל אלה שלפי חרב׃ | 25 |
Pa tsiku lachiwiri lomwelo Abenjamini anatulukanso mu mzinda wa Gibeya ndipo anaphanso ankhondo 18,000. Onse amene anawaphawo anali odziwa kugwiritsa ntchito bwino malupanga.
ויעלו כל בני ישראל וכל העם ויבאו בית אל ויבכו וישבו שם לפני יהוה ויצומו ביום ההוא עד הערב ויעלו עלות ושלמים לפני יהוה׃ | 26 |
Tsono Aisraeli onse, gulu lonse la ankhondo, anapita ku Beteli kukalira pamaso pa Yehova. Anakhala pansi nasala zakudya tsiku lonse mpaka madzulo. Anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova.
וישאלו בני ישראל ביהוה ושם ארון ברית האלהים בימים ההם׃ | 27 |
Bokosi la Chipangano cha Yehova linali kumeneko.
ופינחס בן אלעזר בן אהרן עמד לפניו בימים ההם לאמר האוסף עוד לצאת למלחמה עם בני בנימן אחי אם אחדל ויאמר יהוה עלו כי מחר אתננו בידך׃ | 28 |
Finehasi mwana wa Eliezara mwana wa Aaroni ndiye ankatumikira nthawi imeneyo. Tsono Aisraeli anafunsa Yehova kuti, “Kodi tipitenso kukachita nkhondo ndi mʼbale athu Abenjamini, kapena ayi?” Yehova anayankha kuti, “Pitaninso chifukwa mawa ndidzawapereka mʼmanja mwanu.”
וישם ישראל ארבים אל הגבעה סביב׃ | 29 |
Choncho Aisraeli anayika anthu obisalira mozungulira Gibeya.
ויעלו בני ישראל אל בני בנימן ביום השלישי ויערכו אל הגבעה כפעם בפעם׃ | 30 |
Tsiku lachitatu anapita kukamenyana ndi Benjamini ndipo anayika ankhondo mʼmalo mwawo kuti amenyane ndi Gibeya monga anachitira poyamba.
ויצאו בני בנימן לקראת העם הנתקו מן העיר ויחלו להכות מהעם חללים כפעם בפעם במסלות אשר אחת עלה בית אל ואחת גבעתה בשדה כשלשים איש בישראל׃ | 31 |
Abenjamini anatuluka kukamenyana nawo anthuwo ndipo anapita kutali ndi mzindawo. Iwo anayamba kupha Aisraeli monga poyamba paja, kotero kuti anapha anthu pafupifupi makumi atatu. Mitembo ya ena inali mu misewu yayikulu yopita ku Beteli ndi ku Gibeya, ndipo ina inali kwina poyera.
ויאמרו בני בנימן נגפים הם לפנינו כבראשנה ובני ישראל אמרו ננוסה ונתקנהו מן העיר אל המסלות׃ | 32 |
Abenjamini ankanena kuti, “Tikuwagonjetsa monga poyamba.” Koma Aisraeli ankanena kuti, “Tiyeni tithawe kuti apite ku msewu chapatali ndi mzinda wawo.”
וכל איש ישראל קמו ממקומו ויערכו בבעל תמר וארב ישראל מגיח ממקמו ממערה גבע׃ | 33 |
Choncho Aisraeli onse anachoka mʼmalo mwawo ndi kukandanda ku Baala-Tamara, ndipo Aisraeli obisalira aja anatuluka mʼmalo awo kummawa kwa Geba.
ויבאו מנגד לגבעה עשרת אלפים איש בחור מכל ישראל והמלחמה כבדה והם לא ידעו כי נגעת עליהם הרעה׃ | 34 |
Aisraeli osankhidwa 10,000 ndiwo anabwera kudzalimbana ndi mzinda wa Gibeya. Nkhondoyo inafika poyipa kwambiri mwakuti Abenjamini samadziwa kuti zoopsa zili pafupi kuwagwera.
ויגף יהוה את בנימן לפני ישראל וישחיתו בני ישראל בבנימן ביום ההוא עשרים וחמשה אלף ומאה איש כל אלה שלף חרב׃ | 35 |
Tsono Yehova anagonjetsa Abenjamini pamaso pa Israeli motero kuti Aisraeli anapha ankhondo a Abenjamini 25,100 tsiku limenelo.
ויראו בני בנימן כי נגפו ויתנו איש ישראל מקום לבנימן כי בטחו אל הארב אשר שמו אל הגבעה׃ | 36 |
Choncho Abenjamini anaona kuti agonjetsedwa. Paja Aisraeli anathawa fuko la Benjamini chifukwa ankadalira anthu amene anawayika kuti abisalire mzinda wa Gibeya.
והארב החישו ויפשטו אל הגבעה וימשך הארב ויך את כל העיר לפי חרב׃ | 37 |
Tsono anthu amene anabisala aja anachita changu kuwuthira nkhondo mzinda wa Gibeyawo. Ndipo anapha anthu onse a mu mzindawo ndi lupanga.
והמועד היה לאיש ישראל עם הארב הרב להעלותם משאת העשן מן העיר׃ | 38 |
Chizindikiro chimene Aisraeli anapangana ndi anthu obisalira aja chinali chakuti obisalira aja akangofukiza utsi wambiri ngati mtambo mu mzindamo,
ויהפך איש ישראל במלחמה ובנימן החל להכות חללים באיש ישראל כשלשים איש כי אמרו אך נגוף נגף הוא לפנינו כמלחמה הראשנה׃ | 39 |
ndiye kuti Aisraeli enawo abwerere ku nkhondo. Pa nthawiyo nʼkuti Abenjamini atayamba kale kumenya Aisraeliwo kwambiri ndi kupha pafupifupi anthu makumi atatu. Ndipo iwo ankanena kuti, “Ndithu tawapha monga poyamba paja.”
והמשאת החלה לעלות מן העיר עמוד עשן ויפן בנימן אחריו והנה עלה כליל העיר השמימה׃ | 40 |
Koma pamene utsi wa chizindikiro uja unayamba kukwera tolotolo mmwamba kuchoka mu mzindamo, Abenjamini anayangʼana mʼmbuyo ndipo anangoona utsi mu mzinda onse uli tolotolo kukwera mmwamba.
ואיש ישראל הפך ויבהל איש בנימן כי ראה כי נגעה עליו הרעה׃ | 41 |
Kenaka Aisraeli anabwerera ndipo Abenjamini anachita mantha, chifukwa anaona kuti zoopsa zili pafupi kuwagwera.
ויפנו לפני איש ישראל אל דרך המדבר והמלחמה הדביקתהו ואשר מהערים משחיתים אותו בתוכו׃ | 42 |
Choncho anathawa pamaso pa Aisraeli kudzera njira ya ku chipululu, koma nkhondo inawapeza. Ndipo anaphedwa kumeneko ndi Aisraeli amene anachokera mu mzindamo.
כתרו את בנימן הרדיפהו מנוחה הדריכהו עד נכח הגבעה ממזרח שמש׃ | 43 |
Anawazungulira Abenjaminiwo, nawathamangitsa ndi kuwagonjetseratu osawachitira chifundo mpaka ku dera la kummawa kwa Gibeya.
ויפלו מבנימן שמנה עשר אלף איש את כל אלה אנשי חיל׃ | 44 |
Abenjamini 18,000 olimba mtima anaphedwa.
ויפנו וינסו המדברה אל סלע הרמון ויעללהו במסלות חמשת אלפים איש וידביקו אחריו עד גדעם ויכו ממנו אלפים איש׃ | 45 |
Koma ena anatembenuka nathawira ku chipululu ku thanthwe la Rimoni. Mwa iwowa Aisraeli anapha Abenjamini 5,000 mʼmisewu yayikulu. Anawapitikitsabe Abenjaminiwo mpaka kufika ku Gidomu ndi kuphanso ena 2,000.
ויהי כל הנפלים מבנימן עשרים וחמשה אלף איש שלף חרב ביום ההוא את כל אלה אנשי חיל׃ | 46 |
Pa tsiku limenelo Abenjamini olimba mtima okhala ndi malupanga okwana 25,000 anafa.
ויפנו וינסו המדברה אל סלע הרמון שש מאות איש וישבו בסלע רמון ארבעה חדשים׃ | 47 |
Koma anthu 700 anabwerera ndi kuthawira ku chipululu ku thanthwe la Rimoni kumene anakhalako miyezi inayi.
ואיש ישראל שבו אל בני בנימן ויכום לפי חרב מעיר מתם עד בהמה עד כל הנמצא גם כל הערים הנמצאות שלחו באש׃ | 48 |
Aisraeli anabwerera kukamenyana ndi Abenjamini otsala ndi kuwapha ndi lupanga kuphatikizapo ziweto ndi zonse anali nazo. Ndipo anayatsa moto mizinda yonse anayipeza.