< איוב 5 >
קרא נא היש עונך ואל מי מקדשים תפנה׃ | 1 |
“Itana ngati ungathe, koma ndani adzakuyankhe? Kodi ndi kwa mngelo uti ungapezeko thandizo?
כי לאויל יהרג כעש ופתה תמית קנאה׃ | 2 |
Mkwiyo umapha chitsiru, ndipo njiru imawononga wopusa.
אני ראיתי אויל משריש ואקוב נוהו פתאם׃ | 3 |
Ine ndinaona chitsiru chitamera mizu, koma mwadzidzidzi nyumba yake inatembereredwa.
ירחקו בניו מישע וידכאו בשער ואין מציל׃ | 4 |
Ana ake alibe ndi chitetezo chomwe; amaponderezedwa mʼbwalo la milandu popanda owateteza.
אשר קצירו רעב יאכל ואל מצנים יקחהו ושאף צמים חילם׃ | 5 |
Anthu anjala amamudyera zokolola zake, amamutengera ndi za pa minga pomwe, ndipo anthu akhwinthi amafunkha chuma chake.
כי לא יצא מעפר און ומאדמה לא יצמח עמל׃ | 6 |
Pakuti masautso satuluka mʼfumbi, ndipo kuwukira sikuchokera mʼdothi.
כי אדם לעמל יולד ובני רשף יגביהו עוף׃ | 7 |
Komatu munthu amabadwira kuti azunzike monga momwe mbaliwali zimathethekera mlengalenga.
אולם אני אדרש אל אל ואל אלהים אשים דברתי׃ | 8 |
“Koma ndikanakhala ine, ndikanamudandawulira Mulungu; ndikanapereka mlandu wanga kwa Iye.
עשה גדלות ואין חקר נפלאות עד אין מספר׃ | 9 |
Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka, zodabwitsa zimene sizingatheke kuwerengedwa.
הנתן מטר על פני ארץ ושלח מים על פני חוצות׃ | 10 |
Iye amagwetsa mvula pa dziko lapansi, ndipo amathirira minda ya anthu.
לשום שפלים למרום וקדרים שגבו ישע׃ | 11 |
Iye amakweza anthu wamba, ndipo iwo amene akulira amawayika pa malo otetezedwa.
מפר מחשבות ערומים ולא תעשינה ידיהם תושיה׃ | 12 |
Iyeyo amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera, kotero kuti cholinga chawo sichipindula kanthu.
לכד חכמים בערמם ועצת נפתלים נמהרה׃ | 13 |
Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo, ndipo zolinga za atambwali amazithetsa msangamsanga.
יומם יפגשו חשך וכלילה ימששו בצהרים׃ | 14 |
Mdima umawagwera nthawi yamasana; nthawi yamasana amayenda moyambasayambasa monga nthawi ya usiku.
וישע מחרב מפיהם ומיד חזק אביון׃ | 15 |
Mulungu amapulumutsa amphawi ku lupanga la mʼkamwa mwawo; amawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amphamvu.
ותהי לדל תקוה ועלתה קפצה פיה׃ | 16 |
Choncho osauka ali ndi chiyembekezo, ndipo anthu opanda chilungamo amawatseka pakamwa.
הנה אשרי אנוש יוכחנו אלוה ומוסר שדי אל תמאס׃ | 17 |
“Wodala munthu amene Mulungu amamudzudzula; nʼchifukwa chake usanyoze chilango cha Wamphamvuzonse.
כי הוא יכאיב ויחבש ימחץ וידו תרפינה׃ | 18 |
Pakuti Iye amavulaza koma amamanganso mabalawo; Iye amakantha munthu, komanso manja ake amachiritsa.
בשש צרות יצילך ובשבע לא יגע בך רע׃ | 19 |
Pakuti adzakupulumutsa ku masautso nthawi ndi nthawi, mavuto angachuluke bwanji, sadzakukhudza ndi pangʼono pomwe.
ברעב פדך ממות ובמלחמה מידי חרב׃ | 20 |
Pa nthawi ya njala adzakulanditsa ku imfa, ndipo nthawi ya nkhondo adzakupulumutsa ku lupanga.
בשוט לשון תחבא ולא תירא משד כי יבוא׃ | 21 |
Adzakuteteza kwa anthu osinjirira, ndipo palibe chifukwa chochitira mantha pamene chiwonongeko chafika.
לשד ולכפן תשחק ומחית הארץ אל תירא׃ | 22 |
Uzidzaseka pa nthawi ya chiwonongeko ndi ya njala, ndipo palibe chifukwa chochitira mantha ndi zirombo za mʼdziko lapansi.
כי עם אבני השדה בריתך וחית השדה השלמה לך׃ | 23 |
Pakuti udzachita pangano ndi miyala ya mʼmunda mwako, ndipo nyama zakuthengo zidzakhala nawe mwamtendere.
וידעת כי שלום אהלך ופקדת נוך ולא תחטא׃ | 24 |
Udzadziwa kuti nyumba yako ndi malo otetezedwa; udzawerengera katundu wako ndipo sudzapeza kanthu kamene kasowapo.
וידעת כי רב זרעך וצאצאיך כעשב הארץ׃ | 25 |
Udzadziwa kuti ana ako adzakhala ambiri, ndipo zidzukulu zako zidzakhala ngati udzu wa mʼdziko lapansi.
תבוא בכלח אלי קבר כעלות גדיש בעתו׃ | 26 |
Udzafika ku manda utakalamba, monga mitolo ya zokolola pa nyengo yake.
הנה זאת חקרנוה כן היא שמענה ואתה דע לך׃ | 27 |
“Ife tafufuza zimenezi ndipo ndi zoona, choncho uzimvere ndi kuzitsata.”