< ישעה 65 >
נדרשתי ללוא שאלו נמצאתי ללא בקשני אמרתי הנני הנני אל גוי לא קרא בשמי׃ | 1 |
“Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a amene sankandipempha kanthu; ndipo ndinalola kuti anthu amene ankandifunafuna kuti andipeze. Kwa mtundu wa anthu umene sunkapempha chithandizo kwa Ine, ndinati, ‘Ine ndili pano, Ine ndili pano.’
פרשתי ידי כל היום אל עם סורר ההלכים הדרך לא טוב אחר מחשבתיהם׃ | 2 |
Tsiku lonse ndatambasulira manja anga anthu owukira aja, amene amachita zoyipa, natsatira zokhumba zawo.
העם המכעיסים אותי על פני תמיד זבחים בגנות ומקטרים על הלבנים׃ | 3 |
Ndatambasulira manja anga anthu aja amene nthawi zonse amandikwiyitsa mopanda manyazi. Iwo amapereka nsembe mʼminda ndi kufukiza lubani pa maguwa ansembe a njerwa.
הישבים בקברים ובנצורים ילינו האכלים בשר החזיר ופרק פגלים כליהם׃ | 4 |
Amakatandala ku manda ndipo amakachezera usiku wonse kumalo obisika. Amadya nyama ya nkhumba, ndipo mʼmiphika mwawo muli msunzi wa nyama yodetsedwa.
האמרים קרב אליך אל תגש בי כי קדשתיך אלה עשן באפי אש יקדת כל היום׃ | 5 |
Amawuza ena kuti, ‘Khala patali usandiyandikire, chifukwa ungatengere kupatulika kwanga!’ Ukali wanga pa anthu otere uli ngati utsi mphuno zanga, ngati moto umene umayaka tsiku lonse.
הנה כתובה לפני לא אחשה כי אם שלמתי ושלמתי על חיקם׃ | 6 |
“Taonani, ndatsimikiza kale mlandu ndi chilango chawo; sindidzakhala chete koma ndidzawalanga kwathunthu chifukwa cha machimo awo
עונתיכם ועונת אבותיכם יחדו אמר יהוה אשר קטרו על ההרים ועל הגבעות חרפוני ומדתי פעלתם ראשנה על חיקם׃ | 7 |
ndi a makolo awo,” akutero Yehova. “Chifukwa anapereka nsembe zopsereza pa mapiri ndi kundinyoza Ine pa zitunda zawo, Ine ndidzawalanga kwathunthu potsata zimene anachita kale.”
כה אמר יהוה כאשר ימצא התירוש באשכול ואמר אל תשחיתהו כי ברכה בו כן אעשה למען עבדי לבלתי השחית הכל׃ | 8 |
Yehova akuti, “Pamene madzi akanapezeka mu phava la mphesa ndipo anthu amati, ‘Musawononge phavalo, popeza madzi ena abwino akanalimobe mʼphavalo,’ Inenso chifukwa cha mtumiki wanga; sindidzawononga onse.
והוצאתי מיעקב זרע ומיהודה יורש הרי וירשוה בחירי ועבדי ישכנו שמה׃ | 9 |
Ndidzatulutsa zidzukulu mʼbanja la Yakobo, ndipo a banja la Yuda adzalandira mapiri anga ngati cholowa chawo. Anthu anga osankhidwa adzalandira zimenezi, ndipo atumiki anga adzakhala kumeneko.
והיה השרון לנוה צאן ועמק עכור לרבץ בקר לעמי אשר דרשוני׃ | 10 |
Chigwa cha Saroni chidzakhala kodyetserako nkhosa, ndipo chigwa cha Akori chidzakhala malo opumirako ngʼombe kwa anthu anga ondifunafuna Ine.
ואתם עזבי יהוה השכחים את הר קדשי הערכים לגד שלחן והממלאים למני ממסך׃ | 11 |
“Koma inu amene mumasiya Yehova ndi kuyiwala phiri langa lopatulika, amene munamukonzera Gadi chakudya ndi kuthirira Meni chakumwa,
ומניתי אתכם לחרב וכלכם לטבח תכרעו יען קראתי ולא עניתם דברתי ולא שמעתם ותעשו הרע בעיני ובאשר לא חפצתי בחרתם׃ | 12 |
ndidzakuperekani ku lupanga ngati nsembe, ndipo nonse mudzaphedwa; chifukwa simunayankhe pamene ndinakuyitanani, ndinayankhula koma simunamvere. Munachita zoyipa pamaso panga ndipo munasankha kuchita zoyipa zomwe sindikondwera nazo.”
לכן כה אמר אדני יהוה הנה עבדי יאכלו ואתם תרעבו הנה עבדי ישתו ואתם תצמאו הנה עבדי ישמחו ואתם תבשו׃ | 13 |
Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, “Atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; atumiki anga adzakondwa, koma inu mudzakhala ndi manyazi.
הנה עבדי ירנו מטוב לב ואתם תצעקו מכאב לב ומשבר רוח תילילו׃ | 14 |
Atumiki anga adzayimba mosangalala, koma inu mudzalira kwambiri chifukwa chovutika mu mtima ndipo mudzalira mofuwula chifukwa mudzamva kuwawa mu mtima.
והנחתם שמכם לשבועה לבחירי והמיתך אדני יהוה ולעבדיו יקרא שם אחר׃ | 15 |
Anthu anga osankhidwa adzatchula dzina lanu potemberera. Ambuye Yehova adzakuphani, koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina.
אשר המתברך בארץ יתברך באלהי אמן והנשבע בארץ ישבע באלהי אמן כי נשכחו הצרות הראשנות וכי נסתרו מעיני׃ | 16 |
Aliyense wopempha dalitso mʼdzikomo adzachita zimenezo kwa Mulungu woona; ndipo aliyense wochita malumbiro mʼdzikomo adzalumbira mwa Mulungu woona. Pakuti mavuto akale adzayiwalika ndipo adzachotsedwa pamaso panga.
כי הנני בורא שמים חדשים וארץ חדשה ולא תזכרנה הראשנות ולא תעלינה על לב׃ | 17 |
“Taonani, ndikulenga mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukika, zidzayiwalika kotheratu.
כי אם שישו וגילו עדי עד אשר אני בורא כי הנני בורא את ירושלם גילה ועמה משוש׃ | 18 |
Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya chifukwa cha zimene ndikulenga, pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsa ndipo anthu ake adzakhala achimwemwe.
וגלתי בירושלם וששתי בעמי ולא ישמע בה עוד קול בכי וקול זעקה׃ | 19 |
Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemu ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga. Kumeneko sikudzamvekanso kulira ndi mfuwu wodandaula.
לא יהיה משם עוד עול ימים וזקן אשר לא ימלא את ימיו כי הנער בן מאה שנה ימות והחוטא בן מאה שנה יקלל׃ | 20 |
“Ana sadzafa ali akhanda ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse. Wamngʼono mwa iwo adzafa ali ndi zaka 100. Amene adzalephere kufika zaka 100 adzatengedwa kukhala wotembereredwa.
ובנו בתים וישבו ונטעו כרמים ואכלו פרים׃ | 21 |
Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo, adzadzala mpesa ndipo adzadya zipatso zake.
לא יבנו ואחר ישב לא יטעו ואחר יאכל כי כימי העץ ימי עמי ומעשה ידיהם יבלו בחירי׃ | 22 |
Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo, kapena kudzala ndi ena nʼkudya. Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyo wautali ngati mitengo. Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchito ya manja awo nthawi yayitali.
לא ייגעו לריק ולא ילדו לבהלה כי זרע ברוכי יהוה המה וצאצאיהם אתם׃ | 23 |
Sadzagwira ntchito pachabe kapena kubereka ana kuti aone tsoka; chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Yehova, iwowo pamodzi ndi adzukulu awo omwe.
והיה טרם יקראו ואני אענה עוד הם מדברים ואני אשמע׃ | 24 |
Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe. Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale.
זאב וטלה ירעו כאחד ואריה כבקר יאכל תבן ונחש עפר לחמו לא ירעו ולא ישחיתו בכל הר קדשי אמר יהוה׃ | 25 |
Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi. Mkango udzadya udzu monga ngʼombe, koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka. Pa phiri langa lopatulika sipadzakhala chinthu chopweteka kapena chowononga,” akutero Yehova.