< איוב 30 >

ועתה שחקו עלי צעירים ממני לימים אשר מאסתי אבותם לשית עם כלבי צאני׃ 1
“Koma tsopano akundinyoza, ana angʼonoangʼono kwa ine, anthu amene makolo awo sindikanawalola kuti azithandizana ndi agalu anga kuweta nkhosa zanga.
גם כח ידיהם למה לי עלימו אבד כלח׃ 2
Kodi mphamvu zawo ndi za phindu lanji kwa ine, pakuti mphamvu zawo zinatha kale?
בחסר ובכפן גלמוד הערקים ציה אמש שואה ומשאה׃ 3
Anali atatheratu kuwonda ndi njala, ankayendayenda mʼdziko lopanda madzi, mʼchipululu usiku.
הקטפים מלוח עלי שיח ושרש רתמים לחמם׃ 4
Ankathyola therere ndi masamba owawa, ndipo chakudya chawo chinali mizu ya mitengo ya masache.
מן גו יגרשו יריעו עלימו כגנב׃ 5
Anapirikitsidwa pakati pa anthu anzawo, akuwakuwiza ngati kuti anali akuba.
בערוץ נחלים לשכן חרי עפר וכפים׃ 6
Anawumirizidwa kukhala ku zigwembe za mitsinje yowuma, pakati pa matanthwe ndi mʼmaenje a mʼnthaka.
בין שיחים ינהקו תחת חרול יספחו׃ 7
Ankalira ngati nyama kuthengo ndipo ankawunjikana pamodzi pa ziyangoyango.
בני נבל גם בני בלי שם נכאו מן הארץ׃ 8
Anali anthu achabechabe ndi wopanda dzina, anathamangitsidwa mʼdziko.
ועתה נגינתם הייתי ואהי להם למלה׃ 9
“Ndipo tsopano ana awo akundiyimba nyimbo zachipongwe; ineyo ndasanduka chisudzo chawo.
תעבוני רחקו מני ומפני לא חשכו רק׃ 10
Iwo amanyansidwa nane ndipo amandithawa; akandiona salephera kundilavulira mʼmaso mwangamu.
כי יתרו פתח ויענני ורסן מפני שלחו׃ 11
Tsopano pakuti Mulungu wakhwefula uta wanga ndipo wandisautsa, iwowo analekeratu kundiopa.
על ימין פרחח יקומו רגלי שלחו ויסלו עלי ארחות אידם׃ 12
Ku dzanja langa lamanja anthu akulimbana nane; andikumbira dzenje loti ndigweremo ndikamayenda, andipangira mitumbira ya nkhondo kuti alimbane nane.
נתסו נתיבתי להותי יעילו לא עזר למו׃ 13
Iwo anditsekera njira; akufuna kundichititsa ngozi, popanda wina aliyense wowaletsa.
כפרץ רחב יאתיו תחת שאה התגלגלו׃ 14
Akundithamangitsa ngati madzi olowera pa mpanda wobowoka, iwo akubwererabwerera pakati pa chipasupasu.
ההפך עלי בלהות תרדף כרוח נדבתי וכעב עברה ישעתי׃ 15
Zoopsa zandithetsa mphamvu; ulemu wanga wachita ngati wauluzika ndi mphepo, chuma changa chija chazimirira ngati mtambo.
ועתה עלי תשתפך נפשי יאחזוני ימי עני׃ 16
“Ndipo tsopano mtima wanga wachokamo; ndili mʼmasiku amasautso.
לילה עצמי נקר מעלי וערקי לא ישכבון׃ 17
Mafupa anga akuphwanya usiku pakuti zowawa zanga sizikuleka.
ברב כח יתחפש לבושי כפי כתנתי יאזרני׃ 18
Mʼmphamvu zake Mulungu wakhala ngati chovala changa; Iye wandigwira ngati chovala chondithina pa khosi.
הרני לחמר ואתמשל כעפר ואפר׃ 19
Wandiponya mʼmatope, ndipo ndasanduka ngati fumbi ndi phulusa.
אשוע אליך ולא תענני עמדתי ותתבנן בי׃ 20
“Inu Mulungu, ine ndikulirira kwa Inu, koma simukundiyankha; ndikayimirira, Inu simundiyangʼana nʼkomwe.
תהפך לאכזר לי בעצם ידך תשטמני׃ 21
Inuyo mumandichitira zankhanza; mumandizunza ndi dzanja lanu lamphamvu.
תשאני אל רוח תרכיבני ותמגגני תשוה׃ 22
Mwandinyamulira ku mphepo ndipo mwandiwulutsa ndi mphepoyo; mwandiponya mʼmphepo ya mkuntho.
כי ידעתי מות תשיבני ובית מועד לכל חי׃ 23
Ndikudziwa kuti Inu mudzandifikitsa ku imfa, kumalo kumene amoyo onse adzapitako.
אך לא בעי ישלח יד אם בפידו להן שוע׃ 24
“Ndithudi palibe munthu amene amalanga munthu wosweka mtima, amene akupempha thandizo mʼmasautso ake.
אם לא בכיתי לקשה יום עגמה נפשי לאביון׃ 25
Kodi ine sindinalire nawo iwo amene anali pamavuto? Kodi mtima wanga sunamvere chisoni anthu osauka?
כי טוב קויתי ויבא רע ואיחלה לאור ויבא אפל׃ 26
Koma pamene ndinkayembekezera zabwino, zoyipa ndiye zinandigwera; pamene ndinkafunafuna kuwala, mdima ndiye unandigwera.
מעי רתחו ולא דמו קדמני ימי עני׃ 27
Kuwawa kwa mʼkati mwanga sikukuleka; ndili mʼmasiku amasautso.
קדר הלכתי בלא חמה קמתי בקהל אשוע׃ 28
Ndikuyenda wothimbirira, komatu osati ndi dzuwa; ndimayimirira pa msonkhano ndi kupempha chithandizo molira.
אח הייתי לתנים ורע לבנות יענה׃ 29
Ndasanduka mʼbale wa nkhandwe, mnzawo wa akadzidzi.
עורי שחר מעלי ועצמי חרה מני חרב׃ 30
Khungu langa layamba kuda ndipo likufunduka; thupi langa likutentha chifukwa cha kuphwanya kwa thupi.
ויהי לאבל כנרי ועגבי לקול בכים׃ 31
Pangwe wanga wasanduka woyimbira maliro, ndipo chitoliro changa chikuyimbira anthu olira.

< איוב 30 >