< שופטים 2 >
ויעל מלאך יהוה מן הגלגל אל הבכים ויאמר אעלה אתכם ממצרים ואביא אתכם אל הארץ אשר נשבעתי לאבתיכם ואמר לא אפר בריתי אתכם לעולם׃ | 1 |
Mngelo wa Yehova anapita ku Bokimu kuchokera ku Giligala ndipo anati kwa Aisraeli, “Ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndikukulowetsani mʼdziko limene ndinalumbira kwa makolo anu. Ndinati ‘Sindidzaswa pangano langa ndi inu,
ואתם לא תכרתו ברית ליושבי הארץ הזאת מזבחותיהם תתצון ולא שמעתם בקלי מה זאת עשיתם׃ | 2 |
ndipo inu musadzachite pangano ndi anthu a dziko lino, koma mudzaphwanye maguwa awo ansembe.’ Koma inu simunamvere lamulo langa. Chifukwa chiyani mwachita zimenezi?
וגם אמרתי לא אגרש אותם מפניכם והיו לכם לצדים ואלהיהם יהיו לכם למוקש׃ | 3 |
Ndikukuwuzani tsopano kuti sindithamangitsa nzikazo pamene inu mukufika. Ndidzawasandutsa kukhala adani anu ndipo milungu yawo idzakhala ngati msampha kwa inu.”
ויהי כדבר מלאך יהוה את הדברים האלה אל כל בני ישראל וישאו העם את קולם ויבכו׃ | 4 |
Mngelo wa Mulungu atayankhula izi kwa Aisraeli, onse analira mokweza,
ויקראו שם המקום ההוא בכים ויזבחו שם ליהוה׃ | 5 |
ndipo anatcha malowo kuti Bokimu (kutanthauza kuti Olira). Pamenepo anapereka nsembe kwa Yehova.
וישלח יהושע את העם וילכו בני ישראל איש לנחלתו לרשת את הארץ׃ | 6 |
Yoswa atawuza Aisraeli kuti achoke, iwo anapita kukatenga dzikolo, aliyense dera lake.
ויעבדו העם את יהוה כל ימי יהושע וכל ימי הזקנים אשר האריכו ימים אחרי יהושוע אשר ראו את כל מעשה יהוה הגדול אשר עשה לישראל׃ | 7 |
Anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a moyo wa Yoswa. Atamwalira Yoswa, Aisraeli anatumikirabe Yehova nthawi yonse ya moyo wa akuluakulu amene anaona zazikulu zimene Yehova anawachitira.
וימת יהושע בן נון עבד יהוה בן מאה ועשר שנים׃ | 8 |
Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110.
ויקברו אותו בגבול נחלתו בתמנת חרס בהר אפרים מצפון להר געש׃ | 9 |
Ndipo anamuyika mʼmanda a mʼdziko lake, ku Timnati-Heresi mʼdziko la mapiri la Efereimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.
וגם כל הדור ההוא נאספו אל אבותיו ויקם דור אחר אחריהם אשר לא ידעו את יהוה וגם את המעשה אשר עשה לישראל׃ | 10 |
Mʼbado onse utapita kukakhala ndi anthu a mtundu awo, kenaka panauka mʼbado wina umene sunadziwe Yehova ngakhale ntchito zazikulu zimene Yehova anachitira Aisraeli.
ויעשו בני ישראל את הרע בעיני יהוה ויעבדו את הבעלים׃ | 11 |
Choncho Aisraeli anayamba kuchita zinthu zoyipa pamaso pa Yehova ndipo anatumikira Abaala.
ויעזבו את יהוה אלהי אבותם המוציא אותם מארץ מצרים וילכו אחרי אלהים אחרים מאלהי העמים אשר סביבותיהם וישתחוו להם ויכעסו את יהוה׃ | 12 |
Iwo anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa ku Igupto. Ndipo anatsatira ndi kupembedza milungu yosiyanasiyana ya anthu amene anawazungulira. Motero Aisraeli anakwiyitsa Yehova.
ויעזבו את יהוה ויעבדו לבעל ולעשתרות׃ | 13 |
Iwo anasiya Yehova ndi kumatumikira Baala ndi Asiteroti.
ויחר אף יהוה בישראל ויתנם ביד שסים וישסו אותם וימכרם ביד אויביהם מסביב ולא יכלו עוד לעמד לפני אויביהם׃ | 14 |
Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha amene ankasakaza zinthu zawo. Ndipo analola kuti adani awo owazungulira amene sanathenso kulimbana nawo, awagonjetse.
בכל אשר יצאו יד יהוה היתה בם לרעה כאשר דבר יהוה וכאשר נשבע יהוה להם ויצר להם מאד׃ | 15 |
Nthawi zonse Aisraeli ankati akapita ku nkhondo, Yehova amalimbana nawo kuti agonjetsedwe, monga ananenera molumbira kuti zidzaterodi. Choncho iwo anali pa mavuto aakulu.
ויקם יהוה שפטים ויושיעום מיד שסיהם׃ | 16 |
Choncho Yehova anawawutsira atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankasakaza zinthu zawo.
וגם אל שפטיהם לא שמעו כי זנו אחרי אלהים אחרים וישתחוו להם סרו מהר מן הדרך אשר הלכו אבותם לשמע מצות יהוה לא עשו כן׃ | 17 |
Komabe iwo sanawamvere atsogoleri awowo popeza ankapembedza milungu ina ndi kumayigwadira. Iwo anapatuka msangamsanga mu njira imene ankayendamo makolo awo. Iwo aja ankamvera malamulo a Yehova, koma mʼbado uwu ayi.
וכי הקים יהוה להם שפטים והיה יהוה עם השפט והושיעם מיד איביהם כל ימי השופט כי ינחם יהוה מנאקתם מפני לחציהם ודחקיהם׃ | 18 |
Nthawi zonse Yehova akawautsira mtsogoleri, Iye amakhala naye, ndipo mtsogoleriyo ankawapulumutsa Aisraeliwo mʼmanja mwa adani awo mʼnthawi imene anali moyo. Yehova ankawamvera chisoni Aisraeli pamene ankabuwula chifukwa cha anthu owazunza ndi kuwasautsa.
והיה במות השופט ישבו והשחיתו מאבותם ללכת אחרי אלהים אחרים לעבדם ולהשתחות להם לא הפילו ממעלליהם ומדרכם הקשה׃ | 19 |
Koma nthawi zonse mtsogoleri akamwalira, Aisraeli ankabwerera mʼmbuyo. Iwo amadzisandutsa oyipa kupambana makolo awo popeza ankatsata milungu ina, kuyitumikira ndi kumayigwadira. Anakana kusiya makhalidwe awo oyipa ndi njira zawo zamakani.
ויחר אף יהוה בישראל ויאמר יען אשר עברו הגוי הזה את בריתי אשר צויתי את אבותם ולא שמעו לקולי׃ | 20 |
Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeli ndipo anati, “Chifukwa mtundu uwu waswa pangano limene ndinakhazikitsa ndi makolo awo ndipo sanandimvere,
גם אני לא אוסיף להוריש איש מפניהם מן הגוים אשר עזב יהושע וימת׃ | 21 |
Inenso sindidzapirikitsanso mtundu uli wonse wa anthu amene Yoswa anawasiya pomwalira.
למען נסות בם את ישראל השמרים הם את דרך יהוה ללכת בם כאשר שמרו אבותם אם לא׃ | 22 |
Ndidzatero kuti ndiwayese Aisraeli ndi kuona ngati adzasamala kuyenda mʼnjira ya Ine Yehova monga momwe ankachitira makolo awo.”
וינח יהוה את הגוים האלה לבלתי הורישם מהר ולא נתנם ביד יהושע׃ | 23 |
Choncho Yehova anayileka mitundu imeneyi ndipo sanayithamangitse kapena kuyipereka mʼmanja mwa Yoswa.