< ירמיה 46 >

אשר היה דבר יהוה אל ירמיהו הנביא על הגוים׃ 1
Yehova anamupatsa Yeremiya uthenga wonena za anthu a mitundu ina.
למצרים על חיל פרעה נכו מלך מצרים אשר היה על נהר פרת בכרכמש אשר הכה נבוכדראצר מלך בבל בשנת הרביעית ליהויקים בן יאשיהו מלך יהודה׃ 2
Kunena za Igupto: Yehova ananena za gulu lankhondo la Farao Neko mfumu ya ku Igupto limene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni analigonjetsa ku Karikemesi ku mtsinje wa Yufurate mʼchaka cha chinayi cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda,
ערכו מגן וצנה וגשו למלחמה׃ 3
anati, “Konzani zishango zanu ndi malihawo, ndipo yambanipo kupita ku nkhondo!
אסרו הסוסים ועלו הפרשים והתיצבו בכובעים מרקו הרמחים לבשו הסרינת׃ 4
Mangani akavalo, ndipo kwerani inu okwerapo! Khalani pa mzere mutavala zipewa! Nolani mikondo yanu, valani malaya anu ankhondo!
מדוע ראיתי המה חתים נסגים אחור וגבוריהם יכתו ומנוס נסו ולא הפנו מגור מסביב נאם יהוה׃ 5
Yeremiya anati: Kodi ndikuona chiyani? Achita mantha akubwerera, ankhondo awo agonjetsedwa. Akuthawa mofulumirapo osayangʼananso mʼmbuyo, ndipo agwidwa ndi mantha ponseponse,” akutero Yehova.
אל ינוס הקל ואל ימלט הגבור צפונה על יד נהר פרת כשלו ונפלו׃ 6
Waliwiro sangathe kuthawa ngakhale wankhondo wamphamvu sangathe kupulumuka. Akunka napunthwa ndi kugwa kumpoto kwa mtsinje wa Yufurate.
מי זה כיאר יעלה כנהרות יתגעשו מימיו׃ 7
“Kodi ndani amene akukwera ngati Nailo, ngati mtsinje wa madzi amkokomo?
מצרים כיאר יעלה וכנהרות יתגעשו מים ויאמר אעלה אכסה ארץ אבידה עיר וישבי בה׃ 8
Igupto akusefukira ngati Nailo, ngati mitsinje ya madzi amkokomo. Iye akunena kuti, ‘Ndidzadzuka ndi kuphimba dziko lapansi; ndidzawononga mizinda ndi anthu ake.’
עלו הסוסים והתהללו הרכב ויצאו הגבורים כוש ופוט תפשי מגן ולודים תפשי דרכי קשת׃ 9
Tiyeni, inu akavalo! Thamangani inu magaleta! Tulukani, inu ankhondo, ankhondo a ku Kusi ndi Puti amene mumanyamula zishango, ankhondo a ku Ludi amene mumaponya uta.
והיום ההוא לאדני יהוה צבאות יום נקמה להנקם מצריו ואכלה חרב ושבעה ורותה מדמם כי זבח לאדני יהוה צבאות בארץ צפון אל נהר פרת׃ 10
Koma tsikulo ndi la Ambuye Yehova Wamphamvuzonse; tsiku lolipsira, lolipsira adani ake. Lupanga lake lidzawononga ndi kukhuta magazi, lidzaledzera ndi magazi. Pakuti Yehova, Yehova Wamphamvuzonse, adzapereka adani ake ngati nsembe mʼdziko la kumpoto mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.
עלי גלעד וקחי צרי בתולת בת מצרים לשוא הרביתי רפאות תעלה אין לך׃ 11
“Pita ku Giliyadi ukatenge mankhwala iwe namwali Igupto. Wayesayesa mankhwala ambiri koma osachira; palibe mankhwala okuchiritsa.
שמעו גוים קלונך וצוחתך מלאה הארץ כי גבור בגבור כשלו יחדיו נפלו שניהם׃ 12
Anthu a mitundu ina amva za manyazi ako; kulira kwako kwadzaza dziko lapansi. Ankhondo akunka nagwetsanagwetsana, onse awiri agwa pansi limodzi.”
הדבר אשר דבר יהוה אל ירמיהו הנביא לבוא נבוכדראצר מלך בבל להכות את ארץ מצרים׃ 13
Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za kubwera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kudzathira nkhondo Igupto ndi uwu:
הגידו במצרים והשמיעו במגדול והשמיעו בנף ובתחפנחס אמרו התיצב והכן לך כי אכלה חרב סביביך׃ 14
“Mulengeze ku Igupto. Mulengeze ku Migidoli. Mulengezenso ku Mefisi ndi ku Tapanesi. Muwawuze anthu akumeneko kuti, ‘Imani pamalo panu ndi kukhala okonzeka kudziteteza, chifukwa lupanga lidzawononga zonse zimene muli nazo.’
מדוע נסחף אביריך לא עמד כי יהוה הדפו׃ 15
Chifukwa chiyani mulungu wanu wamphamvu uja Apisi wathawa? Iye sakanatha kulimba chifukwa Yehova anamugwetsa.
הרבה כושל גם נפל איש אל רעהו ויאמרו קומה ונשבה אל עמנו ואל ארץ מולדתנו מפני חרב היונה׃ 16
Ankhondo anu apunthwa ndi kugwa. Aliyense akuwuza mnzake kuti, ‘Tiyeni tibwerere kwathu, ku dziko kumene tinabadwira, tithawe lupanga la adani athu.’
קראו שם פרעה מלך מצרים שאון העביר המועד׃ 17
Kumeneku iwo adzafuwula kuti, ‘Farao, mfumu ya ku Igupto mupatseni dzina lakuti, Waphokoso, Wotaya mwayi wake.’
חי אני נאם המלך יהוה צבאות שמו כי כתבור בהרים וככרמל בים יבוא׃ 18
“Pali Ine wamoyo,” ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse, “wina adzabwera amene ali ngati Tabori phiri lopambana mapiri ena, ngati phiri la Karimeli loti njoo mʼmbali mwa nyanja.
כלי גולה עשי לך יושבת בת מצרים כי נף לשמה תהיה ונצתה מאין יושב׃ 19
Konzani katundu wanu wopita naye ku ukapolo inu anthu a ku Igupto, pakuti Mefisi adzasanduka chipululu ndipo adzakhala bwinja mopanda wokhalamo.
עגלה יפה פיה מצרים קרץ מצפון בא בא׃ 20
“Igupto ali ngati mwana wangʼombe wokongola, koma chimphanga chikubwera kuchokera kumpoto kudzalimbana naye.
גם שכריה בקרבה כעגלי מרבק כי גם המה הפנו נסו יחדיו לא עמדו כי יום אידם בא עליהם עת פקדתם׃ 21
Ngakhale ankhondo aganyu amene ali naye ali ngati ana angʼombe onenepa. Nawonso abwerera mʼmbuyo, nathawa pamodzi. Palibe amene wachirimika. Ndithu, tsiku la tsoka lawafikira; ndiyo nthawi yowalanga.
קולה כנחש ילך כי בחיל ילכו ובקרדמות באו לה כחטבי עצים׃ 22
Aigupto akuthawa ndi liwu lawo lili ngati la njoka yothawa pamene adani abwera ndi zida zawo, abwera ndi nkhwangwa ngati anthu odula mitengo.
כרתו יערה נאם יהוה כי לא יחקר כי רבו מארבה ואין להם מספר׃ 23
Iwo adzadula nkhalango ya Igupto,” akutero Yehova, “ngakhale kuti ndi yowirira. Anthuwo ndi ochuluka kupambana dzombe, moti sangatheke kuwerengeka.
הבישה בת מצרים נתנה ביד עם צפון׃ 24
Anthu a ku Igupto achita manyazi atengedwa ukapolo ndi anthu a kumpoto.”
אמר יהוה צבאות אלהי ישראל הנני פוקד אל אמון מנא ועל פרעה ועל מצרים ועל אלהיה ועל מלכיה ועל פרעה ועל הבטחים בו׃ 25
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, “Ndili pafupi kulanga Amoni mulungu wa Tebesi. Ndidzalanganso Farao ndi Igupto pamodzi ndi milungu yake yonse, mafumu ake ndi onse amene amamukhulupirira.
ונתתים ביד מבקשי נפשם וביד נבוכדראצר מלך בבל וביד עבדיו ואחרי כן תשכן כימי קדם נאם יהוה׃ 26
Ndidzawapereka kwa amene akufuna kuwapha, ndiye kuti kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi atsogoleri ake ankhondo. Komabe, mʼtsogolomo Igupto adzakhalanso ndi anthu monga kale,” akutero Yehova.
ואתה אל תירא עבדי יעקב ואל תחת ישראל כי הנני מושעך מרחוק ואת זרעך מארץ שבים ושב יעקוב ושקט ושאנן ואין מחריד׃ 27
“Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha; usataye mtima, iwe Israeli. Ndithu Ine ndidzakupulumutsa kuchokera ku mayiko akutali, ndidzapulumutsanso zidzukulu zako kuchokera ku mayiko kumene anapita nazo ku ukapolo. Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala motakasuka ndi pa mtendere, ndipo palibenso wina amene adzamuopsa.
אתה אל תירא עבדי יעקב נאם יהוה כי אתך אני כי אעשה כלה בכל הגוים אשר הדחתיך שמה ואתך לא אעשה כלה ויסרתיך למשפט ונקה לא אנקך׃ 28
Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe,” akutero Yehova. “Ndidzawonongeratu mitundu yonse ya anthu a ku mayiko kumene ndakupirikitsira, Koma iwe sindidzakuwononga kotheratu. Ndidzakulanga iwe ndithu koma moyenerera; sindidzakulekerera osakulanga.”

< ירמיה 46 >