< איוב 11 >

ויען צפר הנעמתי ויאמר׃ 1
Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti,
הרב דברים לא יענה ואם איש שפתים יצדק׃ 2
“Kodi mawu ambirimbiriwa nʼkukhala osayankhidwa? Kodi munthu woyankhulayankhulayu nʼkulungamitsidwa?
בדיך מתים יחרישו ותלעג ואין מכלם׃ 3
Kodi anthu nʼkukhala chete atamva kubwebweta kwakoku? Kodi palibe wina amene adzakudzudzule pamene ukuyankhula zonyoza?
ותאמר זך לקחי ובר הייתי בעיניך׃ 4
Iwe ukunena kwa Mulungu kuti, ‘Zikhulupiriro zanga ndi zopanda zolakwika ndipo ndine wangwiro pamaso panu.’
ואולם מי יתן אלוה דבר ויפתח שפתיו עמך׃ 5
Aa, nʼkanakonda Mulungu akanayankhula kuti Iye atsekule pakamwa pake kutsutsana nawe
ויגד לך תעלמות חכמה כי כפלים לתושיה ודע כי ישה לך אלוה מעונך׃ 6
ndi kukuwululira chinsinsi cha nzeru yake, pakuti nzeru yeniyeni ili ndi mbali ziwiri. Dziwa izi: Mulungu wayiwala machimo ako ena.
החקר אלוה תמצא אם עד תכלית שדי תמצא׃ 7
“Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu? Kodi ungafufuze malire a nzeru za Wamphamvuzonse?
גבהי שמים מה תפעל עמקה משאול מה תדע׃ (Sheol h7585) 8
Zili kutali kupambana mayiko akumwamba, nanga ungachite chiyani? Ndi zakuya kupambana kuya kwa manda, nanga ungadziwe chiyani? (Sheol h7585)
ארכה מארץ מדה ורחבה מני ים׃ 9
Muyeso wa nzeru zake ndi wautali kupambana dziko lapansi ndipo ndi wopingasa kupambana nyanja.
אם יחלף ויסגיר ויקהיל ומי ישיבנו׃ 10
“Ngati Iye atabwera ndi kukutsekera mʼndende nakutengera ku bwalo la milandu, ndani angathe kumuletsa?
כי הוא ידע מתי שוא וירא און ולא יתבונן׃ 11
Ndithudi, Mulungu amazindikira anthu achinyengo; akaona choyipa, kodi sachizindikira?
ואיש נבוב ילבב ועיר פרא אדם יולד׃ 12
Munthu wopanda nzeru sizingatheke kukhala wanzeru monganso mwana wa bulu wakuthengo sangasanduke munthu.
אם אתה הכינות לבך ופרשת אליו כפך׃ 13
“Koma ngati upereka mtima wako kwa Iye ndi kutambasulira manja ako kwa Iyeyo,
אם און בידך הרחיקהו ואל תשכן באהליך עולה׃ 14
ngati utaya tchimo limene lili mʼdzanja lako ndi kusalola choyipa kuti chikhale mʼmoyo mwako,
כי אז תשא פניך ממום והיית מצק ולא תירא׃ 15
udzatukula mutu wako wosachita manyazi; udzayima chilili ndipo sudzachita mantha.
כי אתה עמל תשכח כמים עברו תזכר׃ 16
Udzayiwala ndithu zowawa zako, zidzakhala ngati madzi amene apita kale.
ומצהרים יקום חלד תעפה כבקר תהיה׃ 17
Moyo wako udzawala kupambana usana, ndipo mdima udzakhala ngati mmawa.
ובטחת כי יש תקוה וחפרת לבטח תשכב׃ 18
Udzalimba mtima popeza pali chiyembekezo; ndipo udzayangʼana mbali zonse ndi kugona mosatekeseka.
ורבצת ואין מחריד וחלו פניך רבים׃ 19
Udzagona pansi, popanda wina wokuopseza ndipo ambiri adzakupempha kuti uwachitire chifundo.
ועיני רשעים תכלינה ומנוס אבד מנהם ותקותם מפח נפש׃ 20
Koma anthu oyipa adzafuna thandizo osalipeza, ndipo adzasowa njira yothawirapo; chiyembekezo chawo chidzakhala imfa basi.”

< איוב 11 >