< ישעה 63 >
מי זה בא מאדום חמוץ בגדים מבצרה זה הדור בלבושו צעה ברב כחו אני מדבר בצדקה רב להושיע׃ | 1 |
Kodi ndani uyo akubwera kuchokera ku Edomu, atavala zovala za ku Bozira za madontho ofiira? Kodi uyu ndani, amene wavala zovala zokongola, akuyenda mwa mphamvu zake? “Ndi Ineyo, woyankhula zachilungamo ndiponso wamphamvu zopulumutsa.”
מדוע אדם ללבושך ובגדיך כדרך בגת׃ | 2 |
Nanga bwanji zovala zanu zili psuu, ngati za munthu wofinya mphesa?
פורה דרכתי לבדי ומעמים אין איש אתי ואדרכם באפי וארמסם בחמתי ויז נצחם על בגדי וכל מלבושי אגאלתי׃ | 3 |
“Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa, palibe ndi mmodzi yemwe anali nane. Ndinawapondereza ndili wokwiya ndipo ndinawapondereza ndili ndi ukali; magazi awo anadothera pa zovala zanga, ndipo zovala zanga zonse zinathimbirira.
כי יום נקם בלבי ושנת גאולי באה׃ | 4 |
Pakuti ndinatsimikiza mu mtima mwanga kuti lafika tsiku lolipsira anthu anga; ndipo chaka cha kuwomboledwa kwanga chafika.
ואביט ואין עזר ואשתומם ואין סומך ותושע לי זרעי וחמתי היא סמכתני׃ | 5 |
Ndinayangʼana ndipo panalibe munthu wondithandiza. Ndinadabwa kwambiri kuti panalibe wondichirikiza; choncho ndinapambana ndi mphamvu zanga, ndipo mkwiyo wanga unandilimbitsa.
ואבוס עמים באפי ואשכרם בחמתי ואוריד לארץ נצחם׃ | 6 |
Ndinapondereza mitundu ya anthu ndili wokwiya; ndipo ndinawasakaza ndipo ndinathira magazi awo pansi.”
חסדי יהוה אזכיר תהלת יהוה כעל כל אשר גמלנו יהוה ורב טוב לבית ישראל אשר גמלם כרחמיו וכרב חסדיו׃ | 7 |
Ndidzafotokoza za kukoma mtima kwa Yehova, ntchito zimene Iye ayenera kutamandidwa. Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha zonse zimene watichitira. Inde, mwa chifundo ndi kukoma mtima kwake Yehova wachitira nyumba ya Israeli zinthu zabwino zambiri.
ויאמר אך עמי המה בנים לא ישקרו ויהי להם למושיע׃ | 8 |
Yehova anati, “Ndithu awa ndi anthu anga, ana anga amene sadzandinyenga Ine.” Choncho anawapulumutsa.
בכל צרתם לא צר ומלאך פניו הושיעם באהבתו ובחמלתו הוא גאלם וינטלם וינשאם כל ימי עולם׃ | 9 |
Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse, ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa. Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa, anawanyamula ndikuwatenga kuyambira kale lomwe.
והמה מרו ועצבו את רוח קדשו ויהפך להם לאויב הוא נלחם בם׃ | 10 |
Komabe iwo anawukira ndi kumvetsa chisoni Mzimu Woyera. Motero Yehova anatembenuka nakhala mdani wawo ndipo Iye mwini anamenyana nawo.
ויזכר ימי עולם משה עמו איה המעלם מים את רעי צאנו איה השם בקרבו את רוח קדשו׃ | 11 |
Pamenepo anthu ake anakumbukira masiku amakedzana, masiku a Mose mtumiki wake; ndipo anafunsa kuti, “Ali kuti Yehova amene anawawolotsa pa nyanja, pamodzi ndi Mose mʼbusa wawo? Ali kuti Iye amene anayika Mzimu Woyera pakati pawo?
מוליך לימין משה זרוע תפארתו בוקע מים מפניהם לעשות לו שם עולם׃ | 12 |
Ali kuti amene anachita zinthu zodabwitsa ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose? Ali kuti amene anagawa madzi pa nyanja anthu ake akuona, kuti dzina lake limveke mpaka muyaya,
מוליכם בתהמות כסוס במדבר לא יכשלו׃ | 13 |
amene anawayendetsa pa nyanja yozama? Monga kavalo woyendayenda mʼchipululu, iwo sanapunthwe;
כבהמה בבקעה תרד רוח יהוה תניחנו כן נהגת עמך לעשות לך שם תפארת׃ | 14 |
Mzimu Woyera unawapumulitsa ngati mmene ngʼombe zimapumulira. Umu ndi mmene Inu munatsogolera anthu anu kuti dzina lanu lilemekezeke.”
הבט משמים וראה מזבל קדשך ותפארתך איה קנאתך וגבורתך המון מעיך ורחמיך אלי התאפקו׃ | 15 |
Inu Yehova amene muli kumwambako, pa mpando wanu wolemekezeka, wopatulika ndi waulemerero, tiyangʼaneni ife. Kodi changu chanu ndi mphamvu zanu zili kuti? Simukutionetsanso kukoma mtima kwanu ndi chifundo chanu.
כי אתה אבינו כי אברהם לא ידענו וישראל לא יכירנו אתה יהוה אבינו גאלנו מעולם שמך׃ | 16 |
Koma Inu ndinu Atate athu, ngakhale Abrahamu satidziwa kapena Israeli kutivomereza ife; Inu Yehova, ndinu Atate athu, kuyambira kale dzina lanu ndinu Mpulumutsi wathu.
למה תתענו יהוה מדרכיך תקשיח לבנו מיראתך שוב למען עבדיך שבטי נחלתך׃ | 17 |
Chifukwa chiyani, Inu Yehova, mukutisocheretsa pa njira zanu? Bwanji mukutilola kuti tikhale owuma mitima kotero kuti sitikukuopaninso? Bwererani chifukwa cha atumiki anu; mafuko a anthu amene ali cholowa chanu.
למצער ירשו עם קדשך צרינו בוססו מקדשך׃ | 18 |
Anthu anu atangokhala pa malo anu opatulika pa kanthawi kochepa, adani athu anasakaza malo anu opatulika.
היינו מעולם לא משלת בם לא נקרא שמך עליהם׃ | 19 |
Ife tili ngati anthu amene simunawalamulirepo ngati iwo amene sanakhalepo anthu anu.