< איוב 4 >

ויען אליפז התימני ויאמר׃ 1
Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
הנסה דבר אליך תלאה ועצר במלין מי יוכל׃ 2
“Ngati wina atakuyankha, kodi ungakhumudwe? Koma ndani angakhale chete wosayankhula?
הנה יסרת רבים וידים רפות תחזק׃ 3
Taganiza momwe iwe walangizira anthu ambiri, momwe walimbitsira anthu ofowoka.
כושל יקימון מליך וברכים כרעות תאמץ׃ 4
Mawu ako analimbitsa anthu ofuna kugwa; unachirikiza anthu wotha mphamvu.
כי עתה תבוא אליך ותלא תגע עדיך ותבהל׃ 5
Koma tsopano mavuto akufikira ndipo wataya mtima, zakukhudza ndipo uli ndi mantha.
הלא יראתך כסלתך תקותך ותם דרכיך׃ 6
Kodi kuopa Mulungu kwako sindiko kulimbika mtima kwako? Ndipo moyo wako wosalakwa ndiye chiyembekezo chako?
זכר נא מי הוא נקי אבד ואיפה ישרים נכחדו׃ 7
“Ganiza bwino tsopano: Kodi munthu wosalakwa anawonongekapo nʼkale lonse? Nʼkuti kumene munthu wolungama mtima anaphedwa?
כאשר ראיתי חרשי און וזרעי עמל יקצרהו׃ 8
Monga ndaonera ine, anthu amene amatipula zoyipa, ndi iwo amene amadzala mavuto, amakolola zomwezo.
מנשמת אלוה יאבדו ומרוח אפו יכלו׃ 9
Iwo amaphedwa ndi mpweya wa Mulungu; amawonongeka ndi mpweya waukali wa mkwiyo wake.
שאגת אריה וקול שחל ושני כפירים נתעו׃ 10
Mikango imabangula ndi kulira, komabe mano a mikango yamphamvu amathyoledwa.
ליש אבד מבלי טרף ובני לביא יתפרדו׃ 11
Mkango umafa chifukwa chosowa nyama, ndipo ana amkango amamwazikana.
ואלי דבר יגנב ותקח אזני שמץ מנהו׃ 12
“Mawu anabwera kwa ine mwamseri, makutu anga anamva kunongʼona kwake.
בשעפים מחזינות לילה בנפל תרדמה על אנשים׃ 13
Mʼkati mwa maloto ochititsa mantha usiku, nthawi imene anthu amagona tulo tofa nato,
פחד קראני ורעדה ורב עצמותי הפחיד׃ 14
ndinagwidwa ndi mantha, ndi kuyamba kunjenjemera ndipo mafupa anga onse anaweyeseka.
ורוח על פני יחלף תסמר שערת בשרי׃ 15
Pamenepo mzimu unadutsa pamaso panga, ndipo ubweya wa pa thupi langa unayima kuti njoo.
יעמד ולא אכיר מראהו תמונה לנגד עיני דממה וקול אשמע׃ 16
Chinthucho chinayimirira koma sindinathe kuzindikira kuti chinali chiyani. Chinthu chinayima patsogolo panga, kunali zii ndipo ndinamva mawu akuti,
האנוש מאלוה יצדק אם מעשהו יטהר גבר׃ 17
‘Kodi munthu angathe kukhala wolungama kupambana Mulungu? Kodi munthu angathe kukhala wangwiro kupambana Mlengi wake?
הן בעבדיו לא יאמין ובמלאכיו ישים תהלה׃ 18
Ngati Mulungu sakhulupirira atumiki ake omwe, ngati Iye amawapeza angelo ake ndi cholakwa,
אף שכני בתי חמר אשר בעפר יסודם ידכאום לפני עש׃ 19
nanga kuli bwanji ndi iwo amene amakhala mʼnyumba zadothi, amene maziko awo ndi fumbi, amene amathudzuka mosavuta ngati kadziwotche!
מבקר לערב יכתו מבלי משים לנצח יאבדו׃ 20
Mmawa ali moyo, pofika madzulo afa; mwakachetechete, amawonongeka kwamuyaya.
הלא נסע יתרם בם ימותו ולא בחכמה׃ 21
Kodi zonse zimene ali nazo sizimatheratu, kotero kuti amafa osadziwa nʼkanthu komwe?’

< איוב 4 >