< איוב 7 >
הלא צבא לאנוש על ארץ וכימי שכיר ימיו׃ | 1 |
“Kodi munthu sakhala ndi ntchito yowawa pa dziko lapansi? Kodi masiku ake sali ngati munthu waganyu?
כעבד ישאף צל וכשכיר יקוה פעלו׃ | 2 |
Monga ngati kapolo wolakalaka mthunzi wa nthawi yamadzulo, kapena ngati munthu waganyu woyembekezera malipiro ake,
כן הנחלתי לי ירחי שוא ולילות עמל מנו לי׃ | 3 |
choncho ine ndapatsidwa nthawi yongovutika pachabe, ndiponso usiku wamasautso wapatsidwa kwa ine.
אם שכבתי ואמרתי מתי אקום ומדד ערב ושבעתי נדדים עדי נשף׃ | 4 |
Ndikamagona ndimaganiza kuti, ‘Kodi kucha liti?’ Usikuwo umatalika ndipo sindigona tulo mpaka mmawa.
לבש בשרי רמה וגיש עפר עורי רגע וימאס׃ | 5 |
Thupi langa ladzala mphutsi ndi zipsera, khungu langa langʼambika ndipo likutuluka mafinya.
ימי קלו מני ארג ויכלו באפס תקוה׃ | 6 |
“Masiku anga ndi othamanga kupambana makina wolukira nsalu, ndipo amatha wopanda chiyembekezo.
זכר כי רוח חיי לא תשוב עיני לראות טוב׃ | 7 |
Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya; sindidzaonanso masiku achisangalalo.
לא תשורני עין ראי עיניך בי ואינני׃ | 8 |
Amene akundiona tsopano akundiona; mudzandifunafuna koma sindidzapezekanso.
כלה ענן וילך כן יורד שאול לא יעלה׃ (Sheol ) | 9 |
Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka, momwemonso munthu amene walowa mʼmanda sabwerera. (Sheol )
לא ישוב עוד לביתו ולא יכירנו עוד מקמו׃ | 10 |
Iye sadzabweranso ku nyumba kwake ndipo onse omudziwa adzamuyiwala.
גם אני לא אחשך פי אדברה בצר רוחי אשיחה במר נפשי׃ | 11 |
“Nʼchifukwa chake ine sindidzakhala chete; ndidzayankhula mopsinjika mtima, ndidzadandaula mowawidwa mtima.
הים אני אם תנין כי תשים עלי משמר׃ | 12 |
Kodi ine ndine nyanja kapena chirombo chamʼnyanja kuti inu mundiyikire alonda?
כי אמרתי תנחמני ערשי ישא בשיחי משכבי׃ | 13 |
Pamene ndikuganiza kuti ndidzapeza chitonthozo pa bedi panga ndipo pogona panga padzachepetsa madandawulo anga,
וחתתני בחלמות ומחזינות תבעתני׃ | 14 |
ngakhale nthawi imeneyo mumandiopseza ndi maloto ndi kundichititsa mantha ndi masomphenya,
ותבחר מחנק נפשי מות מעצמותי׃ | 15 |
kotero kuti ndimalakalaka kudzikhweza kapena kufa, kupambana kupirira zowawa zimene ndikuzimva mʼthupi mwanga.
מאסתי לא לעלם אחיה חדל ממני כי הבל ימי׃ | 16 |
Ine ndatopa nawo moyo wanga; sindingakonde kukhala moyo nthawi zonse. Ndisiyeni ndekha pakuti moyo wanga ulibe tanthauzo.
מה אנוש כי תגדלנו וכי תשית אליו לבך׃ | 17 |
“Kodi munthu nʼchiyani kuti muzimuganizira chotere, kuti muzisamala zochita zake,
ותפקדנו לבקרים לרגעים תבחננו׃ | 18 |
kuti muzimusanthula mmawa uliwonse ndi kumamuyesa nthawi yonse?
כמה לא תשעה ממני לא תרפני עד בלעי רקי׃ | 19 |
Kodi simudzaleka kumandizonda kuti ndipezeko mpata wopumula?
חטאתי מה אפעל לך נצר האדם למה שמתני למפגע לך ואהיה עלי למשא׃ | 20 |
Ngati ine ndachimwa, ndachita chiyani kwa Inu, Inu wopenyetsetsa anthu? Chifukwa chiyani mwachititsa kuti ndikhale ngati choponyera chandamale chanu? Kodi ndasanduka katundu wolemera kwa Inu?
ומה לא תשא פשעי ותעביר את עוני כי עתה לעפר אשכב ושחרתני ואינני׃ | 21 |
Chifukwa chiyani simukundikhululukira zolakwa zanga ndi kundichotsera machimo anga? Pakuti posachedwa ndilowa mʼmanda; mudzandifunafuna ine koma simudzandionanso.”