< איוב 35 >
Ndipo Elihu anawonjeza kunena kuti,
הזאת חשבת למשפט אמרת צדקי מאל׃ | 2 |
“Kodi mukuganiza kuti mukukhoza? Mukunena kuti, ‘Ndine wolungama pamaso pa Mulungu.’
כי תאמר מה יסכן לך מה אעיל מחטאתי׃ | 3 |
Komanso inu mukufunsa kuti, ‘Kodi phindu langa nʼchiyani, ndipo ndimapeza chiyani ndikapanda kuchimwa?’
אני אשיבך מלין ואת רעיך עמך׃ | 4 |
“Ine ndikufuna ndikuyankheni inu pamodzi ndi abwenzi anu omwe.
הבט שמים וראה ושור שחקים גבהו ממך׃ | 5 |
Yangʼanani kumwamba ndipo muone mitambo imene ili kutali ndi inuyo.
אם חטאת מה תפעל בו ורבו פשעיך מה תעשה לו׃ | 6 |
Inuyo mukachimwa, Iye zimamukhudza motani? Ngati machimo anu ndi ochuluka, zimenezo zimachita chiyani kwa Iye?
אם צדקת מה תתן לו או מה מידך יקח׃ | 7 |
Ngati inu ndinu wolungama, mumamupatsa Iyeyo chiyani? Kapena Iye amalandira chiyani chochokera mʼdzanja lanu?
לאיש כמוך רשעך ולבן אדם צדקתך׃ | 8 |
Kuyipa kwanu kumangokhudza anthu ngati inuyo, ndipo chilungamo chanu chimakhudza anthu anzanu.
מרב עשוקים יזעיקו ישועו מזרוע רבים׃ | 9 |
“Anthu akufuwula chifukwa cha kuzunzidwa; akufuna chithandizo kuti achoke pansi pa ulamuliro wa anthu amphamvu.
ולא אמר איה אלוה עשי נתן זמרות בלילה׃ | 10 |
Koma palibe amene akunena kuti, ‘Kodi ali kuti Mulungu, Mlengi wanga, amene amatisangalatsa nthawi ya usiku,
מלפנו מבהמות ארץ ומעוף השמים יחכמנו׃ | 11 |
amene amatiphunzitsa kupambana nyama za dziko lapansi ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zowuluka?’
שם יצעקו ולא יענה מפני גאון רעים׃ | 12 |
Iye sayankha pamene anthu akufuwulira kwa Iye chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oyipa.
אך שוא לא ישמע אל ושדי לא ישורנה׃ | 13 |
Ndithu, Mulungu samva kupempha kwawo kopanda pake; Wamphamvuzonse sasamalira zimenezi.
אף כי תאמר לא תשורנו דין לפניו ותחולל לו׃ | 14 |
Ndipo ndi bodza lalikulu kunena kuti Iye saona zimene zikuchitika. Iye adzaweruza molungama ngati inu mutamudikira
ועתה כי אין פקד אפו ולא ידע בפש מאד׃ | 15 |
ndiye tsono popeza kuti ukali wake sukupereka chilango, zoyipa zambiri zimene anthu amachita,
ואיוב הבל יפצה פיהו בבלי דעת מלין יכבר׃ | 16 |
abambo Yobu mumangoyankhula zopandapake, mukungochulukitsa mawu opanda nzeru.”