< איוב 3 >

אחרי כן פתח איוב את פיהו ויקלל את יומו׃ 1
Pambuyo pake Yobu anatsekula pakamwa pake nayamba kutemberera tsiku limene iyeyo anabadwa.
ויען איוב ויאמר׃ 2
Ndipo Yobu anati:
יאבד יום אולד בו והלילה אמר הרה גבר׃ 3
“Tsiku limene ine ndinabadwa litembereredwe ndi usiku umene ananena kuti, ‘Mwana wamwamuna wabadwa!’
היום ההוא יהי חשך אל ידרשהו אלוה ממעל ואל תופע עליו נהרה׃ 4
Tsiku limenelo lisanduke mdima; Mulungu wa kumwambako asalilabadirenso; kuwala kusaonekenso pa tsikulo.
יגאלהו חשך וצלמות תשכן עליו עננה יבעתהו כמרירי יום׃ 5
Mdima ndi mthunzi wa imfa zikhale pa tsiku limeneli; mtambo uphimbe tsikuli; mdima wandiweyani udetse kuwala kwake.
הלילה ההוא יקחהו אפל אל יחד בימי שנה במספר ירחים אל יבא׃ 6
Usiku umenewo ukutidwe ndi mdima wandiweyani; usawerengedwenso pamodzi ndi masiku a chaka, kapena kukhala pa mwezi wina uliwonse.
הנה הלילה ההוא יהי גלמוד אל תבא רננה בו׃ 7
Usiku umenewo usabweretse chilichonse chabwino; kusamvekenso nthungululu za chikondwerero.
יקבהו אררי יום העתידים ערר לויתן׃ 8
Odziwa kutemberera masiku alitemberere tsikulo, iwo amene akonzekera kuwutsa Leviyatani.
יחשכו כוכבי נשפו יקו לאור ואין ואל יראה בעפעפי שחר׃ 9
Nyenyezi zake za mʼbandakucha zikhale mdima; tsikulo liyembekezere kucha pachabe ndipo lisaonenso kuwala koyamba kwa mʼbandakucha.
כי לא סגר דלתי בטני ויסתר עמל מעיני׃ 10
Pakuti tsiku limenelo ndiye ndinatuluka mʼmimba ya amayi anga ndipo ndi limene linandionetsa zovuta.
למה לא מרחם אמות מבטן יצאתי ואגוע׃ 11
“Bwanji ine sindinawonongeke pamene ndinkabadwa ndi kufa pamene ndimatuluka mʼmimba?
מדוע קדמוני ברכים ומה שדים כי אינק׃ 12
Chifukwa chiyani panali mawondo wondilandirirapo ndi mawere woti andiyamwitsepo?
כי עתה שכבתי ואשקוט ישנתי אז ינוח לי׃ 13
Pakuti tsopano bwenzi ndili gone mwamtendere; ndikanakhala nditagona tulo ndili pa mpumulo
עם מלכים ויעצי ארץ הבנים חרבות למו׃ 14
pamodzi ndi mafumu ndi aphungu a dziko lapansi, amene anadzimangira nyumba zikuluzikulu zimene tsopano ndi mabwinja,
או עם שרים זהב להם הממלאים בתיהם כסף׃ 15
pamodzi ndi olamulira amene anali ndi golide, amene anadzaza nyumba zawo ndi siliva.
או כנפל טמון לא אהיה כעללים לא ראו אור׃ 16
Kapena, bwanji sindinakwiriridwe pansi monga mwana wobadwa wakufa kale, ngati khanda limene silinaone kuwala kwa dzuwa?
שם רשעים חדלו רגז ושם ינוחו יגיעי כח׃ 17
Ku mandako anthu oyipa sakhalanso pa mavuto, ndipo kumeneko anthu otopa ali pa mpumulo.
יחד אסירים שאננו לא שמעו קול נגש׃ 18
A mʼndende kumeneko akusangalala ndi mtendere; sakumvanso mawu ofuwula a kapitawo wa akapolo.
קטן וגדול שם הוא ועבד חפשי מאדניו׃ 19
Anthu wamba ndi anthu apamwamba ali kumeneko, ndipo kapolo ndi womasuka kwa mbuye wake.
למה יתן לעמל אור וחיים למרי נפש׃ 20
“Chifukwa chiyani dzuwa limawalira iwo amene ali pa mavuto, ndipo moyo umapatsidwa kwa owawidwa mtima,
המחכים למות ואיננו ויחפרהו ממטמונים׃ 21
kwa iwo amene amalakalaka imfa imene sibwera, amene amayifunafuna imfayo kupambana chuma chobisika,
השמחים אלי גיל ישישו כי ימצאו קבר׃ 22
amene amakondwa ndi kusangalala akamalowa mʼmanda?
לגבר אשר דרכו נסתרה ויסך אלוה בעדו׃ 23
Chifuwa chiyani moyo umaperekedwa kwa munthu amene njira yake yabisika, amene Mulungu wamuzinga ponseponse?
כי לפני לחמי אנחתי תבא ויתכו כמים שאגתי׃ 24
Mʼmalo moti ndidye, ndimalira, ndi kubuwula kwanga nʼkosalekeza.
כי פחד פחדתי ויאתיני ואשר יגרתי יבא לי׃ 25
Chimene ndinkachiopa chandigwera; chimene ndinkachita nacho mantha chandichitikira.
לא שלותי ולא שקטתי ולא נחתי ויבא רגז׃ 26
Ndilibe mtendere kapena bata, ndilibe mpumulo, koma mavuto okhaokha.”

< איוב 3 >