< ירמיה 21 >

הדבר אשר היה אל ירמיהו מאת יהוה בשלח אליו המלך צדקיהו את פשחור בן מלכיה ואת צפניה בן מעשיה הכהן לאמר׃ 1
Mfumu Zedekiya inatuma Pasuri mwana wa Malikiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa Yeremiya.
דרש נא בעדנו את יהוה כי נבוכדראצר מלך בבל נלחם עלינו אולי יעשה יהוה אותנו ככל נפלאתיו ויעלה מעלינו׃ 2
Iwo amati akanene kwa Yeremiya mawu akuti, “Tinenere kwa Yehova chifukwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni akutithira nkhondo. Mwina mwake Yehova nʼkutichitira zodabwitsa kuti Nebukadinezarayo achoke kwathu kuno.”
ויאמר ירמיהו אליהם כה תאמרן אל צדקיהו׃ 3
Koma Yehova anawuza Yeremiya kuti ayankhe Pasuri ndi Zefaniya kuti, “Kamuwuzeni Zedekiya kuti,
כה אמר יהוה אלהי ישראל הנני מסב את כלי המלחמה אשר בידכם אשר אתם נלחמים בם את מלך בבל ואת הכשדים הצרים עליכם מחוץ לחומה ואספתי אותם אל תוך העיר הזאת׃ 4
‘Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ndikulandeni zida zimene zili mʼmanja mwanu zimene mukugwiritsa ntchito polimbana ndi mfumu ya ku Babuloni ndi ankhondo ake amene akuzingani kunja kwa lingali. Ndipo ndidzasonkhanitsa zidazo mʼkati mwa mzindawu.
ונלחמתי אני אתכם ביד נטויה ובזרוע חזקה ובאף ובחמה ובקצף גדול׃ 5
Ineyo mwini wakene ndi mkono wotambasula ndi dzanja lamphamvu, ndidzachita nanu nkhondo ndili wokwiya, wokalipa ndi waukali.
והכיתי את יושבי העיר הזאת ואת האדם ואת הבהמה בדבר גדול ימתו׃ 6
Ndidzakantha amene amakhala mu mzinda muno, anthu pamodzi ndi zirombo, ndipo zidzafa ndi mliri woopsa.
ואחרי כן נאם יהוה אתן את צדקיהו מלך יהודה ואת עבדיו ואת העם ואת הנשארים בעיר הזאת מן הדבר מן החרב ומן הרעב ביד נבוכדראצר מלך בבל וביד איביהם וביד מבקשי נפשם והכם לפי חרב לא יחוס עליהם ולא יחמל ולא ירחם׃ 7
Pambuyo pake, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi anthu a mu mzinda muno amene adzapulumuke pa nthawi ya mliri, lupanga ndi njala kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi kwa adani awo amene ankafuna kuwapha. Iye adzawapha ndi lupanga. Sadzawachitira chifundo kapena kuwamvera chisoni kapenanso kuwakomera mtima.’
ואל העם הזה תאמר כה אמר יהוה הנני נתן לפניכם את דרך החיים ואת דרך המות׃ 8
“Yehova anati ndiwawuzenso anthu amenewa kuti asankhe pakati pa moyo ndi imfa.
הישב בעיר הזאת ימות בחרב וברעב ובדבר והיוצא ונפל על הכשדים הצרים עליכם יחיה והיתה לו נפשו לשלל׃ 9
Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzaphedwa ndi lupanga, njala kapena mliri. Koma aliyense amene apite kukadzipereka kwa Ababuloni amene akuzinganiwa adzakhala ndi moyo, adzapulumuka.
כי שמתי פני בעיר הזאת לרעה ולא לטובה נאם יהוה ביד מלך בבל תנתן ושרפה באש׃ 10
Ine ndatsimikiza kuchitira mzinda uno choyipa osati chabwino, akutero Yehova. Udzaperekedwa mʼdzanja la mfumu ya ku Babuloni, ndipo iyeyo adzawutentha ndi moto.
ולבית מלך יהודה שמעו דבר יהוה׃ 11
“Komanso, uwuze banja laufumu la Yuda kuti, ‘Imva mawu a Yehova;
בית דוד כה אמר יהוה דינו לבקר משפט והצילו גזול מיד עושק פן תצא כאש חמתי ובערה ואין מכבה מפני רע מעלליהם׃ 12
inu a mʼbanja la Davide, Yehova akuti, “‘Weruzani mwachilungamo mmawa uliwonse; pulumutsani mʼdzanja la wozunza aliyense amene walandidwa katundu wake, kuopa kuti ukali wanga ungabuke ndi kuyaka ngati moto wosazimitsika chifukwa cha zoyipa zimene mwachita.
הנני אליך ישבת העמק צור המישר נאם יהוה האמרים מי יחת עלינו ומי יבוא במעונותינו׃ 13
Ndidzalimbana nanu, inu amene mukukhala pamwamba pa chigwa, inu okhala ngati thanthwe lapachidikha, akutero Yehova. Inu amene mumanena kuti, ‘Ndani amene angabwere kudzalimbana nafe? Ndani amene angathe kulowa mʼmalinga mwathu?’
ופקדתי עליכם כפרי מעלליכם נאם יהוה והצתי אש ביערה ואכלה כל סביביה׃ 14
Ndidzakulangani molingana ndi ntchito zanu, akutero Yehova. Ndidzatentha nkhalango zanu; moto udzapsereza zonse zimene zakuzungulirani.’”

< ירמיה 21 >