< איוב 20 >

ויען צפר הנעמתי ויאמר׃ 1
Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti
לכן שעפי ישיבוני ובעבור חושי בי׃ 2
“Kuvutika kwa mʼmaganizo kwanga kwandifulumiza kuti ndiyankhe chifukwa ndasautsidwa kwambiri.
מוסר כלמתי אשמע ורוח מבינתי יענני׃ 3
Ndikumva kudzudzula kondinyoza, ndipo kumvetsetsa kwanga kwa zinthu kwandifulumiza kuti ndiyankhe.
הזאת ידעת מני עד מני שים אדם עלי ארץ׃ 4
“Ndithudi iwe ukudziwa momwe zinthu zakhala zikuchitikira kuyambira kale, kuchoka nthawi imene munthu analengedwa pa dziko lapansi,
כי רננת רשעים מקרוב ושמחת חנף עדי רגע׃ 5
kuti chisangalalo cha woyipa nʼchosachedwa kutha, chimwemwe cha wosapembedza Mulungu nʼchakanthawi kochepa.
אם יעלה לשמים שיאו וראשו לעב יגיע׃ 6
Ngakhale atamayenda mapewa ake ali mmwamba ndipo mutu wake uli nengʼaa,
כגללו לנצח יאבד ראיו יאמרו איו׃ 7
iye adzatheratu monga momwe imatayikira ndowe yake yomwe; iwo amene ankamuona adzati, ‘Kodi uje uja ali kuti?’
כחלום יעוף ולא ימצאוהו וידד כחזיון לילה׃ 8
Adzazimirira ngati maloto ndipo sadzapezekanso, adzachotsedwa ngati masomphenya a usiku.
עין שזפתו ולא תוסיף ולא עוד תשורנו מקומו׃ 9
Diso limene linamuona silidzamuonanso; sadzapezekanso pamalo pake.
בניו ירצו דלים וידיו תשבנה אונו׃ 10
Ana ake adzabwezera zonse zimene iyeyo analanda anthu osauka;
עצמותיו מלאו עלומו ועמו על עפר תשכב׃ 11
Mphamvu zaunyamata zimene zili mʼthupi mwake zidzagona naye limodzi mʼfumbi.
אם תמתיק בפיו רעה יכחידנה תחת לשונו׃ 12
“Ngakhale zoyipa zili zozuna mʼkamwa mwake ndipo amazibisa kunsi kwa lilime lake,
יחמל עליה ולא יעזבנה וימנענה בתוך חכו׃ 13
ngakhale salola kuzilavula, ndipo amazisunga mʼkamwa mwake,
לחמו במעיו נהפך מרורת פתנים בקרבו׃ 14
koma chakudya chake chidzawawasa mʼmimba mwake; chidzasanduka ngati ndulu ya njoka mʼkati mwa iyeyo.
חיל בלע ויקאנו מבטנו יורשנו אל׃ 15
Adzachisanza chuma chimene anachimeza; Mulungu adzachitulutsa mʼmimba mwa munthuyo.
ראש פתנים יינק תהרגהו לשון אפעה׃ 16
Iye adzayamwa ndulu ya njoka ndipo ululu wa mphiri udzamupha.
אל ירא בפלגות נהרי נחלי דבש וחמאה׃ 17
Sadzasangalala ndi timitsinje, mitsinje yoyenda uchi ndi mafuta.
משיב יגע ולא יבלע כחיל תמורתו ולא יעלס׃ 18
Ayenera kubweza zimene anazigwirira ntchito osazidya; sadzasangalala ndi phindu la malonda ake.
כי רצץ עזב דלים בית גזל ולא יבנהו׃ 19
Pakuti iye anapondereza anthu osauka ndipo anawasiya wopanda thandizo; iyeyo analanda nyumba zimene sanamange.
כי לא ידע שלו בבטנו בחמודו לא ימלט׃ 20
“Chifukwa choti umbombo wake sutha, sadzatha kusunga chilichonse chimene amakondwera nacho.
אין שריד לאכלו על כן לא יחיל טובו׃ 21
Palibe chatsala kuti iye adye; chuma chake sichidzachedwa kutha.
במלאות שפקו יצר לו כל יד עמל תבואנו׃ 22
Ngakhale ndi munthu wachuma, mavuto adzamugwera; mavuto aakulu adzamugwera.
יהי למלא בטנו ישלח בו חרון אפו וימטר עלימו בלחומו׃ 23
Akadya nʼkukhuta, Mulungu adzamugwetsera ukali wamoto ngati mvula yosalekeza.
יברח מנשק ברזל תחלפהו קשת נחושה׃ 24
Ngakhale athawe mkondo wachitsulo, muvi wamkuwa wosongoka udzamulasa.
שלף ויצא מגוה וברק ממררתו יהלך עליו אמים׃ 25
Muviwo adzawutulutsira ku msana, songa yake yowala kuchoka mʼmphafa mwake. Adzagwidwa ndi mantha aakulu;
כל חשך טמון לצפוניו תאכלהו אש לא נפח ירע שריד באהלו׃ 26
mdima wandiweyani ukudikira chuma chake. Moto wopanda wowukoleza udzamupsereza ndi kuwononga zonse zotsala mʼnyumba yake.
יגלו שמים עונו וארץ מתקוממה לו׃ 27
Zamumlengalenga zidzawulula kulakwa kwake; dziko lapansi lidzamuwukira.
יגל יבול ביתו נגרות ביום אפו׃ 28
Chigumula cha madzi chidzawononga nyumba yake, katundu wake adzatengedwa pa tsiku la ukali wa Mulungu.
זה חלק אדם רשע מאלהים ונחלת אמרו מאל׃ 29
Izi ndi zimene Mulungu amasungira anthu oyipa, mphotho imene Mulungu amayikira iwowo.”

< איוב 20 >