< ישעה 58 >

קרא בגרון אל תחשך כשופר הרם קולך והגד לעמי פשעם ולבית יעקב חטאתם׃ 1
“Fuwula kwambiri, usaleke. Mawu ako amveke ngati lipenga. Uwawuze anthu anga za kulakwa kwawo; uwuze nyumba ya Yakobo za machimo awo.
ואותי יום יום ידרשון ודעת דרכי יחפצון כגוי אשר צדקה עשה ומשפט אלהיו לא עזב ישאלוני משפטי צדק קרבת אלהים יחפצון׃ 2
Pakuti tsiku ndi tsiku amafunafuna Ine; amaoneka ngati a chidwi chofuna kudziwa zimene ndimafuna, kukhala ngati kuti ndi dziko limene limachita zolondola ndipo silinasiye zolamulira za Mulungu wake. Amandipempha kuti ndigamule mlandu wawo mwachilungamo ndipo amaonetsa chidwi chofuna kukhala pafupi ndi Mulungu.
למה צמנו ולא ראית ענינו נפשנו ולא תדע הן ביום צמכם תמצאו חפץ וכל עצביכם תנגשו׃ 3
Anthu akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani ife tasala kudya pamene Inu simukulabadirapo? Kodi ife tavutikiranji nʼkudzichepetsa pamene Inu simunasamalepo?’” Yehova akuti, “Komatu tsiku lanu losala kudya, mumachita zinthu zokukondweretsani, ndipo mumazunza antchito anu onse.
הן לריב ומצה תצומו ולהכות באגרף רשע לא תצומו כיום להשמיע במרום קולכם׃ 4
Mumati uku mukusala kudya, uku mukukangana ndi kumenyana, mpaka kumenyana ndi nkhonya zopweteka. Kusala kudya mukuchitiramu musayembekezere kuti mawu anu amveka kumwamba.
הכזה יהיה צום אבחרהו יום ענות אדם נפשו הלכף כאגמן ראשו ושק ואפר יציע הלזה תקרא צום ויום רצון ליהוה׃ 5
Kodi kusala kudya kumene ndimakufuna Ine nʼkumeneku, kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi? Kodi ndi tsiku loti munthu angowerama pansi ngati bango ndi kumayala ziguduli nʼkuthirapo phulusa nʼkugonapo? Kodi ndiye mumati kusala kudya kumeneko, tsiku lokondweretsa Yehova?
הלוא זה צום אבחרהו פתח חרצבות רשע התר אגדות מוטה ושלח רצוצים חפשים וכל מוטה תנתקו׃ 6
“Kodi si uku kusala kudya kumene Ine ndimakufuna: Kumasula maunyolo ozunzizira anthu ndi kumasula zingwe za goli, kupereka ufulu kwa oponderezedwa ndi kuphwanya goli lililonse?
הלוא פרס לרעב לחמך ועניים מרודים תביא בית כי תראה ערם וכסיתו ומבשרך לא תתעלם׃ 7
Anthu anjala kodi mwawagawira chakudya chanu? Osowa ndi ongoyendayenda, kodi mwawapatsa malo ogona? Munthu wausiwa kodi mwamupatsa chovala?
אז יבקע כשחר אורך וארכתך מהרה תצמח והלך לפניך צדקך כבוד יהוה יאספך׃ 8
Mukatero chipulumutso chanu chidzabwera ngati mʼbandakucha, ndipo mabala anu adzachira msangamsanga; chilungamo chanu chidzakutsogolerani ndipo ulemerero wa Yehova udzakhala chokutchinjirizani kumbuyo kwanu.
אז תקרא ויהוה יענה תשוע ויאמר הנני אם תסיר מתוכך מוטה שלח אצבע ודבר און׃ 9
Mukamadzapemphera Yehova adzakuyankhani; mukadzapempha thandizo, Iye adzati: Ine ndili pano. “Ngati muleka kuzunza anzanu, ngati musiya kuloza chala ndiponso kunena zoyipa za anzanu.
ותפק לרעב נפשך ונפש נענה תשביע וזרח בחשך אורך ואפלתך כצהרים׃ 10
Ndipo ngati mudyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu oponderezedwa, pamenepo kuwala kwanu kudzaonekera mu mdima, ndipo usiku wanu udzakhala ngati usana.
ונחך יהוה תמיד והשביע בצחצחות נפשך ועצמתיך יחליץ והיית כגן רוה וכמוצא מים אשר לא יכזבו מימיו׃ 11
Yehova adzakutsogolerani nthawi zonse; adzakwaniritsa zosowa zanu mʼdziko longʼalukangʼaluka dzuwa ndipo adzalimbitsa matupi anu. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe amene madzi ake saphwa.
ובנו ממך חרבות עולם מוסדי דור ודור תקומם וקרא לך גדר פרץ משבב נתיבות לשבת׃ 12
Anthu ako adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthawi yayitali, ndipo adzamanganso pa maziko akalekale; inu mudzatchedwa okonza makoma opasuka. Anthu okonza misewu ndi nyumba zake.
אם תשיב משבת רגלך עשות חפציך ביום קדשי וקראת לשבת ענג לקדוש יהוה מכבד וכבדתו מעשות דרכיך ממצוא חפצך ודבר דבר׃ 13
“Muzisunga osaphwanya Sabata; musamachite zimene mukufuna pa masiku anga opatulika, tsiku la Sabata lizikhala tsiku lachisangalalo. Tsiku lopatulika la Yehova muzililemekeza posayenda mʼnjira zanu, kapena kuchita zimene mukufuna ndi kuyankhula zopandapake,
אז תתענג על יהוה והרכבתיך על במותי ארץ והאכלתיך נחלת יעקב אביך כי פי יהוה דבר׃ 14
mukatero mudzapeza chimwemwe mwa Yehova, ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi. Mudzadyerera dziko limene ndinapatsa Yakobo kholo lanu.” Yehova wayankhula ndi pakamwa pake.

< ישעה 58 >