< ירמיה 36 >
ויהי בשנה הרביעת ליהויקים בן יאשיהו מלך יהודה היה הדבר הזה אל ירמיהו מאת יהוה לאמר׃ | 1 |
Chaka chachinayi cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti,
קח לך מגלת ספר וכתבת אליה את כל הדברים אשר דברתי אליך על ישראל ועל יהודה ועל כל הגוים מיום דברתי אליך מימי יאשיהו ועד היום הזה׃ | 2 |
“Tenga buku ndipo ulembemo mawu onse amene ndayankhula nawe otsutsa Israeli, Yuda ndi mitundu yonse ya anthu, kuyambira nthawi imene ndinayamba kuyankhula nawe pa nthawi ya ulamuliro wa Yosiya mpaka lero lino.
אולי ישמעו בית יהודה את כל הרעה אשר אנכי חשב לעשות להם למען ישובו איש מדרכו הרעה וסלחתי לעונם ולחטאתם׃ | 3 |
Mwina mwake anthu a ku Yuda adzamva za zoopsa zonse zimene ndakonza kuti ndiwachitire, ndipo munthu aliyense adzatembenuka ndi kusiya ntchito zake zoyipa. Motero ndidzawakhululukira zoyipa zawo ndi machimo awo.”
ויקרא ירמיהו את ברוך בן נריה ויכתב ברוך מפי ירמיהו את כל דברי יהוה אשר דבר אליו על מגלת ספר׃ | 4 |
Tsono Yeremiya anayitana Baruki mwana wa Neriya. Baruki analemba mʼbuku mawu onse amene Yeremiya ankamuwuza, mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya.
ויצוה ירמיהו את ברוך לאמר אני עצור לא אוכל לבוא בית יהוה׃ | 5 |
Kenaka Yeremiya anawuza Baruki kuti, “Ine andiletsa kupita ku Nyumba ya Mulungu.
ובאת אתה וקראת במגלה אשר כתבת מפי את דברי יהוה באזני העם בית יהוה ביום צום וגם באזני כל יהודה הבאים מעריהם תקראם׃ | 6 |
Tsono iwe upite ku Nyumba ya Yehova pa tsiku losala kudya ndipo ukawerenge mawu a Yehova ochokera mʼbukumu amene ndinakulembetsa anthu onse akumva. Ukawawerengere anthu onse a ku Yuda amene amabwera ku Nyumba ya Mulungu kuchokera ku mizinda yawo.
אולי תפל תחנתם לפני יהוה וישבו איש מדרכו הרעה כי גדול האף והחמה אשר דבר יהוה אל העם הזה׃ | 7 |
Mwina mwake adzapempha kwa Yehova ndipo aliyense adzatembenuka ndi kusiya makhalidwe ake oyipa pakuti mkwiyo ndi ukali wa Yehova pa anthu awa ndi woopsa kwambiri.”
ויעש ברוך בן נריה ככל אשר צוהו ירמיהו הנביא לקרא בספר דברי יהוה בית יהוה׃ | 8 |
Baruki mwana wa Neriya anachita zonse zimene mneneri Yeremiya anamuwuza kuti achite. Mʼnyumba ya Yehova, iye anawerenga mawu a Yehova ochokera mʼbukulo.
ויהי בשנה החמשית ליהויקים בן יאשיהו מלך יהודה בחדש התשעי קראו צום לפני יהוה כל העם בירושלם וכל העם הבאים מערי יהודה בירושלם׃ | 9 |
Pa mwezi wachisanu ndi chinayi wa chaka chachisanu cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, anthu onse a mu Yerusalemu ndi onse amene anabwera kumeneko kuchokera ku mizinda ya Yuda, anapangana za kusala kudya kuti apepese Yehova.
ויקרא ברוך בספר את דברי ירמיהו בית יהוה בלשכת גמריהו בן שפן הספר בחצר העליון פתח שער בית יהוה החדש באזני כל העם׃ | 10 |
Atayima pa chipinda cha Gemariya mwana wa mlembi Safani, chimene chinali mʼbwalo lapamwamba, pafupi ndi Chipata Chatsopano cholowera ku Nyumba ya Yehova, Baruki anawerenga mawu onse a Yeremiya amene anali mʼbuku muja kwa anthu onse amene anali ku Nyumba ya Yehova.
וישמע מכיהו בן גמריהו בן שפן את כל דברי יהוה מעל הספר׃ | 11 |
Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani, atamva mawu onse a Yehova ochokera mʼbukumo,
וירד בית המלך על לשכת הספר והנה שם כל השרים יושבים אלישמע הספר ודליהו בן שמעיהו ואלנתן בן עכבור וגמריהו בן שפן וצדקיהו בן חנניהו וכל השרים׃ | 12 |
anapita ku nyumba ya mfumu nakalowa ku chipinda cha mlembi. Akuluakulu, mlembi Elisama, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani mwana wa Akibori, Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya pamodzi ndi akuluakulu ena onse, anali atasonkhana kumeneko.
ויגד להם מכיהו את כל הדברים אשר שמע בקרא ברוך בספר באזני העם׃ | 13 |
Tsono Mikaya anawafotokozera mawu onse amene anamva pamene Baruki ankawerenga buku lija anthu onse akumva.
וישלחו כל השרים אל ברוך את יהודי בן נתניהו בן שלמיהו בן כושי לאמר המגלה אשר קראת בה באזני העם קחנה בידך ולך ויקח ברוך בן נריהו את המגלה בידו ויבא אליהם׃ | 14 |
Pambuyo pake akuluakulu onsewo anatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki kukamuwuza kuti, “Bwera ndi buku limene unawerenga kwa anthu.” Ndipo Baruki mwana wa Neriya anapita nalo bukulo kwa anthuwo.
ויאמרו אליו שב נא וקראנה באזנינו ויקרא ברוך באזניהם׃ | 15 |
Iwo anati, “Khala pansi, ndipo tiwerengere bukuli.” Ndipo Baruki anawawerengera.
ויהי כשמעם את כל הדברים פחדו איש אל רעהו ויאמרו אל ברוך הגיד נגיד למלך את כל הדברים האלה׃ | 16 |
Atamva mawu onsewo, anayangʼanana mwa mantha ndipo anamuwuza Baruki kuti, “Ndithudi tikafotokozera mfumu mawu onsewa.”
ואת ברוך שאלו לאמר הגד נא לנו איך כתבת את כל הדברים האלה מפיו׃ | 17 |
Tsono anamufunsa Baruki kuti, “Tatiwuze, unalemba bwanji mawu onsewa? Kodi ndi Yeremiya anakulembetsa zimenezi?”
ויאמר להם ברוך מפיו יקרא אלי את כל הדברים האלה ואני כתב על הספר בדיו׃ | 18 |
Baruki anayankha kuti, “Inde, ndi Yeremiya amene anandiwuza mawu onsewa, ndipo ine ndinawalemba ndi utoto mʼbukumu.”
ויאמרו השרים אל ברוך לך הסתר אתה וירמיהו ואיש אל ידע איפה אתם׃ | 19 |
Kenaka akuluakuluwo anamuwuza Baruki kuti, “Iweyo ndi Yeremiya, pitani mukabisale. Munthu aliyense asadziwe kumene muli.”
ויבאו אל המלך חצרה ואת המגלה הפקדו בלשכת אלישמע הספר ויגידו באזני המלך את כל הדברים׃ | 20 |
Atayika bukulo mʼchipinda cha mlembi Elisama, analowa mʼbwalo, napita kwa mfumu ndi kukayifotokozera zonse.
וישלח המלך את יהודי לקחת את המגלה ויקחה מלשכת אלישמע הספר ויקראה יהודי באזני המלך ובאזני כל השרים העמדים מעל המלך׃ | 21 |
Itamva zimenezi mfumu inatuma Yehudi kuti akatenge bukulo, ndipo Yehudi anakalitenga ku chipinda cha mlembi Elisama ndipo anawerengera mfumu pamodzi ndi akuluakulu ake amene anali naye.
והמלך יושב בית החרף בחדש התשיעי ואת האח לפניו מבערת׃ | 22 |
Unali mwezi wachisanu ndi chinayi ndipo mfumu inali mʼnyumba ya pa nyengo yozizira, ikuwotha moto umene anasonkha.
ויהי כקרוא יהודי שלש דלתות וארבעה יקרעה בתער הספר והשלך אל האש אשר אל האח עד תם כל המגלה על האש אשר על האח׃ | 23 |
Yehudi ankati akawerenga masamba atatu kapena anayi a bukulo, mfumu inkawangʼamba ndi mpeni ndi kuwaponya pa moto ndipo anapitiriza kuchita zimenezi mpaka buku lonse linapsa.
ולא פחדו ולא קרעו את בגדיהם המלך וכל עבדיו השמעים את כל הדברים האלה׃ | 24 |
Mfumu pamodzi ndi omutumikira ake onse amene anamva mawu onsewa sanachite mantha kapena kungʼamba zovala zawo.
וגם אלנתן ודליהו וגמריהו הפגעו במלך לבלתי שרף את המגלה ולא שמע אליהם׃ | 25 |
Ngakhale kuti Elinatani, Delaya, ndi Gemariya anapempha mfumu kuti isatenthe bukulo, mfumuyo sinawamvere.
ויצוה המלך את ירחמאל בן המלך ואת שריהו בן עזריאל ואת שלמיהו בן עבדאל לקחת את ברוך הספר ואת ירמיהו הנביא ויסתרם יהוה׃ | 26 |
Mʼmalo mwake, mfumu inalamula Yerahimeeli mwana wake, Seraya mwana wa Azirieli ndi Selemiya mwana wa Abideeli kuti agwire mlembi Baruki ndi mneneri Yeremiya. Koma pamenepo nʼkuti Yehova atawabisa.
ויהי דבר יהוה אל ירמיהו אחרי שרף המלך את המגלה ואת הדברים אשר כתב ברוך מפי ירמיהו לאמר׃ | 27 |
Mfumu itatentha buku limene linali ndi mawu amene Yeremiya anamulembetsa Baruki, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti,
שוב קח לך מגלה אחרת וכתב עליה את כל הדברים הראשנים אשר היו על המגלה הראשנה אשר שרף יהויקים מלך יהודה׃ | 28 |
“Tenganso buku lina ndipo ulembe mawu onse amene anali mʼbuku loyamba lija, limene Yehoyakimu analitentha.
ועל יהויקים מלך יהודה תאמר כה אמר יהוה אתה שרפת את המגלה הזאת לאמר מדוע כתבת עליה לאמר בא יבוא מלך בבל והשחית את הארץ הזאת והשבית ממנה אדם ובהמה׃ | 29 |
Ndiponso akamuwuze Yehoyakimu mfumu ya Yuda kuti, ‘Yehova akuti: Iwe unatentha buku lija ndipo unati: Nʼchifukwa chiyani unalemba kuti mfumu ya ku Babuloni idzabwera ndithu kudzawononga dziko lino ndi kupha anthu pamodzi ndi nyama zomwe?’
לכן כה אמר יהוה על יהויקים מלך יהודה לא יהיה לו יושב על כסא דוד ונבלתו תהיה משלכת לחרב ביום ולקרח בלילה׃ | 30 |
Nʼchifukwa chake kunena za Yehoyakimu mfumu ya Yuda Yehova akuti sipadzaoneka munthu wina wolowa mʼmalo mwake pa mpando wa Davide. Akadzafa mtembo wake udzaponyedwa kunja ndipo udzakhala pa dzuwa masana, ndi pachisanu chowundana usiku.
ופקדתי עליו ועל זרעו ועל עבדיו את עונם והבאתי עליהם ועל ישבי ירושלם ואל איש יהודה את כל הרעה אשר דברתי אליהם ולא שמעו׃ | 31 |
Ndidzamulanga pamodzi ndi ana ake ndiponso omutumikira ake chifukwa cha zoyipa zawo; ndidzagwetsa pa iwo ndi pa onse amene akukhala mu Yerusalemu ndiponso pa anthu a ku Yuda masautso onse amene ndinawanena, chifukwa sanamvere.”
וירמיהו לקח מגלה אחרת ויתנה אל ברוך בן נריהו הספר ויכתב עליה מפי ירמיהו את כל דברי הספר אשר שרף יהויקים מלך יהודה באש ועוד נוסף עליהם דברים רבים כהמה׃ | 32 |
Choncho Yeremiya anatenga buku lina napatsa mlembi Baruki mwana wa Neriya, ndipo Yeremiya anamulembetsa mawu onse amene anali mʼbuku limene Yehoyakimu mfumu ya Yuda anatentha. Ndipo anawonjezerapo mawu ambiri monga omwewo.