< איוב 22 >

ויען אליפז התמני ויאמר׃ 1
Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
הלאל יסכן גבר כי יסכן עלימו משכיל׃ 2
“Kodi munthu nʼkukhala waphindu kwa Mulungu? Kodi munthu wanzeru angamupindulire Iye?
החפץ לשדי כי תצדק ואם בצע כי תתם דרכיך׃ 3
Kodi Wamphamvuzonse akanapeza chabwino chotani iweyo ukanakhala wolungama? Kodi iyeyo akanapeza phindu lanji makhalidwe ako akanakhala angwiro?
המיראתך יכיחך יבוא עמך במשפט׃ 4
“Kodi nʼchifukwa choti umamuopa, kuti azikudzudzula, kuti azifuna kukukokera ku mlandu?
הלא רעתך רבה ואין קץ לעונתיך׃ 5
Kodi osati nʼchifukwa chakuti kuyipa kwako nʼkwakukulu? Kodi machimo ako si opanda malire?
כי תחבל אחיך חנם ובגדי ערומים תפשיט׃ 6
Iwe unkawumiriza abale ako kuti akupatse chikole popanda chifukwa; umalanda anthu zovala zawo ndi kuwasiya amaliseche.
לא מים עיף תשקה ומרעב תמנע לחם׃ 7
Sunawapatse madzi anthu otopa, ndipo unawamana chakudya anthu anjala,
ואיש זרוע לו הארץ ונשוא פנים ישב בה׃ 8
ngakhale unali munthu wamphamvu, wokhala ndi malo akeake, munthu waulemu wake, wokhala mʼdzikomo.
אלמנות שלחת ריקם וזרעות יתמים ידכא׃ 9
Ndipo akazi amasiye unawachotsa wopanda kanthu, ndipo unapondereza ana amasiye.
על כן סביבותיך פחים ויבהלך פחד פתאם׃ 10
Nʼchifukwa chake misampha yakuzungulira, nʼchifukwa chake tsoka ladzidzidzi lakuchititsa mantha,
או חשך לא תראה ושפעת מים תכסך׃ 11
nʼchifukwa chake kuli mdima kuti sungathe kuona kanthu, nʼchifukwa chakenso madzi achigumula akumiza.
הלא אלוה גבה שמים וראה ראש כוכבים כי רמו׃ 12
“Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba? Ndipo ona nyenyezi zili mmwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene zililipo!
ואמרת מה ידע אל הבעד ערפל ישפוט׃ 13
Komabe iweyo ukunena kuti, ‘Kodi Mulungu amadziwa chiyani? Kodi Iye amaweruza mu mdima woterewu?
עבים סתר לו ולא יראה וחוג שמים יתהלך׃ 14
Mitambo yakuda yamuphimba, kotero kuti Iye sakutiona pamene akuyendayenda pamwamba pa thambopo.’
הארח עולם תשמר אשר דרכו מתי און׃ 15
Kodi iwe udzayendabe mʼnjira yakale imene anthu oyipa ankayendamo?
אשר קמטו ולא עת נהר יוצק יסודם׃ 16
Iwo anachotsedwa nthawi yawo isanakwane, maziko awo anakokoloka ndi madzi achigumula.
האמרים לאל סור ממנו ומה יפעל שדי למו׃ 17
Anthuwo anati kwa Mulungu, ‘Tichokereni! Kodi Wamphamvuzonse angatichitire chiyani?’
והוא מלא בתיהם טוב ועצת רשעים רחקה מני׃ 18
Chonsecho ndi Iye amene anadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino, choncho ine sindigwirizana ndi uphungu wa anthu oyipa.
יראו צדיקים וישמחו ונקי ילעג למו׃ 19
“Anthu olungama amaona kuwonongeka kwawo ndipo amakondwera; anthu osalakwa amangoseka, akamuona woyipa akulangidwa.
אם לא נכחד קימנו ויתרם אכלה אש׃ 20
Amanena kuti, ‘Ndithudi adani athu awonongeka ndipo moto wawononga chuma chawo!’
הסכן נא עמו ושלם בהם תבואתך טובה׃ 21
“Gonjera Mulungu kuti ukhale naye pamtendere; ukatero udzaona zabwino.
קח נא מפיו תורה ושים אמריו בלבבך׃ 22
Landira malangizo a pakamwa pake ndipo usunge mawu ake mu mtima mwako.
אם תשוב עד שדי תבנה תרחיק עולה מאהלך׃ 23
Ukabwerera kwa Wamphamvuzonse udzabwezeretsedwa; ukachotsa zoyipa zonse zimene zimachitika mʼnyumba mwako,
ושית על עפר בצר ובצור נחלים אופיר׃ 24
ndipo chuma chamtengowapatali nuchiona ngati fumbi, golide wa ku Ofiri numutaya ku miyala ya ku zigwa.
והיה שדי בצריך וכסף תועפות לך׃ 25
Pamenepo Wamphamvuzonseyo adzakhala golide wako, siliva wako wamtengowapatali.
כי אז על שדי תתענג ותשא אל אלוה פניך׃ 26
Pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuzonse ndipo udzakweza nkhope yako kwa Mulungu.
תעתיר אליו וישמעך ונדריך תשלם׃ 27
Udzamupempha ndipo adzakumvera, ndipo udzapereka zimene unalonjeza.
ותגזר אומר ויקם לך ועל דרכיך נגה אור׃ 28
Chimene watsimikiza kuti uchite, chidzachitikadi, kuwala kudzakuwunikira pa njira yako.
כי השפילו ותאמר גוה ושח עינים יושע׃ 29
Pamene anthu agwetsedwa pansi, iwe nʼkunena kuti, ‘Akwezeni!’ Pamenepo Iye adzapulumutsa anthu oponderezedwa.
ימלט אי נקי ונמלט בבר כפיך׃ 30
Iye adzapulumutsa ngakhale munthu amene ndi wolakwa, ameneyo adzapulumutsidwa kudzera mʼkulungama kwako.”

< איוב 22 >