< איוב 41 >

תמשך לויתן בחכה ובחבל תשקיע לשנו׃ 1
“Kodi ungathe kukoka ngʼona ndi mbedza ya nsomba kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe?
התשים אגמון באפו ובחוח תקוב לחיו׃ 2
Kodi ungathe kumanga chingwe mʼmphuno mwake, kapena kubowola nsagwada zake ndi mbedza?
הירבה אליך תחנונים אם ידבר אליך רכות׃ 3
Kodi ngʼonayo idzakupempha kuti uyichitire chifundo? Kodi idzakuyankhula ndi mawu ofatsa?
היכרת ברית עמך תקחנו לעבד עולם׃ 4
Kodi idzachita nawe mgwirizano kuti uyisandutse kapolo wako mpaka muyaya?
התשחק בו כצפור ותקשרנו לנערותיך׃ 5
Kodi udzasewera nayo ngati mbalame, kapena kuyimangirira kuti atsikana ako asewere nayo?
יכרו עליו חברים יחצוהו בין כנענים׃ 6
Kodi anthu adzayitsatsa malonda? Nanga amalondawo nʼkugawanagawana nyama yake kuti akagulitse?
התמלא בשכות עורו ובצלצל דגים ראשו׃ 7
Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi zisonga, kapena kubowola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba?
שים עליו כפך זכר מלחמה אל תוסף׃ 8
Ukayiputa udziwe kuti pali nkhondo, ndipo iweyo sudzabwereranso.
הן תחלתו נכזבה הגם אל מראיו יטל׃ 9
Chiyembekezo choti nʼkuyigonjetsa ndi chabodza; kungoyiona kokha, ndithu iwe kumangodzigwera wekha.
לא אכזר כי יעורנו ומי הוא לפני יתיצב׃ 10
Palibe wolimba mtima kuti ndi kuyiputa. Ndani angalimbe mtima kulimbana ndi Ine?
מי הקדימני ואשלם תחת כל השמים לי הוא׃ 11
Kodi ndani anandipatsa kanthu kuti ndimubwezere? Zonse za pansi pa thambo ndi zanga.
לא אחריש בדיו ודבר גבורות וחין ערכו׃ 12
“Sindidzaleka kuyankhula za ziwalo zake za chirombocho, za mphamvu zake ndiponso za maonekedwe a thupi lake.
מי גלה פני לבושו בכפל רסנו מי יבוא׃ 13
Ndani angasende chikopa chake? Ndani angayiyandikire kuti abowole chikopa chake cholimbacho?
דלתי פניו מי פתח סביבות שניו אימה׃ 14
Ndani angatsekule kukamwa kwake, pakamwa pamene pazunguliridwa ndi mano ochititsa mantha?
גאוה אפיקי מגנים סגור חותם צר׃ 15
Kumsana kwake kuli mizere ya mamba onga zishango zolumikizanalumikizana;
אחד באחד יגשו ורוח לא יבוא ביניהם׃ 16
Mambawo ndi olukanalukana kotero kuti mpweya sungathe kulowa pakati pake.
איש באחיהו ידבקו יתלכדו ולא יתפרדו׃ 17
Ndi olumikizanalumikizana; ndi omatirirana kwambiri kotero kuti sangathe kulekana.
עטישתיו תהל אור ועיניו כעפעפי שחר׃ 18
Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali; maso ake amawala ngati kuwala kwa mʼbandakucha.
מפיו לפידים יהלכו כידודי אש יתמלטו׃ 19
Mʼkamwa mwake mumatuluka nsakali zamoto ndipo mumathetheka mbaliwali zamoto.
מנחיריו יצא עשן כדוד נפוח ואגמן׃ 20
Mʼmphuno mwake mumatuluka utsi ngati wa mʼnkhali yowira yomwe ili pa moto wa bango.
נפשו גחלים תלהט ולהב מפיו יצא׃ 21
Mpweya wake umayatsa makala, ndipo malawi amoto amatuluka mʼkamwa mwake.
בצוארו ילין עז ולפניו תדוץ דאבה׃ 22
Mphamvu zake zili mʼkhosi mwake; aliyense wokumana nayo amangoti njenjenje ndi mantha.
מפלי בשרו דבקו יצוק עליו בל ימוט׃ 23
Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana ndipo ndi yokhwima kwambiri ndi yolimba.
לבו יצוק כמו אבן ויצוק כפלח תחתית׃ 24
Pachifuwa pake ndi powuma ngati mwala, ndi pa gwaa, ngati mwala wamphero.
משתו יגורו אלים משברים יתחטאו׃ 25
Ngʼonayo ikangovuwuka, ndi anthu amphamvu omwe amaopa; amabwerera mʼmbuyo, kuthawa.
משיגהו חרב בלי תקום חנית מסע ושריה׃ 26
Ngakhale ikanthidwe ndi lupanga, lupangalo silichita kanthu, ngakhale mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera.
יחשב לתבן ברזל לעץ רקבון נחושה׃ 27
Chitsulo imachiyesa ngati phesi chabe ndi mkuwa ngati chikuni chowola.
לא יבריחנו בן קשת לקש נהפכו לו אבני קלע׃ 28
Muvi sungathe kuyithawitsa, miyala imene ayilasa nayo imangoyinyenyanyenya.
כקש נחשבו תותח וישחק לרעש כידון׃ 29
Zibonga zimakhala ngati ziputu; imangoseka pamene akuyibaya ndi nthungo.
תחתיו חדודי חרש ירפד חרוץ עלי טיט׃ 30
Mamba a ku mimba kwake ali ngati chopunthira chakunthwa ndipo imasiya mkukuluzi mʼmatope ngati galeta lopunthira tirigu.
ירתיח כסיר מצולה ים ישים כמרקחה׃ 31
Imagadutsa madzi ozama ngati madzi a mʼnkhali, imachititsa nyanja kuti iwire ngati mbiya yoyengera mafuta.
אחריו יאיר נתיב יחשב תהום לשיבה׃ 32
Kumbuyo kwake imasiya nthubwitubwi zambee, kotero kuti munthu angaganize kuti nyanja yachita imvi.
אין על עפר משלו העשו לבלי חת׃ 33
Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho, nʼcholengedwa chopanda mantha.
את כל גבה יראה הוא מלך על כל בני שחץ׃ 34
Chimanyoza nyama zina zonse; icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.”

< איוב 41 >